Ine ndikudziwa kuti Yesu, munthu wolungama amene anakhala padziko lapansi, ndiye chitsanzo chabwino cha nzeru ndi ungwiro. Iye ndiye woweruza woona, wosanama, komanso wopanda.
Chikondi ndi chifundo chake pa anthufe chimamupangitsa kumva ululu wathu tsiku ndi tsiku. Ndiye M'busa wabwino, mphunzitsi, mnzanga, mbale, komanso loya wathu wamkulu.
Kudalira anthu sikungatithandize kupambana, koma Baibulo mu 1 Yohane 2:1 limatiuza kuti Yesu Khristu ndiye loya wathu kwa Atate. Kaya muli pamavuto otani, Yesu amadziwa ndipo akumvetsa.
Kupita kwa Iye kuti akutetezeni ndiye chisankho chanzeru kwambiri. Mulungu akamakuthandizani, muli otetezeka. Mtima wake ndi wolungama, sadzachita zoipa, ndipo maganizo ake onse ndi abwino.
Ngati mwakumana ndi chisalungamo kapena kugwera mumsampha, pitani kwa Woweruza wabwino, muuzeni mavuto anu, ndipo mulole agwire ntchito m'malo mwanu. Musamafune kubwezera choipa ndi choipa, koma dalirani Mulungu. Mukamuuza mavuto anu, adzakumverani ndipo adzakuthandizani.
Khalani paubwenzi wolimba ndi Iye ndipo sungani mtendere, ngakhale mutakumana ndi mavuto, chifukwa mawu omaliza ndi a Mulungu. Mukadziwa Yesu ngati loya wanu, mudzaona momwe adzakhazikirire adani anu.
Mau onse a mdierekezi okunenani kuti ndinu wolakwa adzatha ndi mphamvu ya magazi a Yesu. Chifukwa cha Iye, ndinu omasuka ndipo mulibe chiweruzo. Aleluya.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.
Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.
Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Chauta Wamphamvuzonse alimo m'dziko la Ejipito. Aejipito akadzalira kwa Chauta pa zovuta zao, Iye adzatuma mpulumutsi kuti aŵateteze ndi kuŵapulumutsa.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.
Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya, ndipo mzindawu ndidzautchinjiriza.’ ”
Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake, Chauta Wamphamvuzonse adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu. Adzauteteza ndi kuupulumutsa, adzausiya pambali ndi kuuwombola.”
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ndidzakumenyera nkhondo yako, ndipo ndidzakulipsirira. Ndidzaumitsa nyanja ya ku Babiloni, akasupe ake onse adzaphwa.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo, kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo. Palibe adani amene adzaŵapambane, pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.”
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Pulumutseni kwa adani anga, Inu Mulungu wanga, tetezeni kwa anthu ondiwukira.
Mulungu wanga adzandichingamira chifukwa ndi wa chikondi chosasinthika. Mulungu wanga adzandilola kuti ndisangalale poona adani anga atagonja.
Musaŵaphe pomwepa, kuwopa kuti anthu anga angaiŵale, koma muŵabalalitse ndi mphamvu zanu, ndipo muŵagwetse, Inu Ambuye, Inu chishango changa.
Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,
muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi.
Amabweranso madzulo aliwonse akuuwa ngati agalu, nkumangoyendayenda mu mzinda.
Amanka nafunafuna chakudya ndipo amangofuula akapanda kukhuta.
Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga.
Inu mphamvu zanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokuyamikani, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa, ndinu Mulungu wondiwonetsa chikondi chosasinthika.
Pulumutseni kwa anthu ochita zoipa, landitseni kwa anthu okhetsa magazi.
Tiyeni, Inu Chauta, dzukani kuti munditchinjirize pa mlandu wanga, Inu Mulungu wanga ndi Ambuye anga.
Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu. Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa.
Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo;
Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse.
Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?
Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja.
Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana.
Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.
Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.
Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza.
Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso.
Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga.
Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.
Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu.
Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni. Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu.
Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye.
Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo.
Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.”
Ngati wina autsa nkhondo, si ndine ndachititsa ai. Amene alimbana nawe adzalephera, poti udzaŵagonjetsa.
Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.