Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

107 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

Nthaŵi zina, mavuto amatilimbira, makamaka pankhani ya zachuma. Ambiri a ife tikukhala m’maiko omwe ndalama ndi zofunika kwambiri kuti tipeze zosowa zathu za tsiku ndi tsiku. Komabe, monga ana a Mulungu, tizipereka mavuto athu, kuphatikizapo azachuma, kwa Mulungu m’Malemba Opatulika, pakuti ndi momokhamo momwe Ambuye amatipatsa mayankho omwe tikufuna.

Tiyeni tipemphere kuti mawu a Mulungu atitsogolere njira yathu ndipo akhale nyale ya mapazi athu. “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka mosavuta m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, ngakhale dziko litasweka, ndipo mapiri atagwera m’nyanja.” (Salmo 46:1-2)




Ezekieli 28:4

Nzeru zako ndi kumvetsa kwako zidakulemeretsa pokupatsa chuma cha golide ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:33

Sindidasirire ndalama kapena zovala za munthu aliyense ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 22:16

za golide, siliva, mkuŵa ndiponso chitsulo. Tiyeko uyambepo ntchito zimenezo. Chauta akhale nawe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:19

Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:9

Musatenge ndalama m'zikwama, kaya nzagolide, kaya nzasiliva, kaya nzakopala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:9

Siliva wosula wokutira mafanowo ndi wochokera ku Tarisisi, ndipo golide wake ndi wochokera ku Ufazi. Mafano aowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi anthu odziŵa kuzokota golide. Amaveka mafanowo nsalu zonyezimira ndi zofiirira. Zonsezo ndi ntchito ya anthu aluso chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 13:2

Abramu anali wolemera kwambiri. Anali ndi zoŵeta monga: nkhosa, mbuzi ndi ng'ombe, ndiponso siliva ndi golide yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:11

Mau amodzi olankhula moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide m'choikamo chasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 20:16

Ndipo adauza Sara kuti, “Mlongo wakoyu ndikumpatsa ndalama zasiliva chikwi chimodzi, kuti zikhale ngati mboni kwa onse amene ali nawoŵa kuti iwe ndiwe wosalakwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 13:9

Anthu a m'chigawo chachitatuchi ndidzaŵaika pa moto, ndidzaŵayeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Ndidzaŵayesa monga m'mene amayesera golide. Tsono adzatama dzina langa mopemba, Ine mwiniwake nkuŵayankha. Ndidzanena kuti, ‘Ameneŵa ndi anthu anga.’ Iwowo adzati, ‘Chauta ndi Mulungu wathu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 23:15-16

“Mvereni, mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi masekeli a siliva okwana 400. Koma zimenezo nchiyani pakati pa inu ndi ine? Ikani maliro anu.” Abrahamu adavomera, ndipo pamaso pa anthu onse a ku Hiti adaŵerenga masekeli a siliva okwana 400 amene Efuroni adaatchula, potsata ndalama zomwe anthu amalonda ankagwiritsa ntchito m'dzikomo pa nthaŵi imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:35

Chauta adamdalitsa kwambiri mbuyanga, ndipo adamkuza kwambiri. Ali ndi nkhosa ndi mbuzi ndi ng'ombe zochuluka. Alinso ndi siliva ndi golide, akapolo aamuna ndi aakazi, ndiponso ngamira ndi abulu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 37:28

Tsono Amidiyani ena amalonda adafika pomwepo. Abale akewo adamtulutsa Yosefeyo m'chitsime muja, namgulitsa kwa Aismaelewo pamtengo wokwana masekeli a siliva makumi aŵiri, ndipo iwowo adapita naye ku Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 42:25

Tsono Yosefe adalamula kuti matumba ao adzazidwe ndi tirigu, ndipo kuti ndalama za aliyense ziikidwe m'thumba mwake momwemo. Adalamulanso kuti aŵapatse kamba wapaulendo. Antchito a Yosefe adachitadi zonsezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 44:8

Inu nomwe mudaona kuti ife pochoka ku Kanani, tidabwera ndi ndalama zimene tidaazipeza m'matumba mwathu. Nanga tingaberenji siliva kapena golide m'nyumba mwa bwana wanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 3:22

Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 11:2

Tsopano lankhula ndi anthu, ndipo uuze mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense, kuti apemphe zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide kwa Mwejipito aliyense woyandikana naye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:35-36

Ndiponso Aisraele anali atachita monga momwe Mose adaaŵauzira. Adaapempha kwa Aejipitowo zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Chauta adasandutsa Aejipito aja kuti akhale okoma mtima, ndipo anthuwo adapatsa Aisraele zonse zimene ankapempha. Motero Aisraele adalandako chuma cha Aejipito aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:23

Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:32

Ng'ombe ikapha kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwini ng'ombeyo alipe mwiniwake wa kapoloyo masekeli asiliva makumi atatu, ndipo ng'ombe iphedwe ndi miyala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:17

Koma ngati bambo wake wa namwaliyo akana kuti mwana wakeyo asakwatiwe, munthuyo adzangolipirabe ndalama za chiwongo cha namwali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:3

Zopereka zimene ulandirezo ndi izi: golide, siliva, mkuŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 26:19

Ndipo upange masinde makumi anai asiliva pansi pa mafulemu makumi aŵiriwo. Pansi pa fulemu lililonse pakhale masinde aŵiri ogwirizira zolumikizira ziŵiri zija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 30:16

Ndalama zoombolerazo zochokera kwa Aisraele, mudzagwiritse ntchito ya m'chihema chamsonkhano. Zidzakumbutsa Chauta za Aisraele, ndipo zidzakhala zoombolera moyo wanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:5

‘Muzipereka zopereka kwa Chauta. Tsono aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka, azibwera ndi zopereka izi: golide, siliva, mkuŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 36:24

ndi masinde makumi anai chapansi pake. Pa fulemu lililonse adapanga masinde aŵiri asiliva, ogwirana ndi zolumikizira ziŵiri zija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 5:15

“Munthu akachita zinthu mosakhulupirika, nachimwa posapereka kwa Chauta zinthu zopatulika zofunika, koma mosadziŵa, apereke kwa Chauta nsembe yopepesera kupalamula chifukwa cha tchimo lakelo. Nsembe yake ikhale nkhosa yamphongo yopanda chilema, ndipo mtengo wake wa nkhosayo udzakhale wokwana masekeli asiliva, potsata kaŵerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera kupalamula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 22:11

Koma wansembe akagula kapolo ndi ndalama kuti akhale wake, kapoloyo angathe kudya nao zinthuzo. Ndipo onse amene abadwa m'nyumba mwa wansembe angathe kudyako chakudya chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 27:3

zoyenera kupereka ndi izi: pa munthu wamwamuna wa zaka makumi aŵiri mpaka zaka 60, pakhale masekeli asiliva 50, potsata kaŵerengedwe ka kunyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 27:16

“Munthu akapereka kwa Chauta chigawo cha dera la choloŵa chake, mtengo umene uike ukhale wolingana ndi mbeu zodzabzalamo. Pa mbeu za barele zokwanira makilogaramu 20, mtengo wake ukhale wokwana mashekeli asiliva 50.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 27:25

Potchula mtengo uliwonse, wansembe aziŵerenga monga momwe amaŵerengera m'Nyumba ya Chauta, ndiye kuti sekeli imodzi ikwanire magera makumi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 3:50

Adatenga ndalama zasiliva kwa ana achisamba a Aisraele okwanira 1,365, molingana ndi kaŵerengedwe ka masekeli asiliva a ku Chihema cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 7:13

Adapereka mbale imodzi yasiliva yolemera kilogaramu limodzi ndi theka, mkhate umodzi wasiliva wolemera magaramu 800, potsata muyeso wa ku malo opatulika. Ziŵiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, zoperekera za zakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 18:16

(Muzimuwombola akakhala wa mwezi umodzi). Uike mtengo wake woombolera kuti ukhale ndalama zisanu zasiliva, molingana ndi ndalama za ku malo opatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 31:22

Izi zokha, golide, siliva, mkuŵa, chitsulo, chiwaya ndi mtovu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25

Mudzatenthe mafano ao ofanizira milungu yao. Musadzakhumbire siliva kapena golide amene iwo adapangira mafanowo. Musadzatengeko zimenezi kuti mungagwe mu msampha, popeza kuti zimenezo zimamnyansa Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:13

mukadzakhala ndi ng'ombe, nkhosa, siliva ndi golide, ndipo chuma chanu chikadzanka chiwonjezekeraonjezekera,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:18

Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:17

Mfumu isadzakhale ndi akazi ambiri kuti mtima wake ungadzapotoke. Ndipo isadzadzikundikire siliva ndi golide wambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:19

Pambuyo pake amlipitsenso masekeli asiliva makumi khumi, ndipo azipereke kwa bambo wa mtsikanayo. Alipe ndithu chifukwa choti adanyozetsa mnamwali Wachiisraele amene sadamdziŵeko mwamuna. Komanso adzakhalabe mkazi wake ndithu, ndipo pa moyo wake wonse sadzathanso kumsudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 23:19-20

Mukakongoza mbale wanu ndalama, kapena chakudya kapena kanthu kena kalikonse, musamulipitse chiwongoladzanja pobweza. Mwana wam'chigololo asaloŵe mu msonkhano wa anthu a Chauta, ngakhale zidzukulu zake mpaka mbadwo wachikhumi. Mlendo yekha mungathe kumlipitsa chiwongoladzanja, koma osati mbale wanu. Lamulo limeneli mulimvere ndithu, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzadalitsa ntchito zanu zonse m'dziko limene mukukakhalamolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 25:13-15

Miyeso yopimira kulemera musakhale nayo iŵiri m'thumba mwanu, waukulu ndi waung'ono. Miyeso yopimira kuchuluka musakhale nayo iŵiri m'nyumba mwanu, waukulu ndi waung'ono. Miyeso ikhale miyeso yeniyeni yabwino, kuti mukakhale nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 6:19

Koma zonse zasiliva ndi zagolide, ndiponso zipangizo zamkuŵa ndi zachitsulo zikhale zopatulika za Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 7:21

pakati pa chuma chija, ndidaonapo mwinjiro wokongola wa ku Babiloni, ndi makilogramu aŵiri a siliva ndiponso munsi wa golide wolemera theka la kilogramu. Zonsezi ndidaazikhumba kwambiri, kotero kuti ndidatenga ndithu. Mungathe kuzipeza m'chithando changa m'mene ndidazibisa. Mukapezanso silivayo pansi pa zinthu zinazo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 17:2-4

Iyeyu adauza mai wake kuti, “Pamene munthu adaakuberani ndalama zasiliva 1,100, inu mudaamutemberera wakubayo, matembererowo ine ndidaŵamva. Ndalamazo ndi izi, zili ndi ine. Ndine ndidaatenga.” Mai wakeyo adamuuza kuti, “Chauta akudalitse mwana wanga.” Tsono iye adabwezera ndalama zonse kwa mai wake, ndipo maiyo pofuna kuchotsa temberero lija, adati, “Ndikuzipatula ndalama zasilivazi kuti zikhale za Chauta. Ndidzazipereka kuti aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Choncho ndikubwezera ndalamazo.” Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:36

Apo aliyense amene adzatsale pabanja pako adzabwera kudzampempha iyeyo tindalama kapena kachakudya. Adzanena kuti, “Mundilole ndizithandizako ansembe, kuti ndipezeko kanthu kakudya.” ’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 9:8

Mnyamatayo adayankha kuti, “Pano ndili ndi kandalama kakang'ono kasiliva, ndipo ndikapereka kwa munthu wa Mulunguyo, kuti atiwuze kumene kwapita abuluwo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 8:10-11

adatuma mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide, kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Toi kaŵirikaŵiri. Tsono Yoramuyo adabwera ndi mphatso zopangidwa ndi siliva, golide, ndi mkuŵa. Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina amene adaŵagonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 7:51

Motero Mfumu Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, siliva, golide, ndi ziŵiya. Adaziika m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:21

Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 15:18

Tsono Asa adatenga siliva yense pamodzi ndi golide, zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, napatsira atumiki ake. Ndipo adaŵatuma kuti akazipereke Benihadadi, mwana wa Tabirimoni mdzukulu wa Heziyoni, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 5:5

Pamenepo mfumuyo idamuuza kuti, “Ai ndithu upite, ine ndilemba kalata yofotokozera kwa mfumu ya ku Israele.” Choncho Naamani adanyamuka ulendo wopita ku Samariya, atatenga ndalama zasiliva 30,000, ndalama zagolide 6,000, ndiponso zovala khumi zapachikondwerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 12:13-15

Koma mabeseni asiliva a ku Nyumba ya Chauta, ngakhale mbano, mbale, malipenga, ziŵiya zagolide ndi zasiliva, sadagule ndi ndalama zimene zinkabwera ku Nyumba ya Chauta, pakuti zimenezo ankalipirira antchito okonza Nyumba ya Chauta. Anthu amene ankaŵapatsa ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo, sankaŵafunsa kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti anali anthu okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 15:19-20

Pambuyo pake Pulo, mfumu ya ku Asiriya, adadzathira nkhondo dziko la Israele. Ndipo Menahemu adakapereka kwa Pulo siliva wokwanira makilogramu 34,000, kuti Puloyo amthandize kukhazikitsa ufumu wake. Iyeyu anali wa zaka 16 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 52 ku Yerusalemu. Mai wake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. Menahemu adapeza ndalamazo kuchokera ku msonkho umene ankakhometsa Aisraele. Anthu onse olemera ankaŵakhometsa aliyense masekeli asiliva makumi asanu. Motero mfumu ya ku Asiriya idabwerera, ndipo sidakhale m'dzikomo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 22:4

“Pita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe, ukamuuze kuti aŵerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Chauta, zimene alonda apakhomo adasonkhanitsa kwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 18:10-11

adatuma mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kuti akamlonjere. Adaafunanso kukamuyamika chifukwa chakuti adaamenya nkhondo ndi Hadadezere namgonjetsa. Adaatero pakuti Hadadezereyo ankamenyana nkhondo ndi Tou kaŵirikaŵiri. Tsono adamtumizira Davide mphatso zamitundumitundu zopangidwa ndi golide, siliva ndi mkuŵa. Zimenezonso mfumu Davide adazipereka kwa Chauta, pamodzi ndi siliva ndi golide amene adaafunkha kwa anthu a mitundu ina, ndiye kuti anthu a ku Edomu, a ku Mowabu, kwa Aamoni, kwa Afilisti, ndi kwa Aamaleke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:2-7

Choncho ndidapereka za ku Nyumba ya Chauta wanga monga m'mene ndidathera, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva, mkuŵa wopangira zinthu zamkuŵa, chitsulo chopangira zinthu zazitsulo ndi mitengo yopangira zinthu zamtengo. Ndidaperekanso miyala yochuluka yomangira, ya mtundu wa onikisi, miyala ya maŵangamaŵanga, miyala yambiri yamitundumitundu yamtengowapatali ndiponso miyala ya marabulo. Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu. M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse. Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta. Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe. Tsono Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Chauta nakhala mfumu m'malo mwa Davide atate ake. Zinthu zinkamuyendera bwino, ndipo Aisraele onse ankamumvera. Atsogoleri onse, ankhondo ndi ana a mfumu Davide omwe, onsewo adadzipereka kwa mfumu Solomoni. Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe. Umu ndimo m'mene Davide, mwana wa Yese, adalamulira Aisraele onse. Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33. Tsono adamwalira atafika pokalamba zedi. Masiku ake adachuluka, pamodzi ndi chuma ndi ulemerero wake. Ndipo Solomoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake. Tsono ntchito za mfumu Davide kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza pake, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Samuele, m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la mbiri ya mneneri Gadi. Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga. M'menemo adasimba za kulamulira kwake, za mphamvu zake ndiponso za zonse zimene zidamuwonekera iyeyo, mpakanso zimene zidaonekera fuko la Israele ndiponso zimene zidaonekera maiko ena ozungulira. Ndikupereka matani a golide 100, golide wake wabwino kwambiri wa ku Ofiri, ndi matani a siliva wosalala 240. Zonsezo zidzakhala zokutira makoma a Nyumba, ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?” Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu. Zimene adapereka ku ntchito ya Nyumba ya Chauta ndi izi: matani 170 a golide, makilogramu 84 a ndalama zagolide za mtundu wina, matani 340 a siliva, matani pafupifupi 620 a mkuŵa, ndipo matani oposa 3,400 a chitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:15

Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva ndi golide kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 9:14

osaŵerengera amene ankabwera ndi anthu amalonda. Mafumu onse a ku Arabiya pamodzi ndi nduna zam'dzikomo ankabwera ndi siliva ndi golide kwa Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 24:14

Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva. Anthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 1:4

Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 7:15-16

Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi aphungu anga tapereka mwaufulu kwa Mulungu wa Aisraele, amene Nyumba yake ili ku Yerusalemu. Utengenso siliva ndi golide yense amene mumpeze m'dziko lonse la Babiloni, ndiponso zopereka zimene anthu ndi ansembe adzapereka mwaufulu, mosakakamiza, kuperekera Nyumba ya Mulungu wao ya ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 5:11

Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 7:70-71

Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530. Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 22:25

Koma Mphambe ndiye akhale ngati golide wako, akhale ngati siliva wako wamtengowapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 27:16-17

Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, kapena kukundika zovala ngati mchenga, koma olungama ndiwo amene adzavala zimenezo, ndipo anthu osachimwa adzagaŵana siliva ameneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 28:1

“Ndithudi, ulipo mgodi wa siliva, alipo malo oyengerapo golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:6

Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:10

Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:72

Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:4

Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:14

pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:10-11

Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:20

Mau a munthu wochita zabwino, ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma maganizo a anthu oipa ngachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:3

Siliva amamuyesera m'chitofu, golide amamuyesera m'ng'anjo, koma mitima amaiyesa ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:4

Chotsa zoipa m'siliva, ndipo wosula adzatha kupanga naye chiŵiya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:21

Siliva amasungunulira mu uvuni, golide amasungunulira m'ng'anjo, chonchonso munthu amayesedwa ndi mbiri yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:8

Ndidaadzikundikiranso siliva ndi golide ndiponso chuma chochokera kwa mafumu amene ndinkaŵalamulira. Ndinali ndi ondiimbira nyimbo, amuna ndi akazi omwe. Ndinalinso ndi akazi aang'ono ochuluka, aja amasangalatsa mitima ya amunaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:22

Iwe Yerusalemu, unali ngati siliva, koma tsopano wasanduka wopandapake. Unali ngati vinyo wabwino, koma tsopano uli ngati vinyo wosakanizika ndi madzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:7

Dziko la anthu anu nlodzaza ndi siliva ndi golide, ndipo chuma chao nchosatha. Dziko lao nlodzaza ndi akavalo, ndipo magaleta ao ankhondo ndi osaŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:17

“Ine Chauta ndidzadzutsa Amedi kuti amenyane ndi Ababiloni. Iwo safuna siliva ndipo sakondwa ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:10

Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva, ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:2

Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:30

Iwo ali ngati siliva wotaya, pakuti Chauta waŵakana.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 4:1

Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri. Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu. Miyala ya ku malo oyera yamwazikana, ili vuu, ku mphambano zonse za miseu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:17

Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:20-22

Monga muja anthu amasonkhanitsira siliva, mkuŵa, chitsulo, mtovu ndiponso chitini m'ng'anjo, nasonkheza moto kuti uzisungunule, ndimo m'menenso Ine ndidzakusonkhanitsireni ndili wokwiya ndi waukali. Ndidzakuikani m'kati mwa mzinda ndipo ndidzakusungunulirani m'menemo ngati m'ng'anjo. Ndidzakusonkhanitsani mumzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, mpaka mutasungunuka. Mudzasungunukadi monga momwe siliva amasungunukira m'ng'anjo. Motero mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndakukwiyirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 27:12

“Dziko la Tarisisi linkachita nawe malonda chifukwa cha katundu wako wamtundumtundu, ndipo unkagulako siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu, mosinthana ndi katundu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 2:8

Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa tirigu, vinyo ndi mafuta. Sankadziŵa kuti ndine amene ndinkamupatsa siliva ndi golide wambiri zimene anthuwo ankapangira mafano a Baala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 3:2

Motero ndidamkwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iŵiri ya barele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 2:6

Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa anthu a ku Israele akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo amagulitsa anthu achilungamo ndi siliva, amagulitsa anthu osauka ndi nsapato.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 8:6

kuti osauka tiŵagule ndi siliva, amphaŵi tiŵagule ndi nkhwaŵiro, kutinso tigulitse ndi mungu womwe wa tirigu?’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:11

Kodi ndingathe kulekerera munthu amene ali ndi sikelo zobera anzake ndiponso miyeso yonyenga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:8

Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 11:12-13

Tsono eni nkhosawo ndidaŵauza kuti “Ngati zakukomerani, mundilipire. Koma ngati si choncho, sungani ndalama zanu.” Ndiye iwowo adandilipira masekeli asiliva makumi atatu. Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Uziponye mosungira chuma.” Motero ndidatenga masekeli asiliva zija, mtengo uja adaati ndiyenera kulandirawu, nkukaziponya mosungira chuma m'Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:15

Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:3-5

Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija. Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu. Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda. Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”) Kumeneko adapatsa Yesu vinyo wosanganiza ndi ndulu kuti amwe. Koma atalaŵa, adakana kumwa. Atampachika pa mtanda, adagaŵana zovala zake pakuchita maere. Kenaka adakhala pansi namamlonda. Pamwamba pa mutu wake adaalembapo mau osonyeza mlandu womuphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.” Adapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu. Adati, “Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.” Koma iwo adati, “Ife tilibe nazo kanthu. Izo nzako.” Ankanena kuti, “Iwe, suja unkati, ‘Ndidzapasula Nyumba ya Mulungu nkuimanganso pa masiku atatu?’ Ngati ndiwedi Mwana wa Mulungu tadzipulumutsatu nkutsika pamtandapo.” Nawonso akulu a ansembe pamodzi ndi aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda ankamuseka. Ankati, “Adapulumutsa anthu ena, koma akulephera kudzipulumutsa Iye mwini. Si Mfumu ya Aisraele nanga? Atsiketu tsopano pamtandapo kuti timkhulupirire. Ankadalira Mulungu; ampulumutsetu tsopano Mulunguyo, ngati amamkondadi; paja ankati, Ndine Mwana wa Mulungu!” Zigaŵenga zimene adaazipachika pamodzi ndi Yesu zija, nazonso zinkamunyoza chimodzimodzi. Kuyambira pa 12 koloko masana mpaka pa 3 koloko, padaagwa mdima pa dziko lonse. Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?” Atamva mauwo, ena amene adaaimirira pamenepo adati, “Munthuyu akuitana Eliya.” Motero wina adathamanga nakatenga chinkhupule. Adachiviika m'vinyo wosasa, nkuchitsomeka ku bango nampatsira, kuti amwe. Koma ena adati, “Taima, tiwone ngati Eliya abweredi kudzampulumutsa.” Yudasi adakaziponya ndalamazo m'Nyumba ya Mulungu nachokapo, kenaka nkukadzikhweza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6

Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:18-19

Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:12

Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, Woyera, Wapamwamba, Wokondedwa, Woyera ndi Wangwiro, palibe chofanana ndi Uyerero wanu. Atate Woyera, mundiphunzitse kuyenda m'njira zolungama, ndikupemphani kuti mundipatse nzeru kuti ndizitsogolera m'dziko lopotoka ndi lovunda limene tikukhala masiku ano. Kukhalapo kwa Mzimu wanu Woyera kukhale koyamba m'moyo wanga, kotero kuti chofunika kwambiri kwa ine chikhale kuphunzira kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndi khalidwe logwirizana ndi chifuniro chanu. Mawu anu amati: "Kupeza nzeru n'kwabwino kuposa golidi; ndi kupeza luntha n'kwabwino kuposa siliva." Kumvetsa kuti sindiyenera kuda nkhawa ndi tsiku la mawa, koma kusunga malonjezano anu mumtima mwanga, chifukwa ndinu wopereka zinthu zonse; ndipo ndithudi ndinu Mwini wa golide ndi siliva. Ambuye, lamulirani maganizo anga ndi kalankhulidwe kanga, kuti polankhula mawu anga akhale okondweretsa ndi anzeru, osapweteka kapena kuchititsa munthu manyazi. Inu mukuti m'mawu mwanu: "Mawu oyenera ali ngati apulo wagolide m'mbale yasiliva." Zikomo Atate, ulemerero ndi ulemu zonse zikhale zanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa