Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

132 Mau a Mulungu Okhudza Kutukuka

Pali chuma chimene sichidzachoka, sichofanana ndi cha dziko lino lapansi. Chuma chimenechi chimachokera kwa Mulungu ndipo chimakhalapo nthawi zonse, mosasamala kanthu za mavuto amene mukukumana nawo. Sichimaonekera mwa chuma chakuthupi koma mwa kukula kwa mzimu wanu.

Ndi zoona kuti Mulungu amafuna kuti mukhale ndi moyo wabwino pa chilichonse, koma zimenezi zimachitika pamene moyo wanu wauzimu ukukula. Pamene mukupambana mantha ndi mavuto anu, mukukula ngati munthu ndipo mukuyenda bwino tsiku ndi tsiku.

Yoswa 1.8 imati: “Buku ili la malamulo lisachoke pakamwa pako; koma uziliganizira usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; pakuti pamenepo udzakometsa njira yako, ndipo pamenepo udzapindula.” Anthu ambiri amakhala ndi moyo wabwino popanda Mulungu mumtima mwawo, koma sasangalala ndi moyo wabwino umenewu chifukwa saganizira Mawu a Mulungu. Amasankha kusamvera malamulo ndi mawu Ake. Pamapeto pake, amangokhala ndi nthawi yabwino kwakanthawi kochepa, koma osati chisangalalo cha moyo womasuka.

Mulungu safuna kuti ana ake azivutika choncho. Asanakupatseni chuma, amakukonzerani kuti musatayike chifukwa cha ndalama, pakuti “chikondi cha ndalama ndi muzu wa zoipa zonse.” Choncho, muyenera kuyenda motsatira mfundo zimene Atate anakhazikitsa m’Baibulo kuti mukhale ndi moyo wabwino ndipo njira yanu ikhale yopambana.

Kondani Mulungu kuposa zonse, iye akhale woyamba m'moyo mwanu, ndipo adzakondwera nanu, akudalitseni pa zonse zimene mukuchita, mudzapeza chiyanjo kwa anthu ndipo chisomo chake chidzakhala nanu kulikonse kumene mupita. Deuteronomo 8.18 imati: “Koma udzakumbukira Yehova Mulungu wako, pakuti ndiye wakupatsa mphamvu yakulengetsa chuma, kuti akhazikitse pangano lake, limene analumbirira makolo ako, monga lerolino.”


Masalimo 37:1

Usamavutika ndi anthu oipa. Usamakhumbira kukhala ngati ochita zoipa,

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:25

Munthu waumbombo amautsa mkangano, koma wokhulupirira Chauta adzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 22:23-27

Ubwerere kwa Mphambe modzichepetsa, uchotse zosalungama zonse zimene zimachitika m'nyumba mwako.

Golide wako yense umuyese wachabechabe, ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi,

Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.

Ukatero udzakondwa naye Mphambe, Udzaikapo mtima pa Mulungu mwamtendere.

Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:4

Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta, ndi chuma, ulemu ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 3:10

Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:11

Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 16:19

Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 18:25

Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 30:8-9

Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,

kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:7

Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 16:17

Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:17-19

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.

Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.

Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 11:24

Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 6:33-34

Komabe anthu ambiri adaŵaona akupita, naŵazindikira. Motero adathamanga pa mtunda kuchokera ku mizinda yonse, nakafika kumaloko, Yesu ndi ophunzira ake aja asanafike.

Pamene Yesu adatuluka m'chombomo, adaona chikhamu chachikulu cha anthu. Adaŵamvera chifundo anthuwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa, choncho adayamba kuŵaphunzitsa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:7-8

“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo.

Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 11:6

M'maŵa uzifesa mbeu zako, ndipo madzulo usamangoti manja lende. Sudziŵa chimene chidzapindula, kaya ndi ichi kaya ndi chinachi, mwinanso ziŵiri zonsezo zitha kukhala zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:21-22

Choipa chitsata mwini, koma wochita chilungamo amalandira zabwino.

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:25

Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 28:13

Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:14

Maphunzitso a anthu anzeru ali ngati kasupe wa moyo, amathandiza anthu kuti asakodwe mu msampha wa imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:17-18

Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza.

Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 5:12

Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:1-3

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 29:9

Mau onse a chipangano ichi muŵamvere mokhulupirika, kuti choncho mudzakhoze pa zonse zimene mudzachite.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:11

Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:8

Chauta adzadalitsa ntchito zanu, ndipo nkhokwe zanu zidzadzaza. Adzakudalitsani m'dziko limene akukupatsanilo.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 8:18

Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 127:1

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:22

Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:38

Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 22:13

Ukadzamvera mosamala malamulo ndi malangizo amene Chauta adalamula Mose kuti auze Aisraele, ndiye kuti zinthu zidzakuyendera bwino. Khala wamphamvu, limba mtima, usati uziwopa, usatinso ude nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:7-8

Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana.

Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 30:9

Chauta adzakupezetsani bwino pa zochita zanu zonse. Mudzakhala ndi ana ambiri, zoŵeta zambiri, ndipo minda yanu idzakubalirani zokolola zambiri. Adzakondwera nanu kuti mwakhoza chotere, monga momwe adakondwera ndi makolo anu pamene anali okhoza.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 6:10-12

Chauta, Mulungu wathu, adalonjeza makolo anu aja Abrahamu, Isaki ndi Yakobe kuti adzakupatsani inu dziko limene lili ndi mizinda ikuluikulu ndi yachuma, imene inu simudaimange.

Nyumba zake zidzakhala zodzaza ndi zinthu zabwino zimene inuyo simudaikemo. Zitsime zidzakhala zokumbiratu ndipo padzakhala minda yamphesa ndi yaolivi imene simudalime ndinu. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limeneli, ndipo mukadzakhala ndi chakudya chambiri,

musadzaiŵale Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, dziko laukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 3:13-14

Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”

Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 8:9

Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 2:20

Ine ndidaŵayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino, ndipo ife atumiki ake tiyambapo kumanga. Koma inuyo mulibe chanu muno, mulibe mphamvu yolandirira malo muno, ndipo mulibenso chilichonse chokumbutsa za inu mu Yerusalemu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:1-3

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.

Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 39:2

Chauta anali naye Yosefe, ndipo adamthandiza kuti zonse zimuyendere bwino. Adakhala m'nyumba ya bwana wake, Mwejipito uja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:1-2

Ngwodala aliyense woopa Chauta, amene amayenda m'njira zake.

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:12

Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 23:25

Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:5-6

Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu.

Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:21

Choipa chitsata mwini, koma wochita chilungamo amalandira zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 20:4

Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 48:17

Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:29

Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 35:27

Koma amene amafunitsitsa kuti ndipezeke wosalakwa, afuule ndi chimwemwe ndipo asangalale. Anene nthaŵi zonse kuti, “Chauta ndi wamkulu. Amakondwera akaona mtumiki wake zamuyendera bwino.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:1-2

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani.

Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani.

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.

Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira.

Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:

Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu.

Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu.

Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe.

Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse.

Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:14-15

Chauta akudalitseni inu, pamodzi ndi zidzukulu zanu zomwe.

Akudalitseni Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 5:19

Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:12

Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:7

Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:3

Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:21

Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:7-8

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 1:12

nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:2

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:19

Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:12-13

Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa. Nthaŵi zonse ali pabwino, ndipo amangolemera kosalekeza.

Ine ndasunga mtima wanga woyera, ndasamba m'manja kuwonetsa kuti ndine wosalakwa, koma zonsezi popanda phindu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 1:3

Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 104:27-28

Zonse zolengedwa zimayang'anira kwa Inu, kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.

Mukazipatsa zimachilandira; mukafumbatula dzanja lanu, zimakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 85:12

Inde, Chauta adzapereka zabwino, ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:19-20

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.

“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.

Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 26:12-13

Isaki adabzala mbeu m'dzikomo, ndipo chaka chimenecho adakolola dzinthu dzochuluka koposa, chifukwa Chauta adaamudalitsa.

Chuma chake chidanka chichulukirachulukira, ndipo adasanduka munthu wolemera kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 45:3

Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 10:12

Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 128:5

Chauta amene amakhala ku Ziyoni akudalitse. Uwone m'mene Yerusalemu zinthu zidzamuyendere bwino masiku onse a moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:19

Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:17

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 147:11

Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 146:5

Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:14

“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:32

Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:15

Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake, koma umphaŵi wa anthu osauka ndiye chiwonongeko chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:11

Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:3

Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:29

Ndikudziŵa kuti ndikadzabwera kumeneko, ndidzabwera ndi madalitso ochuluka a Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:18

Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:10

Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 73:26

Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 3:13

Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 4:6-7

Alipo ambiri amene amati, “Ndani angatiwonetse zabwino? Mutiyang'ane ndi chikondi chanu, Inu Chauta.”

Koma Inu mwandisangalatsa mtima kwambiri, kupambana anthu a zakudya ndi zakumwa zambiri!

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:10

Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:5-6

Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:29

Motero aliyense wosiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine, ameneyo adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka adzalandira moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:16

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 115:12

Chauta watikumbukira ndipo adzatidalitsa. Adzadalitsa anthu a Israele, adzadalitsa banja la Aroni.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:1

Pamene Chauta adabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati anthu amene akulota.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:31

Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 92:12

Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 10:13

Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:8

Kuchita choncho kudzapatsa thupi lako moyo, kudzalimbitsa mafupa ako.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:12-13

Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate.

Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 61:3

Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:35

Inu mwanditchinjiriza ndi chishango chanu chachipulumutso. Dzanja lanu lamanja landichirikiza, mwandikweza ndi chithandizo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 12:2

Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:4

Tibwezereni ufulu wathu, Inu Chauta, tikhale ngati mitsinje yam'chipululu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 58:10-11

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.

Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:19

Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:16

Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 2:3

Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 92:14

Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:6

Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga Wamuyaya, Ambuye Wamkulukulu! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate waulemerero, m'dzina la Yesu ndikupempherani chifukwa ndikudziwa kuti mwandilimbikitsa, nthawi zonse dzanja lanu landisamalira ndipo ndinu amene mumandipatsa mphamvu yopezera chuma. Atate ndithandizeni kumvetsetsa kuti ndinu Mulungu wachipembedzo, amene simugawana ulemerero wanu ndi wina aliyense ndipo mwandipanga kuti ndikukondeni ndi kukupembedzerani inu nokha. Mawu anu amati: "Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti chifukwa cha kukukondani iye anakhala wosauka, pokhala wachuma, kuti inu mukhale achuma mwa umphawi wake." Chifukwa cha ine munabwera padziko lapansi ndipo munavutika kuti ine ndikulemerere m'zinthu zonse. Ndikukupemphani kuti mundipatse nzeru zoyendetsera bwino ndalama, munditeteze ku dyera, kudzikuza ndi kudzikonda, mundithandize kumvetsetsa kuti sindiyenera kulamulidwa ndi ndalama, koma ndi chithandizo cha Mzimu Woyera wanu kuti ine ndilamulire zonse zomwe zimabwera m'manja mwanga, kuti ndibweretse mtendere m'moyo wanga ndi m'banja langa. Ambuye ndikulakalaka kuchita bwino pazonse zomwe ndichita. Dalitsani, Ambuye. Mundipangitse kukhala wopambana, kuti ndigaŵane zonse zomwe ndikudziwa, popanda mantha kapena kudzikuza, ndi amene akufunikira ziphunzitso zanga ndi uphungu wanga. Ndithandizeni kukhala ndi mtima wodzichepetsa ndi wodalira inu. Mzimu Woyera mundisunge ndi mtima woyamikira mosasamala kanthu za mkhalidwe wanga kaya ndili ndi zambiri kapena zochepa komanso kukhala wokonzeka kuthandiza ena. M'dzina la Yesu. Ameni.