Uthenga Wabwino wopulumutsa anthu onse ndi ntchito yaikulu imene Yesu anatipatsa ife okhala padziko lapansi. Lamulo ili silikokera kwa anthu ochepa ayi, koma kwa ife tonse amene timadzitcha ana a Mulungu. Choncho, kuyanjanitsa dziko lino ndi Atate kuyenera kukhala cholinga chako chachikulu.
Sungakhale chete kapena kunyalanyaza kufunika kwa Mulungu komwe anthu ali nako. Sungakhale wopanda kanthu kapena wosasamala m’dziko limene tsiku ndi tsiku likuchotserapo Mulungu, pamene anthu ambiri akupita ku gehena. Mbadwo uno ukulira kuti uthandizidwe, ndipo si angelo amene anaitanidwa kufalitsa uthenga uwu wa mtendere, koma iwe.
Monga momwe chipulumutso chinafikira pa moyo wako, tsopano ndi nthawi yoti ukhale njira yopezera chipulumutso kwa ena. Kukhala mmishonale si ntchito yopepuka; okhawo amene amatsogoleredwa ndi Mzimu ndi amene angathe kukwaniritsa lamulo la Mulungu.
Kulimba mtima poyang’anizana ndi mavuto ndi mazunzo, osakana chikhulupiriro, ngakhale utanyozedwe, kuzunzidwa ndi kukankhidwa, kungatheke kokha chifukwa cha mphamvu ya Mzimu Woyera wa Mulungu. Dziwa kuti pali mphoto yaikulu kumwamba kwa amene amafunafuna mokoma mtima anthu otayika, pakuti ichi ndicho chinam’gwirizitsa Yesu pa mtanda, ndipo amasangalala kwambiri akaona otsatira mapazi ake.
Monga mmene Aroma 10:14-15 imanenera: “Koma adzam’itana bwanji Iye amene sanam’khulupirire? Ndipo adzam’khulupirira bwanji Iye amene sanam’ve? Ndipo adzamva bwanji wopanda mlaliki? Ndipo adzalalikira bwanji ngati sanatumidwe? Monga mwalembedwa, Ndi okongola mapazi a iwo amene alalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino.”
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.
Paulo ndi Barnabasi atalalika Uthenga Wabwino ku Deribe kuja, ndi kukopa okhulupirira ambiri, adabwerera ku Listara, ku Ikonio ndi ku Antiokeya m'dera la Pisidiya. Adaŵalimbitsa mtima ophunzira aja, naŵauzitsa kuti asataye chikhulupiriro chao. Adaŵauza kuti, “Kuti tiloŵe mu Ufumu wa Mulungu tiyenera kupirira masautso ambiri.”
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko. Koma kumudzi kumene mukaloŵe, anthu nkupanda kukulandirani bwino, mukapite m'miseu yam'mudzimo, nkukanena kuti, ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la m'mudzi mwanu muno limene linamamatira ku mapazi athu. Komabe dziŵani kuti ufumu wa Mulungu wafika.’ Kunena zoona, pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga mudzi umenewo. “Uli ndi tsoka, iwe Korazini! Uli ndi tsoka, iwe Betsaida! Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa inu, achikhala zidaachitikira ku Tiro ndi ku Sidoni, bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima. Koma pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu. Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.” Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.” Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni. Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Koma sindilabada konse za moyo wanga, ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malinga ndikatsirize ntchito yanga, ndi utumiki umene Ambuye Yesu adandipatsa, ndiye kuti kulalika poyera Uthenga Wabwino wonena za kukoma mtima kwa Mulungu.
Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake. Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno. Mundipempherere tsono kuti ndichifotokoze bwino monga ndiyenera.
Chifukwa cha zimenezi ndidzakutamandani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.
Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Patapita masiku angapo, Paulo adauza Barnabasi kuti, “Tiyeni tibwerere tizinka tiyendera abale ku mzinda uliwonse kumene tidalalikako mau a Ambuye.”
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo. Zonsezi ndimazichita chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti inenso ndilandire nao madalitso a Uthengawo.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.
Koma Iye adaŵauza kuti, “Ndiyenera kukalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso, pakuti ndizo zimene Mulungu adanditumira.”
Masiku onse ndinkayesetsa kulalika Uthenga Wabwino kumalo kokhako kumene dzina la Khristu linali lisanamvekebe. Ndinkaopa kumanga pa maziko amene munthu wina adaika.
Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
Munthu aliyense akakana kukulandirani kapena kumvera mau anu, musanse fumbi la kumapazi kwanu potuluka m'nyumbamo kapena m'mudzimo. Ndithu ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga mudzi wa Sodomu ndi wa Gomora, koma osati polanga mudzi umenewo.
Okhulupirira Khristu aja, amene anali atabalalikana chifukwa cha mazunzo omwe adabuka pa nkhani ija ya Stefano, adafika mpaka ku Fenisiya, ku Kipro, ndiponso ku Antiokeya. Sankalalika mau kwa munthu wina aliyense, koma kwa Ayuda okha. Tsono pamene Petro adabwera ku Yerusalemu, a m'gulu lolimbikira za kuumbala adatsutsana naye. Koma pakati pao panali ena ochokera ku Kipro ndiponso ku Kirene. Ameneŵa adafika ku Antiokeya nayamba kulankhulanso ndi Agriki nkumaŵalalikira Uthenga Wabwino wonena za Ambuye Yesu. Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.
Koma pakati pao panali ena ochokera ku Kipro ndiponso ku Kirene. Ameneŵa adafika ku Antiokeya nayamba kulankhulanso ndi Agriki nkumaŵalalikira Uthenga Wabwino wonena za Ambuye Yesu.
Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.
Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.”
Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.
Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe.
Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse.
kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungiza Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha. Pamene ndinali ku Tesalonika, mudatumiza kangapo zondithandiza pa zosoŵa zanga.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Tsiku lina Chauta adauza Abramu kuti, “Choka kudziko kwako kuno. Usiye abale ako ndi banja la bambo wako, ndipo upite ku dziko limene nditi ndikusonyeze. Koma m'dziko limenelo mudagwa njala. Ndipo chifukwa choti njala idaakula kwambiri, Abramu adapitirira ndithu chakumwera, mpaka kukafika ku Ejipito, nakhala kumeneko kanthaŵi. Pamene anali pafupi kuwoloka malire a Ejipito, adauza mkazi wake Sarai kuti, “Ndikudziŵa kuti iwetu ndiwe mkazi wokongola. Ndipo Aejipito akakupenya, aziti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake,’ tsono kuti akukwatire iwe, andipha ineyo. Chonde, uzikaŵauza kuti, ‘Ndi mlongo wanga.’ Motero zonse zidzandiyendera bwino chifukwa cha iwe, ndipo ndidzapulumuka.” Abramu ataoloka malire kuloŵa mu Ejipito, Aejipito adaonadi kuti mkazi wake ndi wokongola kwambiri. Akalonga a mfumu ya ku Ejipito atamuwona mkaziyo, adakauza Farao za kukongola kwake. Pomwepo anthu aja adamtenga mkaziyo kukamuika ku nyumba ya mfumu. Ndipo Farao adamchitira zabwino Abramu uja chifukwa cha mkaziyo, nampatsa nkhosa, mbuzi, ng'ombe, abulu, ngamira ndiponso akapolo aamuna ndi aakazi. Koma Chauta adagwetsa nthenda zoopsa pa Farao ndi pa anthu a m'nyumba mwake omwe, chifukwa cha Sarai mkazi wa Abramu. Apo Farao adaitana Abramu namufunsa kuti, “Kodi iwe, wandichita zotani? Bwanji osandiwuza kuti ameneyu ndi mkazi wako? Bwanji umanena kuti ndi mlongo wako kuti ine ndimukwatire? Nayu mkazi wako. Mtenge, ndipo uchoke!” Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. “Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno,
Kapena Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha kodi? Suja alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina? Ndithu ndiyenso Mulungu wa anthu a mitundu ina.
Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.
Poyamba ndikuthokoza Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akusimba za chikhulupiriro chanu.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Paulo adaŵauza kuti, “Dziŵani tsono kuti Mulungu watumiza chipulumutso chakechi kwa anthu a mitundu ina. Iwowo adzamva.” [
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo. Ndidzakulanditsa kwa anthu a mtundu wako, ndiponso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutuma. Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’
Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino.
Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.
Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana. Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
ndipo adzakutumizirani Yesu uja amene adamusankhuliratu kuti akhale Mpulumutsi wanu. Iyeyo anayenera kukhala Kumwamba mpaka nthaŵi yakukonza zonse kwatsopano, monga Mulungu adanenera kuyambira kalekale mwa aneneri ake oyera mtima.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Mulungu wathu ndiye amene amandiveka mphamvu, wandichotsera zoopsa m'njira zanga. Amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbaŵala, ndipo amandisunga bwino m'mapiri. Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.
Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.
Tumizani kuŵala kwanu ndi choona chanu kuti zinditsogolere. Zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kokhala Inu.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Zitachitika zimenezi, Paulo adatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Masedoniya ndi ku Akaiya. Adati, “Kuchokera kumeneko ndiyeneranso kukayenda ku Roma.”
Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu.
Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Pambuyo pake Yesu adanka nayendera mizinda ndi midzi akulalika ndi kuuza anthu Uthenga Wabwino wonena za ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja anali naye.
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Koma Malembo adaoneratu kuti anthu a mitundu ina pakukhulupirira, Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Nchifukwa chake Malembowo adaauziratu Abrahamu Uthenga Wabwinowu wakuti, “Mwa iwe Mulungu adzadalitsa anthu a mitundu yonse.”
Choncho tidatuma Timoteo, mbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yolalika Uthenga Wabwino wa Khristu. Tidamtuma kuti adzakulimbitseni mtima ndi kukukhazikitsani m'chikhulupiriro chanu,
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, mutiwunikire ndi chikondi chanu, Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.
Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”
“Ukuze malo omangapo hema lako, ufunyulule kwambiri nsalu zake. Usalephere, utalikitse zingwe zake, ndipo ulimbitse zikhomo zake. Udzasendeza malire ake uku ndi uku. Zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina, zidzadzaza mizinda imene idasiyidwa.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.
Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola?
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”
Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.