Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


55 Mau a M'Baibulo Okhudza Ulemu kwa Makolo

55 Mau a M'Baibulo Okhudza Ulemu kwa Makolo

Ndikufuna ndikuuzani nkhani ya ulemu kwa makolo athu. Nthawi zina timavutika kumvetsa tanthauzo lenileni la ulemu umenewu. Koma Mulungu, m’mawu ake opatulika, amatiuza kuti tiyenera kulemekeza ndi kuwayamikira makolo athu, mosasamala kanthu za msinkhu wawo kapena momwe amatikhalira.

Kulemekeza makolo athu ndi chizindikiro cha chikondi, ndipo chimabweretsa madalitso ambiri m'miyoyo yathu. Sikuti timachita izi chifukwa cha momwe makolo athu alili, koma chifukwa chomvera malamulo a Ambuye. Sikuti timayesa kuwerengera momwe tiyenera kuwachitira, koma timayesetsa kuwachitira ulemu tsiku ndi tsiku, kuti tikhalitse ndi moyo wautali komanso kuti tione chisomo ndi chikondi cha Mulungu m'miyoyo yathu.

Mulungu amatiuza kuti tilemekeze makolo athu. Kulemekeza kumeneku kumaphatikizapo kuwamvera, kutsatira uphungu wawo wanzeru, kuwamvetsera mwatcheru, ndi kulemekeza ulamuliro wawo. Baibulo limatipatsa malangizo omveka bwino okhudza momwe tiyenera kuchitira makolo athu. Musaiwale zimenezi!




Deuteronomo 5:16

Lemekeza atate wako ndi amai ako, monga Yehova Mulungu wako anakulamulira; kuti masiku ako achuluke, ndi kuti chikukomere, m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:19

Udziwa malamulo: Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wakunama, Usanyenge, Lemekeza atate wako ndi amai ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:22

Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amai ako atakalamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4

Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:32

Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8

Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:9

Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:26

Wolanda za atate, ndi wopirikitsa amai, ndiye mwana wochititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:3

Aliyense aope mai wake, ndi atate wake; nimusunge masabata anga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

Lemekeza atate wako ndi amai ako, ndipo, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:11-12

Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8-9

Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako; pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20

Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:4

Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-22

Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mai ako; uwamange pamtima pako osaleka; uwalunze pakhosi pako. Adzakutsogolera ulikuyenda, ndi kukudikira uli m'tulo, ndi kulankhula nawe utauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:20

Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:17

Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Taonani, ana ndiwo cholowa cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:17

Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:4-6

Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:5

Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:51

Ndipo anatsika nao pamodzi nadza ku Nazarete; nawamvera iwo: ndipo amake anasunga zinthu izi zonse mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:10

Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:5-7

Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao; Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera, kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula. Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake; koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda. Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema. Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele; kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao. ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu; napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi. Naperekanso anthu ake kwa lupanga; nakwiya nacho cholowa chake. Moto unapsereza anyamata ao; ndi anamwali ao sanalemekezeke. Ansembe ao anagwa ndi lupanga; ndipo amasiye ao sanachite maliro. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; nawapereka akhale otonzeka kosatha. Tero anakana hema wa Yosefe; ndipo sanasankhe fuko la Efuremu; koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. Ndipo anamanga malo oyera ake ngati kaphiri, monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha. Ndi kuti chiyembekezo chao chikhale kwa Mulungu, osaiwala zochita Mulungu, koma kusunga malamulo ake ndiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:17

Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:13

Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1-2

Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha; Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako. Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera. Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee. Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa. pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:2-3

Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:1-4

Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera. Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Taonani, m'mwemo adzadalitsika munthu wakuopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:4-5

kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:15

Munthu wakukantha atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:16

Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; aukali nagwiritsa chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu. Chikondano sichichitira mnzake choipa; chotero chikondanocho chili chokwanitsa lamulo. Ndipo chitani ichi, podziwa inu nyengo, kuti tsopano ndiyo nthawi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupirira. Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake. Kotero kuti iye amene atsutsana nao ulamuliro, akaniza choikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza, adzadzitengera kulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 21:18-21

Munthu akakhala naye mwana wamwamuna wopulukira, ndi wopikisana naye, wosamvera mau a atate wake, kapena mau a mai wake, wosawamvera angakhale anamlanga; azimgwira atate wake ndi mai wake, ndi kutulukira naye kwa akulu a mzinda wake, ndi ku chipata cha malo ake; pamenepo azituluka akulu anu ndi oweruza anu, nayese kumizinda yomzinga wophedwayo; ndipo anene kwa akulu a mzinda wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera. Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:27

Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1-2

Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika. Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale zako! Yesu wanga, ndikupempha undithandize kutsatira chitsanzo chako cha kumvera Atate, monga momwe iwe unachitira. Ndiphunzitseni kulemekeza ndi kuwachitira ulemu makolo anga, osawalankhula mwadyera kapena mwaukali. Ngati sindikuwalemekeza mwa kumvera, kukhala mwana wachikondi, kuwasamalira, ndi kuwateteza ngakhale atakalamba, andithandizeni. Mawu anu amati: “Lemekeza atate wako ndi amayi ako, monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira, kuti masiku ako akhale ataliatali, ndi kuti zinthu zikuyendere bwino m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.” Ambuye Yesu, ndithandizeni kuyenda m’mawu anu ndikukhala ndi moyo molingana ndi lonjezo limeneli, chifukwa ndikudziwa kuti kumvera kudzabweretsa madalitso anga. M’dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa