Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


113 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

113 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

Nthaŵi zambiri timaganiza kuti kukhala ndi ndalama zokwanira kumatanthauza chuma chambiri ndi katundu wambiri. Koma, m’mawu a Mulungu sitikuuzidwa zimenezo. Ngakhale timaŵerenga nkhani za anthu opembedza komanso olemera, monga Abrahamu ndi Solomo, komanso oipa monga Nabala (1 Samueli 25:2-36), ngakhale Khristu sanakhale mochuluka, koma zosowa zake zonse zimakwaniritsidwa nthawi zonse.

Malemba amatiuza kuti: “Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko lino lapansi, ndipo sitingatulerenso kanthu. Chifukwa chake, pokhala ndi chakudya ndi zovala, tikhale okhutira nazo. Pakuti iwo amene afuna kukhala achuma amagwera m’chiyeso, ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zimene zimiza anthu m’chiwonongeko ndi m’chitayiko; pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha ndalama, chimene ena pochilakalaka anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zisoni zambiri.” (1 Timoteo 6:7-10).

Monga momwe tiyenera kulemekeza Mulungu m’mbali zina za moyo wathu, kumvera Mulungu pankhani ya zachuma kudzabweretsa madalitso ndi mtendere, ndipo kudzatithandiza kukhala bwino ndi ena.




1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:22

Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:21

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21

Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 13:2

Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:10

Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:9

Uzilemekeza nacho Chauta chuma chako chonse, uzimuyamika nazo zokolola zako zonse zam'minda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:34-36

Musankhenso anthu akuluakulu m'dziko lonse lino, ndipo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse za zokolola, azichiika padera pa zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chochuluka. Asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zadzinthu zimene zikubwerazi. Azichita zonsezi ndi ulamuliro wanu, ndipo aziika tirigu padera m'mizinda yonse ndi kumsunga bwino. Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha nthaŵi ya njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri imene idzabwere ndithu mu Ejipito muno, kuti choncho anthu a ku Ejipito asadzafe ndi njala.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28

“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:18

Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:11

Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 28:4

Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa pokupatsa chuma cha golide ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:20

Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma munthu wopusa amachiwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:13

“Musachenjeretse mnzanu kapena kumubera zinthu zake. Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka m'maŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:8-9

Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera, kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:8-9

Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina. Ndinu otembereredwa nonsenu, mtundu wanu wonse, chifukwa choti mumandibera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:1-4

Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu. Yesu adaŵauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga. “Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine. Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni. Tsono mudziŵiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzaŵayankhe pamlandupo. Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa. Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe. Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.” Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri. “Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika. Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo. Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere. Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa. Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6. “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.” Pambuyo pake Yesu adaŵaphera fanizo adati, “Yang'anani mkuyu ndi mitengo ina yonse. Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa. Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale. Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.” “Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.” Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi. Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:7-8

“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 25:35-37

“Mbale wako akakhala wosauka, ndipo sangathe kudzisamala, iweyo umthandize. Uzikhala naye monga ngati mlendo, ndiponso monga ngati munthu wokhala nao kanthaŵi. Usalandire chiwongoladzanja pa ndalama zimene adakongola, kapena kuwonjezerapo zina, koma uziwopa Mulungu wako, ndipo ulole mbale wakoyo kuti akhale nawe. Musakongoze mnzanu ndalama zanu kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumpatsa chakudya kuti mupeze phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:18

Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:7-8

Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja. Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 23:19-20

Mukakongoza mbale wanu ndalama, kapena chakudya kapena kanthu kena kalikonse, musamulipitse chiwongoladzanja pobweza. Mwana wam'chigololo asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta, ngakhale zidzukulu zake mpaka mbadwo wachikhumi. Mlendo yekha mungathe kumlipitsa chiwongoladzanja, koma osati mbale wanu. Lamulo limeneli mulimvere ndithu, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzadalitsa ntchito zanu zonse m'dziko limene mukukakhalamolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:47-48

Paja Chauta adakudalitsani pa zonse, komabe inu simudamtumikire mokondwa ndi mitima yachimwemwe. Motero mudzatumikira adani odzalimbana nanu amene Chauta adzakutumizireni. Mudzamva njala ndi ludzu. Zinthu zonse zidzakusoŵani pamodzi ndi zovala zomwe. Chauta adzakuzunzani mwankhanza, mpaka mutaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12-13

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:23

Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:12

Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:16

Inu Chauta, Mulungu wathu, inde tapereka mphatso zimenezi kuti akumangireni nyumba, koma zonsezi zikuchokera m'manja mwanu ndipo nzanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:11-12

Mulungu adamuyankha kuti, “Chifukwa chakuti waganiza zimenezi mumtima mwako, ndipo sudapemphe katundu, chuma, ulemu, kapena imfa ya adani ako, sudadzipempherenso moyo wautali, koma wapempha nzeru ndi luntha, kuti uzilamulira anthu anga amene ndakulongera ufumu, chabwino nzeruzo ndi luntha ndikupatsa. Ndidzakupatsanso chuma, katundu ndi ulemu, zinthu zoti panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali nazo mwa mafumu amene analipo iwe usanabadwe, ndipo sipadzaonekanso wokhala nazo iweyo utafa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 31:5-6

Tsono lamulo limenelo atangolilengeza, pomwepo Aisraele adayamba kupereka kwambiri zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse. Aisraele ndi Ayuda amene ankakhala ku mizinda ya Yuda, ankabwera ndi zigawo zachikhumi za ng'ombe ndi nkhosa, ndiponso zinthu zopatulika zimene anali atazipereka kwa Chauta, Mulungu wao, namaziika zonsezo m'milum'milu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 32:27-29

Hezekiya anali wolemera kwambiri ndiponso waulemu zedi. Tsono adadzimangira nyumba zomasungiramo chuma cha siliva, golide, miyala yamtengowapatali, zonunkhira, zishango ndiponso mitundu yonse ya ziŵiya zamtengowapatali. Adamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo ndi mafuta. Adamanga makola a mitundu yonse ya ziŵeto zosiyanasiyana ndi makola a nkhosa. Komanso adamanga mizinda yake, ndipo anali ndi nkhosa ndi ng'ombe zambirimbiri, pakuti Mulungu adaamlemeza kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 5:11

Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4

Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:4

Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24-25

Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka. Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:27

Munthu wofunafuna phindu monyenga amavutitsa banja lake, koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:18

Munthu wopanda nzeru amapereka chikole, ndipo amasanduka chigwiriro pamaso pa mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:26-27

Usakhale mmodzi mwa anthu opereka zikole, amene amasanduka chigwiriro cha ngongole. Ngati ulephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4-5

Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa. Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:27

Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23-24

Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:19

Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:2

Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:11

Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:8

Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:26

Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:19

Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28-30

“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10-12

Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu. Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:11-27

Anthu ankamva zimene Yesu ankalankhula. Tsono adaŵaphera fanizo, popeza kuti anali pafupi ndi Yerusalemu, ndipo anthuwo ankaganiza kuti Mulungu akhazikitsa ufumu wake posachedwa. Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao. Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’ Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’ “Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula. Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’ Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’ Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’ Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’ Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu. Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’ Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’ “Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’ Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Koma adani angaŵa, aja ankakana kuti ndikhale mfumu yaoŵa, bwera nawoni kuno, muŵaphe ine ndikuwona.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:44-45

Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:34-35

Panalibe munthu wosoŵa kanthu pakati pao, chifukwa onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankazigulitsa, namabwera ndi ndalama zake kudzazipereka kwa atumwi. Ndipo ndalamazo ankagaŵira munthu aliyense malinga ndi kusoŵa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:2

Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:2

Anthu a m'mipingoyo adayesedwa kwambiri ndi masautso, komabe adakondwa kwakukulu, kotero kuti adapereka moolowa manja kwenikweni, ngakhale anali amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:9

Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6-7

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10-11

Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:11-13

Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo. Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11-12

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja, kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:17-19

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:14

Anthu athunso aziphunzira kudzipereka pa ntchito zabwino, kuti azithandiza pamene pali kusoŵa kwenikweni. Azitero kuti moyo wao usakhale wopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:15-16

Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira. Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:13-15

Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira. Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-3

Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira. Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima. Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula. Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe. Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi. Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake. Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa. Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:4

Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-3

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:17-18

Paja inu mumati, ‘Ndife olemera, ndife achuma, sitisoŵa kanthu;’ osadziŵa kuti ndinu ovutika, ochititsa chifundo, amphaŵi, akhungu ndi amaliseche. Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:10

Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:11

Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali limene amayesa ndi lomutchinjiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:1-2

Ndalama zako uziike pa malonda okagulitsa kutsidya kwa nyanja, ndipo udzapeza phindu patapita masiku ambiri. Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake. Ndalama zako uzisungize pa malo angapo, malo ambiri ndithu, pakuti sukudziŵa choipa chimene chidzaoneke pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:3

Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndikudza kwa Inu, podziwa kuti Inu nokha ndinu kasupe wa chilichonse, ndi Inu amene mupati mphamvu zopezera chuma. Ndikupemphani kuti mundipatse nzeru zoyendetsera bwino ndalama zanga, osati kuzidalira, koma kubweretsa kusintha kwathunthu m'moyo wanga ndi m'banja langa malinga ndi mawu anu. Mundithandize kuzindikira nthawi zonse kuti Inu ndinu wopereka zinthu zonse, ndipo tsiku lililonse mumandalitsa kuti ndithandize ena. Mundithandize kukhala mwana wanu wochita chakhumi mokhulupirika, kuteteza mtima wanga ku umbombo ndi kusirira. Mundithandize kukhala paubwenzi wolimba ndi Inu, kuti ndizindikire kuti palibe changa, koma zonse zimachokera m'manja mwanu. Ndikufuna kumamatira kwambiri ku mawu anu, chifukwa ndiwo chitsimikizo changa chokhala woyang'anira bwino ndalama zanga, kuti ndipambane m'mbali zonse za moyo wanga. Zikomo chifukwa munadzichepetsa kuti ine ndilemere, kundiombola ku umphawi, kuvutika, ndi kusowa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa