Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


141 Mau a m'Baibulo Okhudza Udindo Pantchito

141 Mau a m'Baibulo Okhudza Udindo Pantchito


Akolose 3:23

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:7-8

Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:10

Paja nthaŵi imene tinali nanu pamodzi, tidaakulamulani kuti munthu wosafuna kugwira ntchito, kudyanso asadye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:11

Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4

Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11-12

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja, kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:4-5

Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake. Pakuti aliyense adzayenera kudzisenzera katundu wakewake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:4

Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:29

Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:13

Usakondetse tulo, kuwopa kuti ungagwe mu umphaŵi. Khala maso, ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:9

Wogwira ntchito yake mwaulesi, ali pachibale ndi munthu woononga zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10-11

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:2

Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 9:10

Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10

Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:21

Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:11

Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:17

Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 90:17

Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:24

Ogwira ntchito mwakhama adzakhala olamulira, koma aulesi adzakhala akapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:25-26

Kulakalaka kwa munthu waulesi kumamupha, poti amangokhala manja ali khoba, osagwira ntchito. Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:5

Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:8

Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:19

Wolima m'munda mwake adzakhala ndi chakudya chambiri, koma wonka nafuna zopanda pake adzasauka kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:21

Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:21

Ifetu tikufuna kuchita zabwino, osati pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:28

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:17

Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-3

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:13

Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:7-8

Paja inu nomwe mukudziŵa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsanzira. Ife sitinali aulesi pamene tinali pakati panu. Sitidalandire chakudya kwa munthu aliyense osalipira, koma tidagwira ntchito kwambiri usana ndi usiku mpaka kutopa, kuwopa kuti tingalemetse wina aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:15

Tsono Chauta adamtenga munthuyo, namukhazika m'munda wa Edeni uja kuti azilima ndi kumausamala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:19

Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga, koma njira ya munthu wolungama imakhala ngati mseu wosalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:14-15

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:13

Waulesi amati, “Pali mkango pabwalopo! Ndikaphedwa m'miseu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:9

Munthu wamba, wodzigwirira ntchito napeza zofunika, ali pabwino kuposa wongodzikuza, pamene alibe nchakudya chomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:2

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23-24

Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:35

Iwoŵa adapatsidwa luso lalikulu, kuti achite ntchito za mitundu yonse zimene amachita anthu ozokota, amisiri a ntchito zaluso, anthu oomba nsalu za bafuta wa thonje losalala kwambiri. Akudziŵadi kugwira ntchito zonse, ndipo angathenso kuganizira ntchito zonse zaluso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-16

Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:18

Munthu woipa amalandira malipiro achabechabe, koma wochita zolungama amalandira mphotho yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:4

Kopanda ng'ombe, kumakhalanso kopanda dzinthu, koma kwa ng'ombe zamphamvu, dzinthu dzimachuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:16

Moyo ndiye malipiro a anthu ochita zabwino, koma phindu la ochimwa limadzetsa machimo ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:27

Munthu waulesi sapeza zimene akukhumba, koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:16

Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi, imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5-6

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:12

Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:14

Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:27

Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28

“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:30-34

Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:24-27

“Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:8

Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:26

Njala ya munthu wantchito imamthandiza kulimbikira, ndi njalayo imene imamkakamiza kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:1-2

Chauta akapanda kumanga nawo nyumba, omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe. Chauta akapanda kulonda nawo mzinda, mlonda angochezera pachabe. Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:31

Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 31:3-5

Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi: kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa. Akudziŵanso kuzokota miyala yogwira nayo ntchito, kujoba mitengo, ndi kuchita zaluso zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:12

Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:1

Inu ambuye, antchito anu muzikhalitsana nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziŵa kuti inunso muli ndi Mbuye wanu Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 39:2-3

Chauta anali naye Yosefe, ndipo adamthandiza kuti zonse zimuyendere bwino. Adakhala m'nyumba ya bwana wake, Mwejipito uja. Pompo adammangitsa Yosefe nakamtsekera m'ndende m'mene ankasungamo akaidi a mfumu, ndipo adakhala m'menemo. Koma Chauta anali naye Yosefe, namkomera mtima kwambiri, kotero kuti wosunga ndende adakondwera naye Yosefe. Adamsandutsa kapitao woyang'anira akaidi anzake onse, pamodzi ndi zonse zochitika m'ndendemo. Zonse zinali m'manja mwa Yosefe, ndipo wosunga ndendeyo sankayang'aniranso kanthu kena kalikonse, chifukwa Chauta anali naye Yosefe ndipo ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita. Bwana wakeyo adaona kuti Chauta anali naye Yosefe, ndi kuti ankamukhozetsa pa zonse zimene ankachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:17

Mulungu wanga, ndikudziŵa kuti Inu mumapenyetsetsa mtima, ndipo mumakondwera ndi anthu achilungamo. Ndapereka mwaufulu zinthu zonse ndi mtima wolungama, ndipo tsopano ndaŵaona anthu anu amene ali panoŵa nawonso akupereka mwaufulu ndi mokondwa kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:18

Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake, chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:4

Waulesi sasoseratu pa nthaŵi yoyenera. Pa nthaŵi yokolola adzafunafuna dzinthu, koma sadzapeza kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:14

Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:2

Wolemera ndi wosauka akulingana, pakuti onsewo adaŵalenga ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:1

Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:30

Paja Ine Chauta, Mulungu wa Israele, ndidaalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la atate ako, azidzanditumikira nthaŵi zonse. Koma tsopano ndikuti zimenezo zithe basi! Ndidzachitira ulemu anthu ondichitira ulemu, koma anthu ondinyoza, Inenso ndidzaŵanyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:16

Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:24

Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:24

Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:4

Mau a Chauta ndi olungama, zochita zake zonse amazichita mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:14

Munthu amalandira zabwino zambiri chifukwa cha mau ake abwino, ntchito zimene munthu amazichita ndi manja ake zimampindulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:46-49

Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse. Pa zaka zija za dzinthu dzambiri, m'dziko lonse munali chakudya chochuluka kwambiri. Yosefe adasonkhanitsa chakudya pa zaka zisanu ndi ziŵiri, pamene kunali dzinthu dzambirimbiri ku Ejipito, nadzisunga m'mizinda. Mu mzinda uliwonse ankasungamo chakudya cha ku minda yozungulira mzindawo. Adasonkhanitsa tirigu wochuluka ngati mchenga wakunyanja. Kunali tirigu wochuluka kotero kuti adaaleka nkumuyesa komwe, popeza kuti kunali kosatheka kumuyesa tirigu yenseyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:1

Usamanyadira zamaŵa, pakuti sudziŵa zimene zidzachitika pa tsikulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:5-8

Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe. Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna. Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe. Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:20

Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:21

Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:14-15

Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja. Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:37-38

Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:6

M'maŵa uzifesa mbeu zako, ndipo madzulo usamangoti manja lende. Sudziŵa chimene chidzapindula, kaya ndi ichi kaya ndi chinachi, mwinanso ziŵiri zonsezo zitha kukhala zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:25

Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 22:15-16

Uli nawo anthu antchito ambirimbiri: amisiri a miyala, amisiri a matabwa, ndiponso anthu a nzeru zosiyanasiyana osaŵerengeka, aluso pa ntchito zao za golide, siliva, mkuŵa ndiponso chitsulo. Tiyeko uyambepo ntchito zimenezo. Chauta akhale nawe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:18

Inu mudzafooka msanga, pamodzi ndi anthu muli nawoŵa. Ntchito imeneyi njaikulu kuposa mphamvu zanu, ndipo simungaithe nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:3

Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 12:2-3

Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. “Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:3-5

Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:13-14

“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang'ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. “Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:8

Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:6

Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:17

Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:3-4

Sitifuna kupatsa anthu chifukwa chonyozera ntchito yathu, nchifukwa chake sitikhumudwitsa munthu aliyense ndi kanthu kalikonse. Koma pa zonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu pakupirira kwambiri m'masautso, m'zoŵaŵa ndiponso m'nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:20

Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:28-29

Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:8

Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa