Khalani ndi mtima wofatsa, monga chipatso cha Mzimu Woyera, chimene chimadzaza moyo wanga ndi kukoma mtima, kuleza mtima, ulemu, ndi chifundo. Monga m’mawu a Mulungu m’buku la Afilipi 2:5, tikulimbikitsidwa kukhala ndi mtima ngati wa Khristu Yesu.
Tsiku ndi tsiku, ndimayesetsa kukhala chitsanzo cha Yesu pano padziko, ndikutsatira mapazi ake m’zonse zimene ndimachita. Ndimachotsa mumtima mwanga chilichonse chimene chimalepheretsa Mzimu Woyera kugwira ntchito mwa ine, ndipo ndimapemphera kuti andisinthire kukhala wofanana naye. Mwa njira imeneyi, ndimatha kuwonetsa kuti ndine mwana wa Mulungu.
Mtima wofatsa sudzikweza kapena kufuna ndewu; sudziyang’ana wokha kapena kuchepetsa ena. M’malo mwake, umavala chikondi, bata, ndi kudzichepetsa. Kukhala wofatsa n’kofunika osati mu ubwenzi wanga ndi Mulungu chokha, komanso m’moyo wanga watsiku ndi tsiku ndi anthu anzanga.
Kufatsa kumandilimbikitsa kukhala woleza mtima ndi wachifundo, kufunafuna mtendere m’malo mwa mikangano, ndi kuchitira ena ulemu ndi kukoma mtima.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.
M'dzina la Yesu Khristu wa mtima woleza ndi wofatsa, ine Paulo mwiniwake, amene anthu ena amati ndine wamantha pamene ndili pamaso panu, koma wosaopa konse pamene ndili nanu kutali, ndikuti mundimve.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.
“Uzani mzinda wa Ziyoni kuti, ‘Ona mfumu yako ikudza kwa iwe. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu. Zoonadi yakwera pa kabulu, mwana wa nyama yosenza katundu.’ ”
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza. Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.
Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.
Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta.
Uŵauze kuti asamakamba zoipa za wina aliyense, apewe kukangana, akhale ofatsa, ndipo nthaŵi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
Nanga mukufuna chiyani? Mukufuna kuti ndidzabwere kwanuko ndi mkwapulo, kapena ndi mtima wachikondi ndi wofatsa?
Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Muchotseretu pakati panu kuzondana, kukalipa, ndiponso kupsa mtima. Musachitenso chiwawa, kapena kulankhula mau achipongwe, tayani kuipa konse. Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.
Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao.
“Koma inu amene mukumva mau anga, ndikukuuzani kuti, Muzikonda adani anu, muziŵachitira zabwino amene amadana nanu. Muziŵafunira madalitso amene amakutembererani, muziŵapempherera amene amakuvutitsani. Ngati munthu akumenya pa tsaya, uperekere linalonso. Ndipo munthu akakulanda mwinjiro wako, umlole atenge ndi mkanjo womwe.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.” Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Koma amphaŵi adzaŵaweruza mwachilungamo, ndipo anthu otsika a pa dziko lapansi adzaŵagamulira mlandu wao mosakondera. Mau ochokera m'kamwa mwake adzakhala ngati ndodo yokanthira ochimwa, atalamula iyeyo anthu oipa adzaphedwa.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Nchifukwa chake munthu wodzichepetsa ngati mwana uyu, ameneyo ndiye wamkulu mu Ufumu wakumwamba.
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake. Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lililonse. Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama.
Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu: Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse.
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.”
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Chauta, ndipo anthu osauka adzakondwa chifukwa cha Woyera uja wa Israele.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Munthu wopsa mtima msanga amautsa mkangano, koma munthu woleza mtima amabweretsa mtendere.
Komatu ambiri amene ali oyambirira adzakhala otsirizira, ndipo amene ali otsirizira adzakhala oyambirira.”
Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Kodi kapena ukupeputsa chifundo chachikulu cha Mulungu, kuleza mtima kwake, ndi kupirira kwake? Kodi sukudziŵa kuti Mulungu akukuchitira chifundo chifukwa afuna kuti utembenuke mtima?
Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.
Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo. Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu.
“Anthu adamsautsa ndi kumzunza, koma iye sadalankhule kanthu. Monga momwe amachitira mwanawankhosa wopita naye kuti akamuphe, ndiponso monga momwe nkhosa imakhalira duu poimeta, nayenso adangokhala chete.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.