Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

106 Mauthenga a Mulungu Pa Chuma

Ndikuganiza kuti dalitso la Mulungu ndi chuma ndi katundu basi, ndalakwitsa kwambiri. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu osauka sadalitsidwa ndi Mulungu, kapena kuti Mulungu sawakonda. Sizoona kuganiza kuti Mulungu amalanga ena ndi umphawi, pomwe ena amawadalitsa ndi chuma.

Mawu a Mulungu amatipatsa zitsanzo za anthu okhulupirika ndi omvera kwa Iye, koma anali osauka. Nthawi zina timaona kugwirizana pakati pa dalitso ndi chuma, koma zoona zake n’zakuti Mulungu amatidalitsa m’njira zambiri, ngakhale m’mavuto ndi zovuta.

Tiyenera kukhala oyamikira nthawi zonse, chifukwa Mulungu amaona mtima wathu. Ambiri, akakula m’chuma kapena akapambana, amatamanda Mulungu ndi kumuthokoza panthawiyo, koma chimwemwe chathu ndi ubwino wathu ziyenera kuchokera kwa Mulungu osati pa ndalama.


Miyambo 23:4-5

Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa.

Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:24

Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:1

Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 13:2

Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:2

Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:23-24

Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala.

Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 11:1

Ndalama zako uziike pa malonda okagulitsa kutsidya kwa nyanja, ndipo udzapeza phindu patapita masiku ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 24:35

Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 20:17

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 15:5

Ndi amene sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja, amene salandira chiphuphu kuti azunze munthu wosalakwa. Munthu wochita zimenezi, palibe chilichonse chimene chidzamgwedeze.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 8:17-18

Tsono muchenjere, musamati, “Ndapeza chuma chonsechi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga.”

Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:12

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:47-48

Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe.

Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Samueli 2:7

Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 3:13

Kuwonjezera pamenepo, ndikukupatsanso zimene sudapemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti palibe mfumu imene idzalingane nawe pa masiku onse a moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 10:23

Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 10:27

Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:12

Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mbiri 29:16

Inu Chauta, Mulungu wathu, inde tapereka mphatso zimenezi kuti akumangireni nyumba, koma zonsezi zikuchokera m'manja mwanu ndipo nzanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 1:11-12

Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino

nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 9:22

Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 32:27-29

Hezekiya anali wolemera kwambiri ndiponso waulemu zedi. Tsono adadzimangira nyumba zomasungiramo chuma cha siliva, golide, miyala yamtengowapatali, zonunkhira, zishango ndiponso mitundu yonse ya ziŵiya zamtengowapatali.

Adamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo ndi mafuta. Adamanga makola a mitundu yonse ya ziŵeto zosiyanasiyana ndi makola a nkhosa.

Komanso adamanga mizinda yake, ndipo anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri, pakuti Mulungu adaamlemeza kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 1:1-3

Kudaali munthu wina, dzina lake Yobe, amene ankakhala m'dziko la Uzi. Munthu ameneyo anali wosalakwa ndiponso wolungama. Ankaopa Mulungu namapewa zoipa.

Suja Inu mwakhala mukumteteza ponseponse iye uja, pamodzi ndi banja lake ndi zinthu zake zonse zimene ali nazo. Mudamdalitsanso pa ntchito zimene amachita, ndipo chuma chake nchochuluka kwambiri m'dzikomo.

Koma tsopano tangoyesani kumchotsera zonse zimene ali nazo, muwona, adzakutukwanirani pamaso.”

Chauta adauza Satana kuti, “Chabwino, zonse zimene Yobe ali nazo ndaziika m'manja mwako. Koma iye yekhayo usamkhudze.” Pamenepo Satanayo adachoka, kumsiya Chauta.

Tsiku lina ana aamuna ndi ana aakazi a Yobe ankachita phwando m'nyumba mwa mkulu wao.

Ndiye kudafika wamthenga kwa Yobe kudzamuuza kuti, “Ng'ombe zinalikulima, ndipo abulu analikudya pafupi pomwepo.

Mwadzidzidzi nkubwera Aseba kudzatithira nkhondo nalanda ng'ombezo ndi abulu omwe. Ndipo apha antchito onse, koma ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

Iyeyo akulankhulabe, padafikanso wina, nati, “Kunagwa mphezi ndipo yapsereza nkhosa zonse pamodzi ndi abusa omwe, onse psiti. Ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”

Ameneyu asanatsirize kulankhula, padafikanso wina, nati, “Kunafika magulu atatu a Akaldeya kudzatithira nkhondo. Atilanda ngamira zonse, ndipo apha antchito onse. Ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”

Iyeyo mau akali m'kamwa, padafikanso wina, nati, “Ana anu onse anali pa phwando m'nyumba ya mkulu wao.

Mwadzidzidzi chayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nkudzaomba nyumbayo mbali zonse. Motero yagwa ndi kuŵapsinja anawo. Onse aphedwa, ndapulumukapo ndine ndekha kuti ndidzakuuzeni.”

Anali ndi ana aamuna asanu ndi aŵiri, ndi ana aakazi atatu.

Yobe atamva zimenezo, adadzambatuka, nkung'amba zovala zake. Adameta tsitsi, ndipo adadzigwetsa pansi napembedza Mulungu.

Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”

Ngakhale zidaayenda motero, Yobe sadachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.”

Anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ng'ombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500. Anali ndi antchito ambiri, choncho anali munthu wotchuka koposa anthu onse a m'maiko akuvuma.

Mutu    |  Mabaibulo
Yobu 42:10

Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 49:6-7

Anthu otero amangokhulupirira chuma chao, amanyada chifukwa ali ndi chuma chambiri.

Zoonadi, palibe munthu amene angadziwombole, kapena kupatsa Mulungu mtengo wa moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 49:16-17

Usavutike munthu wina akamalemera, pamene chuma cha m'nyumba mwake chikukulirakulira.

Chifukwa pamene munthuyu amwalira, sadzatengapo kanthu. Chuma chake sichidzapita naye limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 52:7

“Muwoneni munthu amene sadafune kudalira Mulungu, koma adakhulupirira chuma chake chochuluka, nalimbikira kuchita zoipa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 112:3

Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera, ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:14

Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 127:1-2

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe.

Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:13-14

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 8:18

Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:22

Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:4

Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 13:11

Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:6

Munthu wochita chilungamo amakhala ndi chuma chambiri, koma zimene woipa amapindula zimamgwetsa m'mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:11

Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali limene amayesa ndi lomutchinjiriza.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:17

Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 22:1-2

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mukampirikitsa wonyoza, kukangana kudzatha, ndipo ndeu ndi zonyoza zidzalekeka.

Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kulankhula zabwino, adzakhala bwenzi la mfumu.

Chauta amayang'anira bwino anthu odziŵa zinthu, koma mau a anthu osakhulupirika, Iye amaŵalepheretsa.

Waulesi amati, “Pali mkango pabwalopo! Ndikaphedwa m'miseu.”

Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lakuya. Amene Chauta amamkwiyira adzagwamo.

Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.

Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.

Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.

Chidzakhala chokondwetsa ukazisunga, ndi kukhala wokonzeka kumazilankhula pa nthaŵi yake.

Ndakudziŵitsa zimenezi lero kuti makamaka iweyo uzikhulupirira Chauta.

Wolemera ndi wosauka akulingana, pakuti onsewo adaŵalenga ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 27:24

Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse?

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 5:10

Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 5:19

Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mlaliki 6:2

Mulungu kukulemeretsa, kukupatsa chuma ndi ulemu, osasoŵa kanthu kalikonse kamene ukukalakalaka, koma tsono osakupatsa mwai woti udyerere zinthuzo, wodyerera nkukhala munthu wachilendo. Zimenezi nzothetsa nzeru, ndipo ndi vuto lokhumudwitsa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:7

Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide, ndipo chuma chao nchosatha. Dziko lao nlodzaza ndi akavalo, ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 30:23

Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 60:5

Udzaona zimenezi, ndipo udzakondwa, mtima wako udzalumpha ndi chimwemwe. Chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe. Chuma cha maiko onse chidzabwera kwa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 9:23

Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:11

Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 28:4-5

Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa pokupatsa chuma cha golide ndi siliva.

Udachulukitsa chuma chako chifukwa cha nzeru zako zoyendetsera malonda, ndipo ukunyada chifukwa cha chuma chakocho.

Mutu    |  Mabaibulo
Hoseya 12:8

Aefuremu akunena kuti, ‘Ndithu talemera, takhuphuka zedi, wina sangatiloze chala pa kulemera kumeneku.’

Mutu    |  Mabaibulo
Nahumu 2:9

Funkhani siliva! Funkhani golide! Chuma chake nchosatha, za mtengo wapatali nzosaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo
Hagai 2:8

Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 9:3

Tiro adadzimangira linga. Adaunjika siliva ngati dothi, adakundika golide ngati chifwilimbwiti cham'miseu.

Mutu    |  Mabaibulo
Malaki 3:10

Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.

“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.

Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 13:22

Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 16:26

Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:21-22

Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:23-24

Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba.

Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 25:14-30

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake.

Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo.

Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu.

Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri.

Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija.

“Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija.

Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera.

Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’

Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’

Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

“Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu.

Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’

Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu?

Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake.

Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo.

Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera.

Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 4:19

Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 10:21-22

Yesu atamuyang'ana, adamkonda nkumuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Atamva zimenezo, munthu uja nkhope yake idagwa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa adaali munthu wa chuma chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 10:23-25

Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Ophunzirawo adadabwa nawo kwambiri mau akeŵa. Koma Yesu adabwerezanso, adati, “Ndithu, inu ana anga, nkwapatali kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu.

Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wachuma akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 6:24

“Koma ndinu atsoka, anthu achumanu, chifukwa mwalandiriratu zokusangalatsani.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 8:14

Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:15-21

Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Tsono Yesu adaŵaphera fanizo. Adati, “Munthu wina wachuma m'munda mwake mudabereka dzinthu dzambiri.

Ndiye iye uja adayamba kuganiza kuti, ‘Nditani, poti ndilibe mosungira dzinthu dzanga?’

Tsono adati, ‘Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga nkumanga zina zazikulu, ndipo ndidzasungira dzinthu dzanja dzonse ndi chuma changa m'menemo.

Kenaka ndidzauza mtima wanga kuti, Iwe mtima wanga, uli ndi chuma chambiri chimene chidzakukwanira zaka zambiri. Upumule, uzidya, uzimwa ndi kusangalala!’

Kanthu kalikonse kovundikirika kadzaululuka, ndipo kalikonse kobisika kadzadziŵika.

Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘Wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?’ ”

Potsiriza Yesu adati, “Zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:33-34

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge.

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 16:13

“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 18:22-23

Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 18:24-25

Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.

Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 3:27

Yohane adati, “Munthu sangalandire kanthu kalikonse ngati Mulungu sampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 6:27

Musamagwira ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimaonongeka, koma muzigwira ntchito kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chili cha moyo wosatha. Mwana wa Munthu ndiye adzakupatsani chakudya chimenechi, pakuti Mulungu Atate adamuvomereza motsimikiza.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 12:5-6

“Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?”

Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”

Adaatero osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala. Iye ankasunga thumba la ndalama, nkumabamo.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 2:45

Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 4:34-35

Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi.

Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:4

Kodi kapena ukupeputsa chifundo chachikulu cha Mulungu, kuleza mtima kwake, ndi kupirira kwake? Kodi sukudziŵa kuti Mulungu akukuchitira chifundo chifukwa afuna kuti utembenuke mtima?

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 11:33

Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:5

Zoonadi mwa Khristu mwakhala anthu olemera pa zonse, makamaka pa kulankhula ndi pa kudziŵa zinthu,

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 4:7-8

Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?

Ndiye kuti muli nazo kale zonse zimene mumasoŵa! Ndiye kuti mwalemera kale! Ndiye kuti mwasanduka mafumu popanda ife! Ndikadakondwera mukadakhaladi mafumu, kuti ifenso tikhale mafumu pamodzi nanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:26

Paja Malembo akuti, “Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 8:2

Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 8:9

Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:6-8

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.

Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 9:10-11

Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.

Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 1:7-8

Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere

zimene Mulungu adatipatsa mochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 3:8

Pakati pa anthu onse a Mulungu ine ndine wamng'ono koposa, komabe Mulungu adandipatsa ineyo ntchito iyi, yakuti ndilalikire anthu a mitundu ina za chuma chopanda malire, chimene Mulungu amatipatsa mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:27

Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 6:17-19

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.

Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.

Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo
Tito 3:6-7

Mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu, Mulungu adatipatsa Mzimu Woyerayo moolowa manja.

Adachita zimenezi, kuti mwa kukoma mtima kwake tisanduke olungama pamaso pake, ndipo tikalandire moyo wosatha umene tikuuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:34

Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:10-11

Ndipo mbale wolemera nayenso anyadire pamene Mulungu amtsitsa, pakuti adzatha ngati duŵa la udzu.

Dzuŵa limatuluka nkutentha kwake, ndipo limaumitsa udzu. Duŵa la udzuwo limathothoka, kukongola kwake nkutha. Chomwechonso moyo wa wolemerayo udzazimirira ali pakati pa zochita zake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 5:1-3

Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani.

Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira.

Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima.

Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula.

Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.

Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.

Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.

Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.

Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake.

Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza,

Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu.

dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.

Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:17-18

Paja inu mumati, ‘Ndife olemera, ndife achuma, sitisoŵa kanthu;’ osadziŵa kuti ndinu ovutika, ochititsa chifundo, amphaŵi, akhungu ndi amaliseche.

Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, landirani ulemu ndi chiyamiko chonse, inu woyera, wamuyaya, wosayananitsidwa. Ndimakulambirani chifukwa ndinu woyenera, wokhulupirika, ndi chuma changa chapadera. Atate Woyera, ndikubwerera kwa inu podziwa kuti ndinu nokha gwero la zinthu zonse ndi wopatsa mphamvu yopezera chuma. Ndikupemphani kuti mundipatse nzeru zoyendetsera bwino ndalama zanga, munditeteze kuti ndisagonjetsedwe nazo, mundithandize kuzindikira kuti sindiyenera kulamulidwa ndi ndalama, koma ndi chithandizo cha Mzimu Woyera wanu, ndikhale ine wolamulira ndalama, kuti ndibweretse mtendere m'moyo mwanga ndi m'banja langa. Atate, ndithandizeni kumvetsa kuti ndinu Mulungu wachipembedzo, amene simugawana ulemu wanu ndi wina aliyense ndipo munandilenga kuti ndikukondeni ndi kukulambirani inu nokha. Mawu anu amati: "Mumatani kugulira chakudya chosakhala mkate, ndi kugwira ntchito yanu yosakhuta? Mundimvere tsopano, mudzadya zabwino, ndipo moyo wanu udzakondwera ndi mafuta." Ndithandizeni kukhala ndi mtima wodzichepetsa ndi wodalira inu, kuti ndizitha kuyamikira nthawi zonse kaya ndili ndi zambiri kapena zochepa, komanso kukhala ndi mtima wopatsa ena. Mundipatse mphamvu yogwira mwamphamvu kukhalapo kwanu kwaulemerero, pakuti ndinu chitsimikizo cha chipambano changa ndi kukhala woyang'anira bwino ndalama zanga. M'dzina la Yesu. Ameni.