Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
ndi kuŵapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Mulungu amene sanama, adalonjeza moyo wosathawu nthaŵi isanayambe.
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
Mvetsetsani, ndikuuzeni chinsinsi. Sikuti tonse tidzamwalira, komabe tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.
Tsopano chimene chikundidikira ndi mphotho ya chilungamo imene Mulungu wandisungira. Ambuye amene ali Woweruza wolungama, ndiwo amene adzandipatsa mphothoyo pa tsiku la chiweruzo. Tsonotu sadzangopatsa ine ndekha ai, komanso ena onse amene mwachikondi akudikira kuti Ambuyewo adzabwerenso.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse.
Padzakhala mfuu wa mau a mngelo wamkulu ndi wa lipenga la Mulungu. Ndipo pamenepo Ambuye mwini adzatsika kuchokera Kumwamba. Anthu amene adafa akukhulupirira Khristu, adzayamba ndiwo kuuka. Pambuyo pake ife amoyofe, otsalafe, tidzatengedwa pamodzi nawo m'mitambo kuti tikakumane ndi Ambuye mu mlengalenga. Motero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Sikudzakhalanso usiku, ndipo sipadzafunikanso kuŵala kwa nyale kapena kuŵala kwa dzuŵa, pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuŵala kwake, ndipo iwo adzakhala mafumu olamulira mpaka muyaya.
Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”
Tsono thupi lotha kuwolali likadzasanduka losatha kuwola, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzachitikadi zimene Malembo adanena kuti, “Imfa yagonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”
Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuŵalezera mtima onse amene adzamkhulupirire kuti alandire moyo wosatha.
Koma potsata lonjezo la Mulungu, tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, m'mene chilungamo chizidzakhalamo.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.
Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.”
Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.
Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziŵa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.
Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.
Komabe musakondwere chifukwa choti mizimu yoipa ikukugonjerani, koma muzikondwera kuti maina anu adalembedwa Kumwamba.”
Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Zidzateronso pamene akufa adzauka. Thupi loikidwa m'nthaka ngati mbeu yofesa, limaola, koma likadzauka, lidzakhala losaola. Thupi loikidwa m'manda, ndi lonyozeka ndi lofooka, koma likadzauka lidzakhala lokongola ndi lamphamvu. Thupi loikidwa m'manda, ndi lamnofu chabe, koma likadzauka, lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi lamnofu, palinso thupi lauzimu.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.”
Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo.
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m'kuwoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Khristuyo adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Ngodala anthu amene adzauke nao pa kuuka koyamba kumeneku. Ameneŵa ndiwo akeake a Mulungu. Imfa yachiŵiri ilibe mphamvu pa iwo, koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Yesu Khristu, ndipo azidzalamulira pamodzi naye zaka chikwi chimodzi.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Koma aliyense wodzamwa madzi amene Ine ndidzampatse, sadzamvanso ludzu konse mpaka muyaya. Madzi amene ndidzampatsewo azidzatumphukira mwa iye ngati kasupe wa madzi opatsa moyo, nkumupatsa moyo wosatha.”
Moyowo udaoneka, ndipo ife tidauwona. Tikuuchitira umboni, ndipo tikukulalikirani za moyo wosatha, umene unali kwa Atate ndipo udatiwonekera.
Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka.
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Mzimu Woyera ndi Mkwati wamkazi akuti, “Bwerani!” Aliyense womva mauŵa, anenenso kuti, “Bwerani!” Aliyense womva ludzu, abwere. Aliyense woŵafuna, aŵalandire mwaulere madzi opatsa moyo.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Ndithu tikulimba mtima, ndipo makamaka tikadakonda kutuluka m'thupi lathu lino ndi kukakhala kwa Ambuye.
Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Anthu anu amene adafa adzakhalanso ndi moyo, matupi ao adzauka. Inu nonse amene muli m'manda, dzukani ndi kuimba mosangalala. Monga momwe mame amafeŵetsera pansi kutsitsimutsa zomera, momwemonso Chauta adzaukitsa anthu amene adafa kale.
Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Tsonotu si zolengedwa zokhazi zikubuula ai. Koma ngakhale ifenso amene tili ndi mphatso zoyamba za Mzimu Woyera, tikubuula mu mtima, podikira kuti Mulungu atilandire ngati ana ake, ndi kupulumutsa matupi athu omwe.
Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda.
Pambuyo pake ndidamva mau ochokera Kumwamba. Adati, “Lemba kuti, Ngodala anthu akufa amene kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno afa ali otumikira Ambuye.” Mzimu Woyera akuti, “Inde, ngodaladi. Akapumule ntchito zao zolemetsa, pakuti ntchito zaozo zimaŵatsata.”
Ndiponso iwe, mnzanga weniweni pa ntchito yathuyi, bwanji uŵathandize azimaiŵa. Paja ameneŵa pofalitsa Uthenga Wabwino akhala akugwira ntchito kolimba pamodzi ndi ine ndi Klemensi ndi antchito anzanga ena onse, amene maina ao ngolembedwa m'buku la amoyo.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.
Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya.
Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.
Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Simoni Petro adati “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake.
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.
“Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.
Iwo adzakhala ngati angelo, mwakuti sangafenso ai. Iwo ndi ana a Mulungu popeza kuti Iye adaŵaukitsa kwa akufa.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Amene mudaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa. Chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pankhope pao. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chisangalalo. Chisoni ndi kubuula zidzatha.
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
“Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha.
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Musadabwe nazo zimenezi, pakuti ikudza nthaŵi pamene anthu onse amene ali m'manda adzamva mau ake nadzatuluka. Anthu amene adachita zabwino, adzauka kuti akhale ndi moyo, koma amene adachita zoipa, adzauka kuti azengedwe mlandu.”
“Sipadzafikanso dzuŵa loti likuŵalire masana, kapena mwezi wokuŵalira usiku. Koma Ine Chauta ndiye ndidzakuŵalire mpaka muyaya. Ine Mulungu wako ndiye ndidzakhale ulemerero wako. Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe. Chokuunikira ngati dzuŵa sichidzaloŵanso, ndipo chokuunikira ngati mwezi sichidzazimiriranso, chifukwa ndi Chauta amene adzakhala kuŵala kwako mpaka muyaya. Choncho masiku ako olira adzatha.
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya. Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa. Tsono popeza tikudziŵa kuti Ambuye ngoyenera kuŵaopa, timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziŵa kwathunthu, ndipo tikhulupirira kuti inunso mumatidziŵa kwenikweni m'mitima mwanu. Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima. Ngati tidachita ngati tapenga, tidachita zimenezi kuti tilemekeze Mulungu. Koma ngati tikuchita zanzeru, tikuchita zanzeru kuti tikuthandizeni. Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo. Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero. Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano. Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike. Nchifukwa chake tsono tikubuula ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu yakumwambayo,
Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Pakuti tikudziŵa kuti Mulungu amene adaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa, adzatiwukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatifikitsa pamodzi nanu pamaso pake.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.
Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa. Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Musachite nazo mantha zoŵaŵa zimene mukukakumana nazo. Ndithu enanu Satana adzakuponyetsani m'ndende kuti akuyeseni, ndipo mudzazunzika pa masiku khumi. Khalani okhulupirika mpaka kufa, ndipo ndidzakupatsani moyo ngati mphotho yanu.
Popeza kuti tili mwa Khristu Yesu, Mulungu adachita ngati kutiwukitsa kwa akufa pamodzi naye, kuti choncho atipatse malo aulemu pamodzi naye m'dziko la Kumwamba. Adachita zimenezi kuti mwa chifundo chake chimene adatichitira mwa Khristu Yesu, aonetse kwa nthaŵi zonse zam'tsogolo kuti ngwokomadi mtima kopambana.
Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti. Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.
Koma tsopano mwamasulidwa ku uchimo, ndipo ndinu otumikira Mulungu. Phindu lake ndi kuyera mtima, ndipo potsiriza pake kulandira moyo wosatha.
Ngodala amene amachapa mikanjo yao, kuti aloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyo, ndiponso kuloŵa mu mzinda kudzera pa zipata zija.
Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka. Pakuti monga imfa idadza pansi pano kudzera mwa munthu wina, momwemonso kuuka kwa akufa kudadza kudzera mwa munthu wina. Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.
Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.
Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa.
Mulungu ndiye amene adatikonzeratu kuti tilandire zimenezi, ndipo adatipatsa Mzimu Woyera ngati chikole chake.
Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ”
kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
Monga Atate amaukitsa akufa, naŵapatsa moyo, moteronso Mwana amapatsa moyo kwa amene Iye afuna.
Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa. Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Adachita zimenezi, kuti mwa kukoma mtima kwake tisanduke olungama pamaso pake, ndipo tikalandire moyo wosatha umene tikuuyembekeza.
Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine.