Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

65 Mau a Mulungu Olimbikitsa

Mtima wanga, ukudziwa kuti chimwemwe chenicheni chimachokera kwa Yesu. Iye ndiye chiyembekezo chathu, mphamvu yathu yopitirira patsogolo. Chikondi chake chimatipatsa mphamvu zothana ndi mavuto onse, ndipo m'manja mwake muli chitetezo.

Ndikudziwa kuti nthawi zina mtima umalefuka, ndipo timafuna kungosiya zonse. Zinthu sizimayenda monga momwe tinkafunira, ndipo timaganiza kuti zonse zatayika. Koma kumbukira, bola ukupumabe, bola dzuwa likutulukabe m'mawa uliwonse, ulikali ndi mwayi waukulu wokwaniritsa maloto ako, kuona banja lako likukhalanso labwino, kuchira matenda ako, ndi kumasulidwa mwauzimu.

Palibe chosatheka kwa Mulungu Wamphamvuyonse. Ukani tsopano, pukuta misozi yako, tamanda Mulungu, ndipo yang'ana kwa Yesu kuti chikhulupiriro chako chilimbe. Sangalala ngakhale pakati pa mayesero, ndipo pakamwa pako patuluke ulemerero wa Yehova.

Kumbukira kuti nthawi yovutayi ndi yakanthawi kochepa chabe. Mulungu wakukonzera zinthu zazikulu. Khulupirira Iye, yenda naye limodzi, ndipo ugonjetse zimphona m'dzina lake.

Monga momwe Yesu ananenera: "Kwa anthu ichi n'chosatheka, koma kwa Mulungu zonse n'zotheka." (Mateyu 19:26)


Mateyu 14:27

Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 1:8

Usaŵaope, Ine ndili nawe, ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 31:24

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 6:50

Onsewotu atamuwona adaaopsedwa. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine, musaope.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 9:2

Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 19:26

Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.

“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”

Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo
Marko 9:23

Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 23:11

Tsiku lomwelo, usiku, Ambuye adadzaima pafupi ndi Paulo namuuza kuti, “Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma.”

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 9:22

Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:1

Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 1:9

Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 31:8

Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 15:7

Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:18

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 11:28

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:27

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 16:7-8

Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga. Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe.

Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”

Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu.

Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,

ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 121:5-8

Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja.

Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.

Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:26

Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Nahumu 1:7

Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.

Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 28:15

Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:7-8

“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo.

Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:26

Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 1:37

Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:11-12

“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine.

Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:7

Chauta Wamphamvuzonse ali nafe. Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:30-31

Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 20:1

Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 14:2-3

M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo.

Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu.

“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”

Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?”

Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.

Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.

“Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu.

Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine.

Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire.

Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:23-24

Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.

Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 126:5

Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoswa 10:8

Ndipo Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope anthu amenewo. Ndaŵapereka kale kwa iwe kuti uŵagonjetse. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatha kulimbika.”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5-6

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 91:15

Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 138:3

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:16-18

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.

Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.

Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:1-2

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,

chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:16-18

Khalani okondwa nthaŵi zonse.

Muzipemphera kosalekeza.

Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.

Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 17:22

Mtima wosangalala umakhala ngati mankhwala abwino, koma mtima woziya umaumitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 118:24

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 5:3-5

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira,

kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 10:23

Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:2-4

Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu.

Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.

Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi.

Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera.

Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.

Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.

Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.

Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Yesu wokondedwa, ndinu bwenzi lokhulupirika komanso malo achitetezo, chifukwa simusiya wolungama ndipo nthawi zonse mumalimbikitsa moyo wa iwo amene alibe chiyembekezo. Lero ndikupemphani kuti mundilimbikitse mtima, ndikubwera kwa inu chifukwa ndinu nokha gwero la chimwemwe chosatha. Chifukwa chake, ndikutsegula mtima wanga kuti mundikonze, munditsitse, ndi kunditonthoza ndi Mzimu wanu Woyera. Ndithandizeni kutuluka mu nthawi ino yachisoni, wonjezerani chikhulupiriro changa mwa inu, kuti ndikhale wokhoza kuyika chidaliro changa chonse mu chikondi chanu kuti palibe vuto lomwe lingakhudze moyo wanga wamaganizo. Lero ndidzipereka pa mapazi anu, ndikuyembekezera kuchitapo kanthu kwanu mwachangu. Ndikulengeza mu ola lino kuti Mzimu wanu umandipatsa mphamvu ndipo umandipatsa mphamvu kuti ndidzuke molimba popanda kugwa. Ine ndimabisala mwa inu, popeza ndinu malo anga achitetezo. Ndimakukondani Mulungu wanga ndipo ndikukuthokozani, chifukwa ndikudziwa kuti nthawi zabwino zikubwera kwa ine. M'dzina la Yesu, Ameni.