Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 6:18 - Buku Lopatulika

18 ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 ndipo ndidzakhala kwa inu Atate, ndi inu mudzakhala kwa Ine ana aamuna ndi aakazi, anena Ambuye Wamphamvuyonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndipo “Ndidzakhala Atate anu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 6:18
21 Mawu Ofanana  

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo Yakobo anati kwa Yosefe, Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine pa Luzi m'dziko la Kanani nandidalitsa ine, nati kwa ine,


Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Ndidzakhala atate wake, ndi iye adzakhala mwana wanga; ndipo sindidzamchotsera chifundo changa monga muja ndinachotsera iye amene anakhala usanakhale iwe;


Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.


Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga akazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi;


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.


Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.


Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake;


Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu.


Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;


Pakuti inu nonse muli ana a Mulungu, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


Ndipo sindinaone Kachisi momwemo; pakuti Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, ndi Mwanawankhosa ndiwo Kachisi wake.


Iye wakupambana adzalandira izi; ndipo ndidzakhala Mulungu wake, ndi iye adzakhala mwana wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa