Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Davideyo adaimbira Chauta nyimbo iyi yakuti, “Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. “Chauta adandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, adandifupa molingana ndi ungwiro wanga. Ine ndidatsata njira za Chauta sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Ndidamvera malangizo ake onse, ndipo malamulo ake sindidaŵataye. Ndinalibe mlandu pamaso pake, ndinkalewa zoipa m'moyo wanga. Nchifukwa chake Chauta wandipatsa mphotho molingana ndi kulungama kwanga, monga momwe akuwonera kuti ndilibe mlandu. “Kwa anthu okhulupirika, Inu Mulungu mumadziwonetsa okhulupirika, kwa anthu aungwiro mumadziwonetsa abwino kotheratu. Kwa anthu oyera mtima mumadziwonetsa okoma mtima, koma kwa anthu oipa mtima mumadziwonetsa ochenjera koposa. Paja anthu odzichepetsa Inu mumaŵapulumutsa, koma anthu odzikuza mumaŵatsitsa. Ndithu Inu Chauta, ndinu nyale yanga, Inu Mulungu, mumandiwunikira mu mdima. Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka. Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta.
Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo.
Onse ankamwanso chakumwa chauzimu chimodzimodzi, pakuti analikumwa m'thanthwe lauzimu limene linkaŵatsatira. Thanthwelo linali Khristu yemwe.
Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa.
Palibe mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha.
Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa, musachite ngati simukundimva, chifukwa ngati mukhala chete, ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda.
“Chauta ndiwamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wanga, thanthwe londipulumutsa.
“Iye adzandiwuza kuti, ‘Inu ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe londipulumutsa.’
Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Musadedere, musaope. Suja kuyambira kale lomwe ndakhala ndikukuuzani ndi kutsimikiza zimenezi? Inuyo ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine? Iyai, palibenso Thanthwe lina, sindikudziŵa lina lililonse.”
imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Inu Aisraele, mwaiŵala Mulungu Mpulumutsi wanu, simudamkumbukire Iye amene ndiye thanthwe lokupulumutsani. M'malo mwake, mumabzala mbeu zabwino, kubzalira milungu yachilendo,
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Ndimafunsa Mulungu, thanthwe langa, kuti, “Mwandiiŵaliranji? Ndiziyenderanji ndilikulira chifukwa chondipsinja mdani wanga?”
Tcherani khutu kuti mundimve, fulumirani kudzandipulumutsa. Mukhale thanthwe langa lothaŵirako, ndi linga langa lolimba londipulumutsa. Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo. Atamandike Chauta: wandiwonetsa modabwitsa chikondi chake chosasinthika, pamene ndinali mu mzinda wozingidwa ndi gulu la ankhondo. Ndidalankhula mwankhaŵa kuti, “Andipirikitsira kutali ndi Inu.” Koma Inu mudamva kupempha kwanga pamene ndidakudandaulirani kuti mundithandize. Kondani Chauta, inu nonse anthu oyera mtima. Chauta amasunga anthu okhulupirika, koma amalanga koopsa anthu odzikuza. Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta. Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta.
Adapitirira kunenanso kuti, “Pafupi ndi Ine pano pali thanthwe, iwe uimirire pathanthwepo. Tsono ulemerero wanga ukamapita, ndikuika mu mng'alu wa thanthwe, ndipo ndikuphimba ndi dzanja langa mpaka nditabzola.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Aliyense mwa iwo adzakhala ngati pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe. Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma, ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
Adani ao amadziŵa kuti milungu yao ndi yopanda mphamvu, ndi yosalingana ndi Mulungu wa Aisraele.
“Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha?
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Chauta akunena kuti: “Tcherani khutu inu amene mufuna kupulumuka, inu amene mufuna kuti ndikuthandizeni. Taganizani za thanthwe kumene mudasemedwa, ku nkhuti ya miyala kumene adakukumbani.
Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza.
Ndiye Mulungu wanga ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga. Ndiye linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndinu amene mumandiwombola pa nkhondo.
Bwerani kwa Iye amene ali mwala wamoyo womwe anthu adaukana, koma Mulungu adausankha kuti ngwamtengowapatali. Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.
Ine ndimathaŵira kwa Inu Chauta. Musandichititse manyazi. Adani anga amandinena, anthu olondalonda moyo wanga amapangana limodzi, namanena kuti, “Mulungu wamsiya yekha. Mlondoleni, mumgwire, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe woti ampulumutse.” Inu Mulungu, musandikhalire kutali. Inu Mulungu wanga, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ondineneza achite manyazi ndipo aonongeke. Anthu ofunafuna kundipweteka anyozedwe, ndipo achite manyazi kotheratu. Koma ine ndidzakhulupirira Inu nthaŵi zonse, ndipo ndidzapitirizabe kukutamandani. Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake. Ndidzabwera ndi uthenga wofotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta. Ndidzatamanda chilungamo chanu chokha. Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo. Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu, zimafikira mpaka kumwambamwamba. Pali yani wofanafana nanu, Inu Mulungu, amene mwachita zazikulu? Koma mundilanditse ndi kundipulumutsa, pakuti ndinu Mulungu wolungama. Tcherani khutu kuti mundimve, ndipo mundipulumutse.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Chifukwa chakuti wavomera Chauta kuti akhale malo ako othaŵirako, wavomera Wopambanazonse kuti akhale malo ako okhalamo,
Pamenepo Chauta adzafunsa anthu ake kuti, “Nanga milungu yamphamvu yomwe mumaikhulupirira ija ili kuti?
Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti, “Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika, mwala wapangodya wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu. Pamwalapo palembedwa kuti, ‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’
Onetsani chifundo chanu pakuchita zodabwitsa, Inu amene mumaŵapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja onse obwera kwa Inu, kuthaŵa adani ao.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.
Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani. Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse. Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu kuti munditeteze.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika. Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse. Mudatswanya chilombo cha m'nyanja ndi kuchisandutsa mtembo. Mudabalalitsa adani anu ndi mkono wanu wamphamvu. Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo. Mudalenga kumpoto ndi kumwera. Mapiri a Tabori ndi Heremoni akukutamandani ndi chimwemwe. Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana. Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita. Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta. Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu, ndipo amatamanda kulungama kwanu. Amanyadira ulemerero wanu ndi mphamvu zanu. Mphamvu zathu zalimba chifukwa mwatikomera mtima. Chauta ndiye chishango chathu, Woyera wa Israele ndiye mfumu yathu. Kale mudalankhula m'masomphenya kwa anthu anu okhulupirika, mudati, “Ndamuveka chisoti chaufumu munthu amene ali wamphamvu, ndamukweza amene ali wosankhidwa pakati pa anthu. Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya, kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Paja m'Malembo mudalembedwa kuti. “Ndasankha mwala wamtengowapatali. Ndikuuika tsopano m'Ziyoni, ngati mwala wapangodya. Wokhulupirira Iye sadzachita manyazi.”
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake. Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira.
ndiye adzakhala ngati malo opatulika. Koma kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzakhala ngati mwala wokhumudwitsa, ndiponso ngati thanthwe logwetsetsa. Kwa anthu a mu Yerusalemu, adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Davide adavutika koopsa, pakuti anthu ankakamba zoti amponye miyala, chifukwa cha chisoni chao pokumbukira ana ao aamuna ndi aakazi. Koma Davide adapeza mphamvu mwa Chauta, Mulungu wake.
Koma ulendo uno simudzachoka mofulumira, simudzachita chothaŵa. Chauta azidzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Aisraele azidzakutetezani kumbuyo kwanu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta! Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Yesuluni, anthu ake a Chauta adakulupala, koma iwowo adamuukira, adanenepa ndi kukula thupi, ndipo adakhuta zedi, kenaka adasiya Mulungu Mlengi wao, nanyoza mtetezi ndi mpulumutsi wao.
Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja.
Adaŵathandiza kuti azilamula maiko amapiri, ndipo adadya zomera zam'minda. Adaŵadyetsa uchi wam'mathanthwe, ndi mafuta ochokera m'nthaka yamiyala.
Pamene ankatsogolera anthu ake m'chipululu, iwo sadamve ludzu. Adaŵapatsa madzi otuluka m'thanthwe. Adang'amba thanthwelo, ndipo mudatuluka madzi.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
“Mtheradi ndikudziŵa kuti Momboli wanga alipo, ndipo pa nthaŵi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
Mulungu amathandiza mfumu yake, kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.
Mau a Mulungu akutinso, “Umenewu ndi mwala wokhumudwitsa anthu, ndi thanthwe loŵagwetsa.” Amakhumudwa popeza kuti amakana kumvera mau a Mulungu, ndipo anali oyeneradi kuti adzaone zotere.
“Inu anthu onse a pa dziko lapansi, tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke. Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.
Ena amatamira magaleta ankhondo, ena amadalira akavalo, koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu, timamutama Iyeyo mopemba.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.