Musataye mtima, chifukwa mphoto yake ndi yaikulu. Baibulo limatiuza mu Aheberi 10:35. Mphoto ndi chinthu chamtengo wapatali chomwe timapeza. Mukakhulupirira Mulungu, mudzalandira mtendere, bata, ndi chitetezo. Palibe chamtengo wapatali kuposa kukhala ndi moyo wamtendere, ndipo izi zimachitika Mukamupatsa Mulungu malo oyamba mu mtima mwanu.
Mukamupempha Yesu kuti alamulire maganizo ndi mtima wanu, palibe chomwe chingakuchotseni kotheratu pa cholinga chanu. Mwina poyamba zingakukhudzeni, koma mudzabwezeretsa mphamvu zanu mwachangu, chifukwa mwayika chikhulupiriro chanu kwa Iye amene sadzalephera. Ndi chifukwa chake, ndikofunikira kuti mmawa uliwonse mulimbitse chiyembekezo chanu mwa Yesu, kuti mupitirize kukhala ndi chikhulupiriro mwa Iye, kuti mudzidyetse ndi mawu ake kuti mzimu wanu usafooke.
Motero, mudzasunga chimwemwe chanu tsiku ndi tsiku, mukupumula mu Mzimu Woyera. Musaiwale kuti mwa Mulungu ndinu wopambana, kuti palibe choletsa chomwe chingakulimbane nacho m'dzina lake. Zoonadi, padzakhala masiku ovuta ndi nthawi zopweteka, komanso ndi zoona kuti mudzalandira mphoto yaikulu chifukwa chokhulupirira Mulungu.
Moyo wanu udzadzaza ndi ubwino, simudzaopa tsogolo ndipo Mulungu sadzalephera kukwaniritsa lonjezo lake. Ngakhale anthu angasinthe, Yesu Khristu ndiye chizindikiro cha chikhulupiriro chosatha. Chifukwa chake, mukhoza kupumula, kupuma mozama, kuimitsa mutu wanu ndi kuyang'anitsitsa kumwamba.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
“Koma ndi wodala munthu wokhulupirira Chauta, amene amagonera pa Chautayo. Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Koma ine ndimadalira chikondi chanu chosasinthika. Mtima wanga udzakondwera chifukwa mwandipulumutsa.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika.
Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
Koma ine ndimadalira chikondi chanu chosasinthika. Mtima wanga udzakondwera chifukwa mwandipulumutsa. Ndidzaimbira Chauta, popeza kuti wandichitira zabwino.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.
Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka. Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu. Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo. Mulungu adzakutchinjiriza, ndipo udzapumula mwamtendere.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.” Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa. Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse.
Chauta ndiye mphamvu zimene anthu ake amadalira, ndiye kothaŵira komwe wodzozedwa wake amapulumukirako.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika. Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno. Munthu woipa amazonda munthu wabwino, amafunafuna kuti amuphe. Koma wolungamayo Chauta sadzamsiya yekha m'manja mwa mdani wake, sadzalola kuti pomuweruza, mlandu wake umuipire. Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka. Ndidaona munthu woipa akunyada ndi kudzitukumula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Koma pambuyo pake, podutsanso, ndidaona kuti palibe. Ngakhale ndidamfunafuna, sindidathe kumpeza. Upenye munthu wopanda cholakwa ndi wolungama, ndipo udzapeza kuti munthu wamtendere ali ndi zidzukulu zambiri. Koma anthu ochimwa adzaonongekeratu kwathunthu, iwo pamodzi ndi zidzukulu zao zomwe. Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.