Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

71 Mau a Mulungu Paubwenzi: Nthawi Yabwino Kwambiri

Kale lomwe dziko lisanakhaleko, Mulungu anali atakukumbukira iwe. Anakukonzeratu moyo wako ndipo anaika mzimu wake mwa iwe kuti ukhale mwana wake.

Mulungu ndi Atate wabwino kwambiri, chikondi chake ndi choyera komanso chopanda malire, ndiye wabwino kuposa onse, amakukonda popanda chifukwa chilichonse.

Mwina unamvapo za Mulungu ndi mphamvu zake zazikulu, mwina mwa nkhani za anthu ena kapena mwa zimene waona mwa anthu, koma lero Mulungu akufuna kudziwitsa kwa iwe ngati Atate wako.

Mwina mpaka pano wamuwona ngati wochiritsa, woteteza kapena wopereka, koma tsopano akufuna kudzionetsa m'mtima mwako kuti umvetse kuti mwa iye uli ndi Atate wachikondi amene sadzakusiya, koma adzakhala nawe nthawi zonse.

Mulungu ndi Atate wathu Wakumwamba, wodzala ndi ubwino, chifundo ndi chikondi. Mulungu ndi wabwino! Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulumeka iye asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mulungu anapereka mwana wake chifukwa cha chikondi, kusonyeza kufunika kwako kwa iye. Yandikirani kwa Mulungu tsiku lililonse, mudziwe ndipo sangalalani ndi chikondi chake ndi chipulumutso chimene wakupatsani.


Masalimo 103:13

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:24

Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:5

Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:6

Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 18:14

Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:11

Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:48

Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:36

Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:2

M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:13

Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 8:6

koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:32

Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 63:16

Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israele satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wachikhalire ndi dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:32

Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:15

Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:20

Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi, Amen.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:16

Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthawi yonse,

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:21

Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:8

Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala ophunzira anga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 64:8

Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:21

Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 14:36

Ndipo ananena, Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:6

Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:26

Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 1:12

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 6:57

Monga Atate wamoyo anandituma Ine, ndipo Inenso ndili ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya Ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:9

Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 17:24

Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:6

Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:28

Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 12:32

Ndipo mlembiyo anati kwa Iye, Chabwino, Mphunzitsi, mwanena zoona kuti ndiye mmodzi; ndipo palibe wina, koma Iye:

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:23

Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:15

Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:33

Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:27

Zinthu zonse zinaperekedwa kwa Ine ndi Atate wanga; ndipo palibe munthu adziwa Mwana, koma Atate yekha, ndi palibe wina adziwa Atate, koma Mwana yekha, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:15

Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:7-9

Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?

Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.

Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:13-14

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine.

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 1:12-13

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;

amene sanabadwe ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 6:18

ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 15:20

Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:18

Sindidzakusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 11:11-13

Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?

Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?

Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:10

Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga, koma Yehova anditola.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:16

Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:8

Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:3

Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 1:5

Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:5

Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:1

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 49:15-16

Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.

Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 10:30-31

komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 4:16

Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:18

Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:3

Chisomo kwa inu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:3

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 4:16

Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 3:26-27

Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Pakuti nonse amene munabatizidwa kwa Khristu mudavala Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:9

Yesu ananena naye, Kodi ndili ndi inu nthawi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikire, Filipo? Iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate?

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,

ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wokondedwa, ndinu wabwino ndi woona, wodabwitsa, wachifundo, ndikupemphani kuti mutitsogolere ndi kutilimbitsa pamaso panu. Ndipo kuti ine ndiyambe kuyandikira inu nthawi zonse ndi kukhala paubwenzi ndi inu. Mawu anu amati: “Monga atate achifundo pa ana awo, Chomwecho Yehova achifundo pa iwo akuopa Iye.” Ambuye, chitani chifuniro chanu pa moyo wanga ndipo mundithandize kusiya chilichonse chomwe si chanu. Ndikulengeza kuti moyo wanga ukuzungulira inu ndipo popanda inu sindingathe kuchita kalikonse, mundiphunzitse kumvera mawu anu ndikudziwa Mzimu wanu Woyera waulemerero. Munditeteze ku ziwembu zonse ndi machenjera a mdani. M'dzina la Yesu. Ameni.