Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

116 Mau a Mulungu Okhudza Chikondi

Chikondi sichisonyeza ndi mawu okha, koma ndi zochita. Taonani Yesu, anatifera ife tonse, kuti machimo athu akhululukidwe. Anakonda kwambiri moti anadzipereka yekha.

Sanalankhule zambiri, koma anangokhala chete, akuvumbula zowawa zomwe tinali kuyenera ife chifukwa cha zoipa zathu. Yesu ndiye chitsanzo chabwino kwambiri choti titsatire. Kutsatira njira yake yachikondi ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.

Mulungu amafuna kuti tizikondana monga momwe Iye watikondera ife. Chikondi chenicheni chimachokera kwa Mulungu, amene ndiye kasupe wosatha wa chikondi. Mukalandira chikondi chake, mudzaphunzira kukonda anthu ena popanda malire.

Mulungu akufuna kuti abale ndi alongo athu azikondana ndi kudzipereka kwa anthu osowa. Dziko lino lilibe chikondi chokwanira, ndipo inu mukuyenera kukhala chitsanzo cha Yesu padziko lapansi.

Chikondi sichiona mtundu wa khungu kapena udindo wa munthu. Sichinthu choti ena akuchitireni, koma ndi chimene inuyo mungachite kwa ena. Ndicho chikondi chenicheni.


1 Akorinto 16:14

Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:21

Amene amatsata chilungamo ndi chifundo adzapeza moyo ndi ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:4-7

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona.

Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:26

Thokozani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 3:16

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 2:4-5

Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana.

Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:8

Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:14

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:3-4

Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako.

Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse.

Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse.

Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo.

Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa.

Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima.

Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.

Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:16

Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:13

Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 22:37-39

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu.

Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:2

Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:2

Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:15

Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:9

Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,

ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:12

Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:44

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:2

Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 3:15

Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:10

Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:12

Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:20

Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 143:8

Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:1

Pitirizani kukondana monga abale.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:13

Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:18

Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 3:12

Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:5

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:1

hokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:22

Mwayeretsa mitima yanu pakumvera choona, kotero kuti muzikondana ndi akhristu anzanu mosanyenga. Nchifukwa chake muzikondana ndi mtima wonse, mosafookera.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.

M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:1

Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:30

“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ndi womwaza.

Mutu    |  Mabaibulo
Yuda 1:2

Mulungu achulukitse chifundo chake, mtendere wake ndi chikondi chake kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:2

Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:10

Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:35

Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:10

Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 103:8

Chauta ndi wachifundo ndi wokoma mtima, ndi wosakwiya msanga, ndipo chikondi chake chosasinthika nchachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 42:8

Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 8:3

Koma munthu akamakonda Mulungu, ndiye kuti amadziŵika ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:15

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 63:9

Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 5:3

Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:14

Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:4

Chauta yekhayo amachita zodabwitsa zazikulu, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 1:4-5

Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.

Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 5:14

Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:15

Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:1-2

Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.

Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza,

Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.

Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu.

Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi.

Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko.

Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:17

Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 100:5

Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 49:15

Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:2

Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:12-14

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:1-3

Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.

koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha.

Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo.

Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.

Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.

Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse.

Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:5

Adalenga zakumwamba ndi nzeru zake, pakuti chikondi chake nchamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 22:39

Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 3:17-19

Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu.

Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:6

Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:8-9

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Poyenderana, muzisamalirana bwino mosadandaula.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:8

Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:12

Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:4

Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:11-12

Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni.

Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 13:11

Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:25

Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:38

Komabe pakuti Mulungu ngwachifundo, adaŵakhululukira machimo ao, ndipo sadaŵaononge. Kaŵirikaŵiri ankadziletsa kukwiya, sadalole kuti mkwiyo wake wonse uyake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:5

Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:64

Inu Chauta, dziko lapansi nlodzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 2:17

Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:30

Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:2

Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 116:1-2

Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba.

Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.”

Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.”

Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira?

Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.

Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse.

Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake.

Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga.

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.

Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse.

Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta!

Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:16-18

Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.

Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 131:2

Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:13

Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 89:1

Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika. Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:14

Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:5

Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:21

Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:159

Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:7-9

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 3:5

Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m'chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:23

Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:23

Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, koma amalanga koopsa anthu odzikuza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:16-17

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.

Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 13:4-8

Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza.

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona.

Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.

Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Atesalonika 2:16-17

Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma.

Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:1

Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:7

Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:8

Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, landirani ulemu ndi kutamanda konse, pakuti Inu nokha ndiye woyenera. Ndikupempherani m'dzina lamphamvu la Yesu, ndikuthokozani chifukwa cha kukhalapo kwanu ndi chithandizo chanu, chifukwa mwalidi chishango changa ndi pothawirapo panga. Atate wanga wokondedwa, ndikukupemphani kuti mundithandize kuona mnzanga ndi maso anu ndikumukonda ndi mtima wanu. Ndithandizeni kumvetsera anthu ndikumva chisoni chawo kuti ndiwathamange momwe ndingathere. Mundipatse mtima wopatsa kuti ndithandize amasiye, osauka ndi ana amasiye. Mzimu Woyera, chonde ndithandizeni kukhululukira onse andipweteka mwanjira ina iliyonse, chiritsani mtima wanga kuti pasakhale kukhumudwa kapena njiru ndikakumana nawo. Mawu anu amati: “Zoonadi ndikukuuzani, chilichonse chimene munachitira m'modzi wa abale anga awa aang'ono, munandichitira Ine.” Ndithandizeni kutumikira mnzanga monga momwe Yesu anachitira, ndikufuna kukhala chombo champhamvu yanu ndi ulemerero wanu, kukhala woyang'anira bwino chuma changa kuti ndithandize amene mungandiuze. Mundipatse nzeru kuti ndikhale ndi ubale wabwino, wolimbikitsana komanso wopindulitsa ndi banja langa, abwenzi ndi ogwira nawo ntchito. Ndikupemphani Mulungu wanga kuti mudzaze mtima wanga ndi chikondi chifukwa ndi chomangira cha ungwiro. M'dzina la Yesu. Ameni.