Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mauthenga a Mulungu Okhudza Golide

104 Mauthenga a Mulungu Okhudza Golide

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, taganizirani za golide. Limayikidwa pamoto wamphamvu kuti lisungunuke, kuchotsa zoipa zonse. Koma motowo suyenera kukhala wamphamvu kwambiri moti ungawononge golidelo. Kenako, limakhomeredwa ndi nyundo, pang'onopang'ono, mpaka litakhala lokongola komanso lowala.

M'buku la Yobu 23:10, Baibulo limati: "Koma Iye adziwa njira yanga; Nditayesedwa ndidzatuluka ngati golide." Nthawi zina zimakhala zovuta kumvetsa, koma ifenso tili ngati golidelo. Pali zinthu m'miyoyo yathu zomwe ziyenera "kuwotchedwa" pamoto, kuti kuwala kwa Mulungu komwe kuli mkati mwathu kuwonekere. Sikuti tiyenera kudzitukumula, koma tiziwala chifukwa cha ubwino wa Mulungu.




Masalimo 119:127

Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:32

Pa zitseko ziŵiri zija za mtengo wa olivi adazokotapo zithunzi za akerubi, za mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa. Tsono zitsekozo adazikuta ndi golide, ndipo adapaka golide pa akerubiwo ndi pa mitengo ya mgwalangwa ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:10

Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:12

Anthu ndidzaŵasandutsa osapezekapezeka kuposanso m'mene aliri golide wangwiro, mtundu wa anthu udzakhala wosoŵa ngati golide wa ku Ofiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:24

Tsono ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo pozungulira pake ponse upange mkombero wagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:11-12

Mtsinje woyamba ndi Pisoni, ndipo umayenda mozungulira dziko la Havila, kumene kumapezeka golide. (Golide wakumeneko ndi wabwino. Kumapezekanso bedeliyo ndi miyala ya mtengowapatali yotchedwa onikisi.)

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:8

Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 13:2

Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:3

Siliva amamuyesera m'chitofu, golide amamuyesera m'ng'anjo, koma mitima amaiyesa ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:22

Namwali uja atamaliza kumwetsa ngamirazo, munthuyo adatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli, naveka Rebeka pamphuno pake. Adamuvekanso pamikono pake zigwinjiri ziŵiri zolemera masekeli agolide okwana 100.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:18

Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:21

Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 4:1

Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri. Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu. Miyala ya ku malo oyera yamwazikana, ili vuu, ku mphambano zonse za miseu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:53

Kenaka adatulutsa zinthu zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi zovala, napatsa Rebeka. Adaperekanso mphatso zamtengowapatali kwa mlongo wake wa Rebekayo ndi kwa mai wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 3:22

Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 11:2

Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:35-36

Ndiponso Aisraele anali atachita monga momwe Mose adaaŵauzira. Adaapempha kwa Aejipitowo zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Chauta adasandutsa Aejipito aja kuti akhale okoma mtima, ndipo anthuwo adapatsa Aisraele zonse zimene ankapempha. Motero Aisraele adalandako chuma cha Aejipito aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:3

Zopereka zimene ulandirezo ndi izi: golide, siliva, mkuŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:11

Ulikute ndi golide wabwino kwambiri m'kati mwake ndi kunja komwe. Upange mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:17-18

“Upange ndi golide wabwino kwambiri chivundikiro cha bokosi, kutalika kwake masentimita 114, kupingasa kwake masentimita 69. Pa mbali ziŵiri za chivundikirocho, m'mphepete mwake, upange akerubi aŵiri, agolide, osula ndi nyundo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:36

“Upangenso duŵa la golide wabwino kwambiri, ulembepo mozokota mau akuti, ‘Choperekedwa kwa Chauta.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:2-4

Tsono Aroni adauza anthuwo kuti, “Vulani nsapule zagolide kukhutu kwa akazi anu, kwa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi omwe, ndipo mubwere nazo kwa ine.” Pomwepo adakatenga mwanawang'ombe amene Aroni adapanga, namperapera ngati ufa, ndipo adakamtaya m'madzi. Tsono Aisraele aja adaŵamwetsa madziwo. Kenaka Mose adafunsa Aroni uja kuti, “Kodi anthu ameneŵa adakuchita zotani iwe, kuti uŵachimwitse koopsa chotere?” Aroni adayankha kuti, “Musakwiyire ine mbuyanga. Mumaŵadziŵa anthu ameneŵa kuti ngovuta. Iwoŵa adandiwuza kuti, ‘Tipangireni milungu yoti ititsogolere ife, chifukwa sitikudziŵa chomwe chamgwera Mose, amene adatitsogolera potitulutsa ku Ejipito.’ Tsono ine ndidaŵauza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi golide abwere naye.’ Ndipo amene anali nazo zinthu zopangidwa ndi golide adandipatsa. Ndidaziponya pa moto, ndipo ndidapanga fano la mwanawang'ombe lija.” Mose adaonadi kuti anthuwo ngosokonezeka, (chifukwa Aroni adaaŵalekerera, mpaka iwo kusanduka anthu oŵanyodola pakati pa adani ao). Moseyo adaimirira pa chipata cha mahema aja ndipo adafuula mokweza nafunsa kuti, “Kodi ndani akufuna Chauta? Bwerani kuno.” Pompo Alevi onse adadzasonkhana kwa iye, ndipo Mose adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Aliyense mwa inu atenge lupanga, ndipo mupite ku mahema ndi kuloŵa m'zipata zonse. Aliyense mwa inu akaphe mbale wake kapena bwenzi lake kapena mnansi.’ ” Aleviwo adachitadi monga momwe Mose adaŵalamulira, ndipo amuna 3,000 adaphedwa pa tsiku limenelo. Apo Mose adauza Aleviwo kuti, “Lero lino mwadzipatula nokha kuti mukhale ansembe otumikira Chauta, pakupha ana anu ndi abale anu omwe. Motero Chauta akudalitsani lero.” Anthuwo adavuladi nsapule zao, ndipo adabwera nazo kwa Aroni. M'maŵa mwake Mose adauza anthu kuti, “Inu mudachimwa koopsa. Koma tsopano ndidzapita kwa Chauta ku phiri, ndipo nditakupemphererani, kapena angathe kukukhululukirani machimo anu.” Tsono Mose adabwerera kwa Chauta nakanena kuti, “Anthu aŵa adachimwa koopsa. Adadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, chonde muŵakhululukire machimo ao. Mukapanda kuŵakhululukira, chonde mufafanize dzina langa m'buku m'mene mudalemba.” Apo Chauta adauza Mose kuti, “Yekhayo amene wandilakwira Ine, ndiye amene ndidzachotse dzina lake m'buku langa. Tsopano pita uŵatsogolere anthuwo ku malo amene ndidakuuza. Kumbukira kuti mngelo wanga adzakutsogolera, koma tsiku likubwera limene ndidzaŵalange iwowo chifukwa cha machimo ao.” Motero Chauta adatumiza nthenda pa anthuwo, chifukwa choti adakakamiza Aroni kuti aŵapangire fano la mwanawang'ombe. Tsono Aroni adalandira golideyo kumanja kwa anthuwo, ndipo adamsungunula, napanga fano la mwanawang'ombe m'chikombole. Ndipo anthu adayamba kufuula kuti, “Inu Aisraele, nayi milungu yanu imene idakutulutsani ku Ejipito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:2

Tsono lonselo adalikuta ndi golide m'kati mwake ndi kunja komwe, ndipo adalemba mkombero wagolide kuzungulira bokosi lonselo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:6

Kenaka adapanga chivundikiro cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, muufupi wake masentimita 69.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:16

Adapanganso ziŵiya za golide wabwino kwambiri za pa tebulolo, monga mbale, zikho, mitsuko ndi mabeseni ogwiritsira ntchito pa zopereka zamadzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:23-24

Ndipo adapanga nyale zisanu ndi ziŵiri za pa choikaponyalecho, napanganso mbanira ndiponso zoolera phulusa za golide wabwino kwambiri. Popanga choikaponyalecho, pamodzi ndi zipangizo zake zonsezo, adagwiritsa ntchito makilogaramu 34 a golide wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:9

Ndipo adamuveka nduŵira kumutu. Kumaso kwa nduŵirayo adaikako mphande yagolide, chizindikiro chopatulira, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 7:14

Adaperekanso kambale kamodzi kagolide kolemera magaramu 110, kodzaza ndi lubani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 31:50-51

Ndipo ife tabwera ndi zopereka kwa Chauta zimene munthu aliyense adapeza, monga golide, zibangiri, zikono, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda, kuti achitire mwambo wopepesera machimo athu pamaso pa Chauta.” Apo Mose ndi wansembe Eleazara adalandira golide kwa atsogoleriwo, pamodzi ndi zinthu zonse zosula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:13

mukadzakhala ndi ng'ombe, nkhosa, siliva ndi golide, ndipo chuma chanu chikadzanka chiwonjezekeraonjezekera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:17

Mfumu isadzakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake ungadzapotoke. Ndipo isadzadzikundikire siliva ndi golide wambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 6:19

Koma zonse zasiliva ndi zagolide, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi zachitsulo zikhale zopatulika za Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 7:21

pakati pa chuma chija, ndidaonapo mwinjiro wokongola wa ku Babiloni, ndi makilogramu aŵiri a siliva ndiponso munsi wa golide wolemera theka la kilogramu. Zonsezi ndidaazikhumba kwambiri, kotero kuti ndidatenga ndithu. Mungathe kuzipeza m'chithando changa m'mene ndidazibisa. Mukapezanso silivayo pansi pa zinthu zinazo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 8:24-26

Gideoni adaŵauzanso kuti, “Ndikupempheni kanthu kamodzi. Aliyense mwa inu andipatse ndolo zimene adafunkha.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide chifukwa chakuti anali Aismaele). Iwo adayankha kuti, “Tikuvomera kukupatsani zimenezi.” Apo adayala chovala, ndipo munthu aliyense adaponyapo ndolo zofunkhazo. Kulemera kwake kwa ndolo zagolide zimene anthu adaperekazo kunali makilogramu 20, osaŵerengera kulemera kwa mphande, ukufu wam'khosi, zovala zofiira za mafumu a Midiyani, ndiponso malamba am'khosi a ngamira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 6:8

Tsono mutenge Bokosi lachipanganolo, muliike pa galeta, ndipo pambali pake muikepo bokosi la zinthu zagolide zija zimene mukutumiza kwa Chauta, kuti zikhale nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake muzitaye ng'ombezo ndipo galeta lizipita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 8:7

Davide adatenga zishango zagolide zimene anyamata a Hadadezere ankanyamula, nabwera nazo ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:20-22

Chinali cha mamita asanu ndi anai ponseponse, m'litali mwake, m'mimba mwake ndiponso mumsinkhu mwake. Ndipo adachikuta ndi golide weniweni. Adapanganso guwa lansembe la matabwa amkungudza. Tsono Solomoni adakuta golide weniweni m'kati mwake mwa Nyumbayo, ndipo adalambalika maunyolo agolide mopingasitsa kutsogolo kwa chipinda chopatulika cham'kati naŵakuta ndi golide. Chipinda chimenechinso chidakutidwa ndi golide. Motero adaikuta Nyumba yonseyo ndi golide mpaka idatha. Guwa lansembe la m'chipinda chopatulika nalonso adalikuta ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:30

Kenaka adayalanso golide pansi m'Nyumbamo m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 7:48-50

Solomoni adapangitsanso ziŵiya zimene zinali m'Nyumba ya Chauta: ndiye kuti guwa lagolide, tebulo lagolide la buledi woperekedwa kwa Mulungu, zoikaponyale za golide weniweni, kumwera zisanu, kumpoto zisanu, m'kati mwenimweni mwa malo opatulika. Adapangitsa maluŵa, nyale ndi mbano, zonse zagolide. Ndipo makomo onse ndi mawindo omwe, mafuremu ake anali olingana monsemonse, m'litali mwake ndi m'mimba mwake, ndipo windo linkapenyana ndi windo linzake pa mizere itatu. Adapangitsanso zikho, zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani, ndiponso ziwaya zopalira moto, zonse za golide weniweni. Ndipo adapangitsa ndi golide zomangira zitseko za chipinda cham'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 9:28

Tsono amalinyerowo adapita ku Ofiri, ndipo adakatengako golide wokwanira makilogramu 14,000, nabwera naye kwa mfumu Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:2

Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:10-11

Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zokometsera chakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yamtengowapatali. Sikudafikenso konse zokometsera zakudya zochuluka chotere zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni. Zombo za mfumu Hiramu nazonso zidabwera ndi golide wa ku Ofiri. Zidatenganso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:14-18

Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000, osaŵerengera amene ankabwera ndi alendo ndi anthu amalonda, ndiponso wina wochokera kwa mafumu onse a ku Arabiya, ndi kwa nduna zam'dzikomo. Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu asanu ndi awiri. Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira kilogramu limodzi ndi theka. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu, niwukuta ndi golide wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:21-22

Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni. Mfumu inali ndi zombo zochokera ku Tarisisi zimene zinkayenda pa nyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu; ndipo chaka chachitatu chilichonse zinkabwera zitanyamula golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 12:28

Motero mfumuyo itaganizaganiza pa zimenezi, idapanga mafano aŵiri a anaang'ombe agolide. Tsono idauza anthu kuti, “Inu anthu a ku Israele, ku Yerusalemu mwakhala mukupitako nthaŵi yaitali. Tsopano milungu yanu ndi iyi imene idakutulutsani ku dziko la Ejipito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:2-7

Choncho ndidapereka za ku Nyumba ya Chauta wanga monga m'mene ndidathera, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuŵa wopangira zinthu zamkuŵa, chitsulo chopangira zinthu zazitsulo ndi mitengo yopangira zinthu zamtengo. Ndidaperekanso miyala yochuluka yomangira, ya mtundu wa onikisi, miyala ya maŵangamaŵanga, miyala yambiri yamitundumitundu yamtengowapatali ndiponso miyala ya marabulo. Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu. M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse. Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe. Tsono Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Chauta nakhala mfumu m'malo mwa Davide atate ake. Zinthu zinkamuyendera bwino, ndipo Aisraele onse ankamumvera. Atsogoleri onse, ankhondo ndi ana a mfumu Davide omwe, onsewo adadzipereka kwa mfumu Solomoni. Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe. Umu ndimo m'mene Davide, mwana wa Yese, adalamulira Aisraele onse. Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33. Tsono adamwalira atafika pokalamba zedi. Masiku ake adachuluka, pamodzi ndi chuma ndi ulemerero wake. Ndipo Solomoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono ntchito za mfumu Davide kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza pake, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Samuele, m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la mbiri ya mneneri Gadi. Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga. M'menemo adasimba za kulamulira kwake, za mphamvu zake ndiponso za zonse zimene zidamuwonekera iyeyo, mpakanso zimene zidaonekera fuko la Israele ndiponso zimene zidaonekera maiko ena ozungulira. Ndikupereka matani a golide 100, golide wake wabwino kwambiri wa ku Ofiri, ndi matani a siliva wosalala 240. Zonsezo zidzakhala zokutira makoma a Nyumba, ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?” Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu. Zimene adapereka ku ntchito ya Nyumba ya Chauta ndi izi: matani 170 a golide, makilogramu 84 a ndalama zagolide za mtundu wina, matani 340 a siliva, matani pafupifupi 620 a mkuŵa, ndipo matani oposa 3,400 a chitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:15

Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 3:4-6

Chipinda chapoloŵera, m'litali mwake chinali cha mamita asanu ndi anai, kulingana ndi m'mimba mwake mwa nyumbayo. Msinkhu wake unali wa mamita 54. Nyumbayo m'kati mwake adaikuta ndi golide weniweni. Chipinda chachikulucho adachichinga ndi matabwa amlombwa, nachikuta ndi golide wosalala, ndipo pamakoma adalochapo zithunzi za kanjedza ndi za maunyolo. Adaikometsa nyumbayo ndi miyala yamtengowapatali. Golide wake anali wa ku Paravaimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 4:20-22

Zoikaponyale pamodzi ndi nyale zake za golide weniweni, kuti ziziyaka m'kati mwenimweni mwa malo opatulika, monga kudaalembedwera. Adapangitsa maluŵa, nyale ndiponso mbano za golide weniweni. Zozimira nyale, mabeseni, mbale zofukiziramo lubani ndiponso ziwaya zopalira moto, zonsezi za golide weniweni. Ndipo adapangitsa zomangira zitseko za Nyumba ya Chauta ija, zitseko zam'kati zoloŵera ku malo opatulika kopambana, ndiponso zitseko zoloŵera m'Nyumba ya Chauta, zonsezo zinali zagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 9:9

Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zonunkhira zambirimbiri ndiponso miyala yamtengowapatali. Nkale lonse sikudaoneke zokometsera chakudya zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 9:13-17

Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000, osaŵerengera amene ankabwera ndi anthu amalonda. Mafumu onse a ku Arabiya pamodzi ndi nduna zam'dzikomo ankabwera ndi siliva ndi golide kwa Solomoni. Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu pafupi asanu ndi aŵiri. Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira makilogramu atatu. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu niwukuta ndi golide weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 24:14

Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva. Anthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 1:4

Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:25-27

Ndipo ndidaŵayesera siliva ndi golide, ndiponso ziŵiya ndi zopereka za ku Nyumba ya Mulungu wathu zimene mfumu ndi aphungu ake ndi akalonga ake ndi Aisraele onse amene anali kumeneko, adaazipereka. Nditaziyesa zonse, ndidaŵapatsa m'manja mwao siliva wa matani 22, ziŵiya zasiliva za makilogaramu 70, ndiponso golide wa makilogaramu 3,400, mbale zagolide makumi aŵiri zolemera makilogaramu pafupi 8 ndi theka, ndiponso ziŵiya ziŵiri za mkuŵa wosalala wonyezemira bwino, zamtengowapatali wonga wa golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 7:70-71

Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530. Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 22:24-25

Golide wako yense umuyese wachabechabe, ndithu, chuma chamtengowapatali uchiwone ngati dothi, Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 28:15-19

Nzeru sangazipate ndi golide, mtengo wake sangauyerekeze ndi siliva wambiri. Ngakhale golide wokoma kwambiri wa ku Ofiri sangafike pa mtengo wa nzeruzo, miyala ya onikisi kapena ya safiro nayonso singafikepo. Golide ndi mwala wagalasi sizingakwanire kuti agulire nzeru. Nzeru sangazisinthanitse ndi zokometsera za golide weniweni. Mtengo wake wa nzeru ndi woposa miyala ya korali ndi krisitala, umapambananso ndi miyala ya rubi yomwe. Mtengo wake wa nzeru umapambana ndi ngale zomwe. Miyala ya topazi ya ku Etiopiya sungaiyerekeze ndi nzeru, ngakhale golide wabwino kwambiri sangafikepo pa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:9

ana aakazi a mafumu ali m'gulu la mbumba zanu zolemekezeka. Ku dzanja lanu lamanja kwaima mfumukazi, yovala zovala za golide wa ku Ofiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:13

“Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:14-15

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:10

Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:19

Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:12

Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:8

Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 1:11

Tidzakupangira ukufu wagolide, wokhala ndi timakaka tasiliva. Mkazi

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:7

Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide, ndipo chuma chao nchosatha. Dziko lao nlodzaza ndi akavalo, ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:20

Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:9

Zimenezo ndi zombo zochokera ku maiko akutali, za ku Tarisisi zili patsogolo. Zikudzatula ana anu amene atenga siliva ndi golide, kuti alemekeze dzina la Chauta, Mulungu wanu, Woyera uja wa Israele, chifukwa Iyeyo adakupatsani ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:17

“Ndidzakupatsa golide m'malo mwa mkuŵa, m'malo mwa chitsulo ndidzakupatsa siliva, mkuŵa m'malo mwa mtengo, chitsulo m'malo mwa mwala. Okuyang'anira ndidzaŵasandutsa amtendere, okulamulira ndidzaŵasandutsa olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:9

Siliva wosula wokutira mafanowo ndi wochokera ku Tarisisi, ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi. Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi anthu odziŵa kuzokota golide. Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira. Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:7

Pajatu Babiloni anali ngati chikho chagolide m'manja mwa Chauta, kuti aledzeretse dziko lonse lapansi. Mitundu yambiri ya anthu idamwako vinyo wake, nchifukwa chake idapenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 4:1-2

Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri. Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu. Miyala ya ku malo oyera yamwazikana, ili vuu, ku mphambano zonse za miseu. Ngakhale akazi achifundo ndi manja ao omwe adafika pophika ana ao. Ana aowo adasanduka chakudya chao pa nthaŵi imene anthu anga adaonongedwa. Chauta adakwiya kwambiri, nagwetsa pansi mkwiyo wake wamotowo. Adayatsa moto ku Ziyoni ndipo motowo udaononga maziko a mzindawo. Mafumu a pa dziko lapansi sadakhulupirire, kapena wina aliyense wokhala pa dziko lapansi, kuti adani kapena ankhondo nkuloŵa pa zipata za Yerusalemu. Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi ntchito zoipa za ansembe ake, amene ankakhetsa magazi a anthu osalakwa m'malinga amumzindamu. Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu, zovala zao zili magazi psu, mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza. Anthu ankaŵafuulira kuti, “Chokani, inu anthu oipitsidwa. Chokani! Chokani apa! Musakhudzane ndi ife!” Motero adathaŵa, namangoyendayenda, anthu a mitundu ina ankati, “Asadzakhalenso ndi ife.” Chauta mwiniwake ndiye adaŵamwaza, salabadakonso za iwo. Ansembe sadaŵalemekezenso. Akuluakulu sadaŵamvere chifundo. Maso athu adatopa nkuyang'anira chithandizo, koma popanda phindu. Tidadikiradikira mtundu wina wa anthu amene sangathe kutipulumutsa. Anthu ankangotilondola nthaŵi zonse, kotero kuti sitinkathanso kuyenda m'miseu yathu. Masiku athu ankacheperachepera, imfa yathu idaayandikira, ndithu chimalizo chinali chitafika. Anthu otilondolawo anali aliŵiro kupambana adembo ouluka mu mlengalenga. Adatipirikitsa ku mapiri, adatilalira ku chipululu kuti atiphe. Onani ana okondedwa a m'Ziyoni amene kale anali ngati golide kwa ife, tsopano akuŵayesa mbiya zadothi zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:13

Motero udavaladi zokongoletsa zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za bafuta wosalala, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta a olivi. Udakula mokongola zedi, ndipo udasanduka mfumukazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:17

Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 2:8

Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:5

Inu mudatenga siliva ndi golide wanga ndi zinthu zanga zina zamtengowapatali, kupita nazo ku nyumba za milungu yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 8:6

kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 2:9

Funkhani siliva! Funkhani golide! Chuma chake nchosatha, za mtengo wapatali nzosaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 13:9

Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:3

Adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri wapang'anjo woyeretsa siliva, ndipo adzayeretsa Alevi monga amayeretsera golide ndi siliva, mpaka kuti azidzapereka nsembe zoyenera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:11

Adaloŵa m'nyumba, naona mwanayo ali ndi Maria mai wake, ndipo adagwada nampembedza. Kenaka adamasula chuma chao, nampatsa mitulo ya golide, lubani ndi mafuta onunkhira a mure.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:16-17

“Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’ Inu anthu opusa ndi akhungu! Chachikulu nchiti, chuma chija, kapena Nyumba imene ikusandutsa chumacho kuti chikhale chopatulika?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:19

Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa lansembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6

Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:29

“Tsono popeza kuti tili ngati ana a Mulungu, sitiyenera kuganiza kuti umulungu wake umafanafana ndi fano lagolide kapena lasiliva kapena lamwala, lopangidwa mwa luso ndi nzeru za munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:12

Pa mazikoŵa munthu angathe kumangapo ndi golide, siliva, miyala yamtengowapali, mitengo, udzu kapena mapesi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:9

Ndikufunanso kuti akazi azivala mwaulemu, mwanzeru ndi moyenera. Inde adzikongoletse, komatu osati ndi tsitsi lochita kukonza monyanyira, kapena ndi zokongoletsa zagolide, kapena mikanda yamtengowapatali, kapena zovala zamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:20

M'nyumba yaikulu simukhala ziŵiya zagolide kapena zasiliva zokhazokha; mumakhalanso zamtengo kapena zadothi. Zina zimakhala za ntchito zolemerera, zina za ntchito wamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:4

Chipindachi chinali ndi guwa lagolide lofukizirapo lubani. M'chipindamo munalinso bokosi lachipangano. Bokosi lonselo linali lokutidwa ndi golide. M'bokosimo munali kambiya kagolide m'mene munali mana uja, ndi ndodo ya Aroni, ija idaaphukayi. Munalinso miyala iŵiri ija yolembedwapo mau a chipangano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:11-12

Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:7

Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:18-19

Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:3-4

Kudzikongoletsa kwanu kusangokhala kwa maonekedwe akunja pakuluka tsitsi, ndi kuvala zamakaka zagolide ndi zovala zamtengowapatali. Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:12-13

Nditacheuka kuti ndiwone akundilankhula ndani, ndidaona ndodo zoikapo nyale zisanu ndi ziŵiri zagolide. Pakati pake pa ndodo za nyalezo ndidaona wina wooneka ngati mwana wa munthu. Anali atavala mkanjo wautali, atamangira lamba wagolide pa chifuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:4

Mkaziyo adaavala zovala zofiirira ndi zamlangali, ndipo adaadzikongoletsa ndi golide, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. M'manja mwake anali ndi chikho chagolide chodzaza ndi zonyansa, ndi zoipa za ntchito zake zadama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:18-21

Linga la mzindawo linali la miyala yambee, ndipo mzinda weniweniwo unali wa golide wangwiro, woŵala ngati galasi. Maziko aja omwe linga la mzindawo lidaamangidwapo, adaaŵakongoletsa ndi miyala yamitundumitundu yamtengowapatali. Maziko oyamba anali a mwala wambee; achiŵiri anali a mwala wabuluu ngati thambo; achitatu anali a mwala wotuŵira; achinai anali a mwala wobiriŵira; Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira. Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, Wapamwamba, m'dzina la Yesu ndikubwera kwa Inu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate Woyera, ndikuyandikira kwa Inu podziwa kuti palibe wina ngati Inu, pakali pano ndikupereka moyo wanga wonse kwa Inu, ndikupempha kuti mundipatse mphamvu ndipo tsiku ndi tsiku ndizifuna Inu kwambiri kuposa golide ndi siliva. Mzimu Woyera, ndithandizeni kugwira mawu anu, osadandaula ndi zina, koma ndisunge malonjezano anu chifukwa siliva ndi yanu, golide ndi yanu, ndipo mudzapitiriza kupereka zonse zomwe ndikusowa. Ambuye, ndipatseni nzeru ndi kulimba mtima kuti mtima wanga ukhale woyera kuti ndidziwe momwe ndingakhalire pakati pa mbadwo woipa, kuti ngakhale zinthu zili bwanji, ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba chomwe chidzayesedwe ngati golide ndipo chidzapezeka choyenera ulemerero mtsogolo muubwenzi wanu. Ndipatseni kumvetsetsa kuti chimwemwe ndi masautso ndizofunikira pakukula kwanga, chifukwa chitsimikizo changa chachikulu ndichakuti simundisiya ndekha, koma mundipatse chisomo kuti ndipambane. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa