Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
“Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu.
Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Chabwino, ndikupatsani chakudya chimene chidzagwa ngati mvula kuchokera kumwamba. Anthu azituluka tsiku ndi tsiku kukatola chakudya chokwanira tsiku limodzi, kuti ndiŵayese ndipo ndiwone ngati adzayenda motsata malamulo anga kapena ai.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Chauta akunena kuti, “Inu nonse omva ludzu, bwerani, madzi ali pano. Ndipo inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule chakudya, kuti mudye. Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka, osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Zonse zolengedwa zimayang'anira kwa Inu, kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake. Mukazipatsa zimachilandira; mukafumbatula dzanja lanu, zimakhuta.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Tsono mai uja adapita kukafotokozera Elisa, munthu wa Mulungu uja. Ndipo Elisayo adauza maiyo kuti, “Mai, pitani mukagulitse mafutawo, ndipo mukabweze ngongole zanuzo. Tsono ndalama zotsala zikhale zothandizira inu ndi ana anu.”
Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
“Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Komabe Iye adalamula mitambo yamumlengalenga, natsekula zitseko zakumwamba. Poŵagwetsera mana kuti adye, adaŵapatsa tirigu wakumwamba. Motero anthu adadya buledi wa angelo, ndipo Mulungu adaŵatumizira chakudya chochuluka.
Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Ufa umene uli m'mbiyawo sudzatha, mafutanso amene ali m'nsupawo sadzatha, mpaka tsiku limene Chauta adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.
Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.
Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.
Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
Poti inu muli ndi zambiri tsopano, muyenera kumathandiza osoŵa, kuti m'tsogolomo nawonso akadzakhala ndi zochuluka, azidzakuthandizani pa zosoŵa zanu. Motero padzakhala kulingana.
Anthu onsewo adadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake ophunzira aja adatola zotsala nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri.
Yesu adaŵafunsa kuti, “Nthaŵi ina ndidaakutumani opanda thumba la ndalama, kapena thumba lapaulendo, kapenanso nsapato. Kodi pamene paja mudaasoŵapo kanthu?” Iwo adati, “Iyai.”
Sadzamva njala kapena ludzu. Mphepo yotentha kapena dzuŵa sizidzaŵapsereza, chifukwa amene amaŵachitira chifundo adzaŵatsogolera ndi kuŵaperekeza ku akasupe a madzi.
Munthu wabwino ali nazo zokwanira zoti adye nkukhuta, koma m'mimba mwa munthu woipa mumakhala pululu ndi njala.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Aisraele chakudyacho adachitcha mana. Maonekedwe ake anali onga njere zamapira, ndiponso oyera. Pakudya, ankazuna ngati buledi wopangidwa ndi uchi.
Abrahamu adaŵatcha malowo kuti Chauta adapatsa. Ndipo mpaka lero lino anthu amati, “Paphiri la Chauta adzapatsa.”
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu. Atumiki anga adzakondwa, koma inu mudzakhala ndi manyazi.
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Tsono atayesa ndi muyeso wa malita aŵiri, adaona kuti amene adaatola tambiri, sitidaŵatsalireko, amene adaatola pang'ono, sitidaŵathere. Aliyense adangotola tokwanira.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Mukamadzabzala mbeu zanu, Chauta adzakugwetserani mvula kuti zimere, ndipo mudzakolola zambiri. Tsiku limenelo ng'ombe zanu zidzapeza mabusa aakulu.
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika. Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.
Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.