Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 20:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “ ‘Munthu aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. Magazi ake adzakhala pamutu pake chifukwa iye watemberera abambo kapena amayi ake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 20:9
17 Mawu Ofanana  

Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.


Munthu wakutemberera atate wake, kapena amai wake, aphedwe ndithu.


Wotemberera atate wake ndi amake, nyali yake idzazima mu mdima woti bii.


Pali mbadwo wotemberera atate ao, osadalitsa amai ao.


Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.


napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.


Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.


Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.


Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao.


Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu;


Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wake kapena mai wake. Ndi anthu onse anene, Amen.


Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.


kuti chiwawa adachitira ana aamuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa