Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka. Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga. Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.
Mundichitire chifundo Inu Mulungu, mundichitire chifundo, pakuti mtima wanga ukudalira Inu. Ndidzathaŵira pansi pa mapiko anu, mpaka chiwonongeko chitandipitirira.
Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika, Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu ndi kuŵalimbikitsa anthu ake. Mulungu atamandike.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu. Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu, amene m'mitima mwao amafunitsitsa kudzera m'miseu yopita ku Ziyoni. Akamadutsa chigwa cha Baka chopanda madzi, amachisandutsa malo a akasupe, mvula yachizimalupsa imachidzaza ndi zithaphwi. Mphamvu zao zimanka zichulukirachulukira. Mulungu wa milungu adzaoneka m'Ziyoni.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.
Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Ndani mwa inu amaopa Chauta, ndi kumvera mau a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira, akhulupirire dzina la Chauta, ndipo adalire Mulungu wake.
Inu Chauta yang'aneni ine, ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha, ndipo ndazunzika kwambiri. Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga, ndipo munditulutse m'masautso anga.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.
Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga. Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. M'kuŵala kumene kunali pamaso pake, munkafumira matalala ndi makala amoto, amene adabzola mitambo yophimba ija. Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto. Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu. Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera. Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Zoonadi, ndinu thanthwe langa ndi linga langa. Tsogolereni ndi kundiwongolera chifukwa Inu ndinu Chauta.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Akunena kuti, “Ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza zitunda. Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuŵa, ndipo ndidzathyolathyola mipiringidzo yake yachitsulo.
Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Mundikhalire thanthwe lothaŵirako, ndiponso linga lolimba lopulumukirako. Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa, koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Lolani kuti m'maŵa ndimve za chikondi chanu chosasinthika, chifukwa ndimakhulupirira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiziyendamo, pakuti ndimapereka mtima wanga kwa Inu.
Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu. Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.
Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza.
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.