Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

116 Mau a M'Baibulo Okhudza Aphunzitsi

Ndikufuna ndikuuzeni, ntchito yophunzitsa m’thupi la Khristu ndi yofunika kwambiri. Kudzera mu zimene mumaphunzitsa, mpingo umamangika. Inu ndinu kuunika mu mdima, ndinu kumveka bwino m’dziko la chisokonezo, ndipo ndinu mawu oyenera nthawi yake otsogolera mtima.

Ndi dalitso lalikulu kukhala mphunzitsi wa Mawu a Mulungu m’nthawi ino, chifukwa dziko lino likufunika kutsogoleredwa ku choonadi cha Khristu. N’chifukwa chake muyenera kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mzimu Woyera kuti mumvetse bwino zimene Atate amalankhula kwa anthu ake.

Musaphunzitse zinthu zolakwika zochokera mwa inu nokha kapena m’nzeru zanu, koma muzimangirira pa nzeru za Mulungu Wamphamvuyonse. Ngati ndinu mphunzitsi, musapatuke pa Mawu a Mulungu ndipo lankhulani moganizira bwino. Samalani kuti musaphunzitse zinthu zosalungama, chifukwa kumbukirani kuti mudzaweruzidwa ndi Ambuye pa chilichonse; yesetsani kuti musapezeke ndi mlandu.

Lemba la Agalatiya 6:6 limati: “Wophunzitsidwa mawu a Mulungu agawirene mphunzitsi wake zinthu zake zonse zabwino.”


Yakobo 3:1

Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:2

Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:19-20

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.

Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo.

Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 5:12

Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:11

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:99

Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 18:20

Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 13:13

Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:4-5

Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:4

Msilikali amene akumenya nkhondo sasamalako ntchito zakumudzi, chifukwa iye amangofuna kukondweretsa mkulu wa ankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:2-3

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.

Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 7:16

Yesu adati, “Zimene ndimaphunzitsa si zangatu ai, ndi za Atate amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:16

Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 9:9

Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:29

chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.

Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo.

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 3:14-15

Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa.

Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 44:23

“Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zoyera ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekera nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 5:42

Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:66

Patseni luntha ndi nzeru, chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 18:26

Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 15:35

Paulo ndi Barnabasi adakhalabe ku Antiokeya, akuphunzitsa ndi kulalika mau a Ambuye pamodzi ndi anthu ena ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:13

Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 5:17

Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 29:15

Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 32:8

Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 3:6

Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:28

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:24

Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:30

Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 13:14

Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:24-27

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.

Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.

Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga.

Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:6

Munthu amene akuphunzira mau a Mulungu, agaŵireko mphunzitsi wake zabwino zonse zimene iye ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:135

Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:7

Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 51:6

Ndithudi, Inu mumakonda mtima woona, choncho mundiphunzitse nzeru zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:14

Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:11-12

Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama.

Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 6:6-7

Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.

Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 54:13

Anthu ako ndidzaŵaphunzitsa ndekha, Ine Chauta, ana ako ndidzaŵadalitsa ndi kuŵapatsa mtendere waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:4

Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:24-25

Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai.

Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:19-20

Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.

Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu.

Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:21

Wa mtima wanzeru amamutcha wozindikira bwino zinthu, kulankhula kwake kokometsera kumakulitsa mphamvu ya mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 2:11-12

Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake.

Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:11-12

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.

Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:171

Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:14

Anzeru amakundika nzeru, koma kubwebwetuka kwa chitsiru kumadzetsa chiwonongeko.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:8

Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 28:10

Akuyesa kumatiphunzitsa pang'onopang'ono lemba ndi lemba, mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro. Zonsezo akungoti apa pang'ono, apa pang'ono.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:130

Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:9

Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:7

Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:22

Nzeru ndi kasupe wopatsa moyo kwa amene ali nazo, koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa anthu opusa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:6

Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:12

Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 2:3-4

Chimodzimodzinso azimai achikulire, uŵauze kuti azikhala ndi makhalidwe oyenera azimai oyera mtima. Asakhale osinjirira anzao kapena akapolo a zoledzeretsa. Akhale alangizi abwino,

kuti choncho athe kuphunzitsa azimai achitsikana kukonda amuna ao ndi ana ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 3:26-27

Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu.

Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 4:15

Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 6:12

Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:13

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani.

Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.

Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.

Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:101

Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 30:5

Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:148

Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:4

Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:11

Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 24:5

Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:7

Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:174

Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:10-11

Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.

Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:20-21

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.

Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 22:22

Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Petro 3:18

Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:5

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 1:11-12

Abale, ntakuuzani: Uthenga Wabwino umene ine ndimalalika, ndi wosachokera kwa anthu.

Sindidaulandire kwa munthu, ndipo palibenso munthu amene adandiphunzitsa Uthengawo, koma ndi Yesu Khristu yemwe amene adawuulula kwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:21

Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 5:14

Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 2:1-5

Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga.

Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa.

Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza.

Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri,

amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima.

Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama.

Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga.

Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika,

amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake.

Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa.

Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo.

Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu.

Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo.

Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo.

Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo.

Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu.

Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika.

Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 2:7

Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:19

Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:24

Malamulo anu amandikondwetsa, ndiwo amene amandilangiza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:31

Imvi zili ngati chisoti chaufumu chopatsa ulemerero, munthu amazipata akakhala ndi moyo wautali.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:13-14

Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:1-2

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.

Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka.

Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama.

Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai.

Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo.

Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa.

Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira.

Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu.

Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao.

Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu.

Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.

Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 4:10-11

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 12:11

Mau a anthu anzeru ali ngati zisonga, ndipo zokamba zao zimene adasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomerera kwambiri. Zolankhula zonsezo amapereka ndi Mbusa mmodzi yekha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:20

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:19

Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:40

Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:7

Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:21

Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wanga, Mpulumutsi! Lero ndikufuulirani, ndikuyang'ana nkhope yanu kuti ndikupatseni ulemerero ndi ulemu. M'dzina lamphamvu la Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha utumiki umene mwandipatsa monga mphunzitsi. Ambuye, ndipatseni kuti ndizichita ndi chikondi, nzeru, kuzindikira, kuleza mtima ndi mphamvu mogwirizana ndi chifuniro chanu. Ndithangateni kuti ndilankhule ndikuchita zinthu motsogozedwa ndi Mzimu Woyera wanu, ndi maso anu achifundo kuti ndingofuna zabwino ndi kukula m'mawu anu kwa aliyense amene amandimvera. Ndipatseni mtima wanzeru ndi wozindikira kuti ndiphunzitse zimene inu Ambuye mukufuna kuti ndilankhule. Mawu anu amati: “Chotero ngati wina adzidziyeretsa ku izi, adzakhala chotengera cholemekezeka, chopatulika, chothandiza kwa mbuye wake, chokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” Ndikufuna kuwadziwitsa makhalidwe anu Yesu, zokhumba za mtima wanu ndi amene muli kwa mpingo wanu. Ndithangateni kuwalangiza, kuwaphunzitsa ndi chifundo ndi kulimba mtima monga momwe inu munkachitira, ndithangateni kuwongolera zolakwa zawo. Ndipatseni kuti ndiwayese kukhala omanga chilungamo ndi mtendere, kuwona mtima, ubale ndi chikhululukiro, oteteza moyo ndi choonadi kwa ophunzira amene mwandipatsa. Ndi chifatso ndigawane nawo chikhulupiriro, ndiwapatse chiyembekezo kuti apatsire ena. M’dzina la Yesu. Ameni.