Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, palibe ntchito yaikulu kuposa yothetsa mtendere pakati pa Mulungu ndi anthu, kutanthauza kuwathandiza ena kuti adziwe Yesu Khristu. Dziko lathu likufunikira Mulungu kwambiri, ndipo inuyo mwakuitanidwa kuti mutsogolere m'badwo kuchoka mu mdima kupita ku kuunika kodabwitsa.
Mukakhala ndi chifukwa chomwe Khristu adamwalirira mumtima mwanu, mudzakhala ndi chilakolako chofuna kulalikira uthenga wabwino. Monga momwe chikondi cha Atate chinafikira mu moyo wanu ndi kukusonyezani chifundo chake, ndikofunikira kuti mugawane ndi ena omwe akuzungulirani.
Nthawi iliyonse ndi nthawi yoyenera kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Kupulumutsa miyoyo ya anthu ndi chikondwerero chopanda malire kumwamba, ndikusangalatsa mtima wa Yesu powerenga kuti pali anthu omwe amamvetsa ntchito yomwe adachita chifukwa cha anthu.
Mulungu safuna kuti wina aliyense atayike, ndipo wakupatsani inu ntchito yopezera anthu otayika ndi kuwapulumutsa ku chiwonongeko. Kupulumutsa miyoyo ya anthu kuyenera kukhala chisangalalo chachikulu kwa mwana wa Mulungu, chifukwa pogwira ntchito imeneyi yomwe Yesu anatipatsa, timabweretsa chimwemwe kumwamba.
Kumbukirani zomwe zalembedwa m'buku la Yakobo 5:20, "Amene abweza wochimwa ku cholakwa chake adzapulumutsa moyo wake ku imfa, ndipo adzaphimba machimo ambiri."
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.
Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Ndine mfulu, osati kapolo wa munthu wina aliyense ai, komabe ndidadzisandutsa kapolo wa anthu onse, kuti ndikope anthu ambiri.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Kwa Ayuda ndidakhala ngati Myuda, kuti ndiŵakope. Ngakhale ineyo sindilamulidwa ndi Malamulo a Mose, komabe kwa Ayuda amene ali olamulidwa ndi Malamulowo, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chao chomwe choipitsidwa ndi machimo.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Abale, chimene ndimakhumbitsa ndi mtima wanga wonse, ndipo chimene ndimapempha Mulungu, ndi chakuti Aisraele apulumuke.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo.
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe. Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, mutiwunikire ndi chikondi chanu, Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.
Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu. Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake. Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu.
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
“Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola? Okolola ayamba kale kulandira malipiro, ndipo akututira mbeu ku moyo wosatha, kuti obzala ndi okolola akondwere pamodzi.
Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.
Munda uja ndi dziko lino lapansi. Mbeu zabwino zija ndi anthu ake a Ufumu wakumwamba. Namsongole uja ndi anthu ake a Woipa uja.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu.
Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungiza Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu.
Mafumu onse a m'dziko adzakutamandani, Inu Chauta, chifukwa amva mau a pakamwa panu. Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta, pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Uŵapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe. Uŵalanditse amene akuyenda movutikira popita kukaŵapha.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Onseŵa ankalimbikira kupemphera ndi mtima umodzi, pamodzi ndi akazi ena, ndi Maria amai ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.
Chautayo akunena kuti, “Nchinthu chochepa kwambiri kuti ukhale mtumiki wanga, kuti udzutse mafuko a Yakobe ndi kuŵabweza kwao Aisraele amene adapulumuka. Ndidzakusandutsa kuŵala kounikira mitundu ina ya anthu, kuti chipulumutso changa chikafike mpaka ku mathero a dziko lapansi.”
Ndikamaitana, mundiyankhe Inu Mulungu, Mtetezi wanga. Mudabwera kudzandithandiza pamene ndinali m'mavuto. Mundichitire chifundo, ndi kumvera pemphero langa.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Ndithu kunena zoona, aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu.
Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
Anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Chauta, mabanja a mitundu ina ya anthu adzampembedza.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Abale, ndikufuna kuti mudziŵe kuti zimene zandigwera, zathandiza ndithu kufalitsa Uthenga Wabwino.
Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.
Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.
Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
ndikuyembekeza kudzakuwonani pamene ndidzadzera kwanuko popita ku Spaniya. Ndidzakondwera kukuchezerani masiku angapo, ndipo pambuyo pake ndifuna kuti mudzandithandize kupitiriza ulendo wanga.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.
Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m'khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”