M’kati mwa matenda, Mulungu ali nawe. Ndipo si pamenepa pokha, koma kuyambira uli m’mimba mwa amayi ako, iye analipo, akusamalira. Dziwa kuti mwa Mulungu muli ndi Atate, bwenzi lokhulupirika, chitonthozo m’masautso, mtendere wanu m’chipwirikiti, ndi dokotala wabwino koposa. Sindikudziwa kuti ndi gawo liti la thupi lanu lomwe likudwala, kapena kuti matenda anu ndi otani, koma chomwe ndikudziwa ndichakuti, kudzera m’magazi a Yesu, mungachiritsidwe, ndipo Iye akufunanso kukuchiritsani. Amakukondani kwambiri moti sakufuna kuti mudwale ndi matenda aliwonse. Choncho, kupita kwa Iye m’mavuto anu ndi malo abwino kwambiri otetezeka omwe mungapeze, chifukwa Iye amadziwa zomwe mukufuna, zomwe mukusowa, ndi komwe mukumva kupweteka. Ngati mungakhulupirire ndikupempha ndi chikhulupiriro, adzalemekezedwa.
Ndi chifukwa cha nsembe ya Yesu Khristu ife tili omasuka ku matenda. Mwina mwalandira kale mawu a dokotala, koma limbikani mtima chifukwa Mulungu ndiye amene ali ndi mawu omaliza pa moyo wanu. Mumakhala ndipo mumapitiriza chifukwa cha zomwe zimatuluka mkamwa mwa Mulungu Wamphamvuyonse. Choncho, bwererani mukhulupirire, dzadzani ndi chiyembekezo, ndipo dikirani Mulungu moleza mtima. Angachite chozizwitsa ndi kukhala yankho la pempho lanu. Choncho, dzilengezeni kuti ndinu wathanzi m’dzina la Yesu ndipo khalani m’mawu ake. Zoonadi, iye ananyamula matenda athu, natenga zowawa zathu; koma ife tinamuyesa wolasa, wamenyedwa ndi Mulungu, ndi wozunzidwa. Yesaya 53:4.
“Komabe m'tsogolo mwake ndidzaupatsanso moyo ndi kuuchiritsa. Anthu ake ndidzaŵachiritsa ndi kuŵapatsa zabwino zochuluka ndi mtendere weniweni.
Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Anenedi choncho oomboledwa a Chauta, amene Iye waŵapulumutsa ku mavuto. Chauta adatumiza mau ake, naŵachiritsa anthuwo, adaŵapulumutsa kuti asaonongeke. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.
Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Ndichitireni chifundo, Inu Chauta, chifukwa chakuti ndine wofooka. Limbitseni, Inu Chauta, chifukwa m'nkhongono mwanga mwaweyeseka.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Chauta adzakutchinjirizani pa matenda onse. Iye sadzalolanso kuti matenda oopsa a ku Ejipito amene mumaŵadziŵa aja, afikenso pa inu, koma Mulungu adzadzetsa matenda ameneŵa pa adani anu onse.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa. Usamadziwona ngati wanzeru. Uziwopa Chauta, ndipo uleke zoipa. Kuchita choncho kudzapatsa thupi lako moyo, kudzalimbitsa mafupa ako.
“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao. Anthu onse akutali ndi apafupi, ndidzaŵapatsa mtendere. Ndidzachiritsa anthu anga.
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
Chauta adatumiza mau ake, naŵachiritsa anthuwo, adaŵapulumutsa kuti asaonongeke. Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.
Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo.
Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale chovala chake chokhacho, ndichira.”
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri.
Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.”
Anthu akunena kuti, “Tiyeni, tibwerere kwa Chauta. Watikadzula, komabe adzatichiritsa. Watikantha, komabe adzamanga mabala athu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse. Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula. Tamandani Chauta, inu magulu a ankhondo ake onse, atumiki ake ochita zimene Iye afuna. Tamandani Chauta, inu zolengedwa zake zonse, ku madera onse a ufumu wake. Nawenso mtima wanga, tamanda Chauta! Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse. Ndiye amene amapulumutsa moyo wako ku manda. Amakuveka chikondi chake chosasinthika ndiponso chifundo chake ngati chisoti chaufumu.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena. Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako. Paja zimampatsa moyo amene wazipeza, zimachiritsa thupi lake lonse.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.