Mulungu amafuna kukhala nawe pa chilichonse chimene ukuchita. Afuna ukhale ndi chikhulupiriro chonse kuti Atate akuyang’anira zinthu zonse zazing’ono ndi zazikulu m’moyo wako.
Pa nthawi yokongola iyi m’moyo wako, uli ndi dalitso lalikulu, mphatso yapadera yomwe uyenera kuisamalira ndi kuikonda kwambiri. Uyenera kuisamalira kuti ikule bwino, ukhale woleza mtima ndipo uiiyetse mwanzeru pamene ikukula.
Kukhala ndi pakati kukubweretsera chimwemwe chachikulu, chifukwa uli ndi munthu amene akukufuna tsiku lililonse. Muzipsompsona, muziimbira nyimbo, ndipo muzipempherera.
Sangalala ndi gawo lililonse la mimba yako ndipo ukhale ndi chiyembekezo kuti zonse zidzayenda bwino. Lankhula ndi Mzimu Woyera, umupemphe kuti akuthandize pa mantha ako ndi kukupatsa mphamvu pa nthawi yobereka.
Mwana akangobadwa, yamikani Mulungu ndipo sangalalani ndi mphindi iliyonse naye. Kubweretsa moyo padziko lapansi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.
Pa nthaŵi yochira mai amavutika chifukwa nthaŵi yake yafika. Koma pamene wabadwa mwana, saganizakonso za kuzunzikako, chifukwa cha chimwemwe chakuti kunja kuno kwabadwa mwana.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Tsono poti mkazi wa Isaki anali wosabereka, Isakiyo adapempherera mkazi wake kwa Chauta. Chauta adamva pemphero lake, ndipo Rebeka adatenga pathupi.
Adamu adakhala ndi mkazi wake Heva ndipo mkaziyo adatenga pathupi. Tsono adabala mwana wamwamuna, ndipo adati, “Ndalandira mwana wamwamuna mwa chithandizo cha Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Kaini.
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Tsono Mulungu adakumbukira Rakele, namva pemphero lake, nkulola kuti abale ana.
Iyenso adatenga pathupi, nabala mwana wamwamuna. Ndipo adati, “Mulungu wandichotsa manyazi a uchumba wanga.”
Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Pambuyo pake mkazi wake Elizabeti adatenga pathupi, nabindikira miyezi isanu.
Adati, “Ambuye andichitira zotere: nthaŵi inoyi andiwonetsa chifundo chao, andichotsa manyazi pakati pa anthu.”
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
“Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.
Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”
Pamene Elizabeti adamva malonje a Maria, mwana adayamba kutakataka m'mimba mwake. Elizabeti adadzazidwa ndi Mzimu Woyera,
ndipo adalankhula mokweza mau kuti, “Ndinu odala kupambana akazi ena onse, ngwodalanso Mwana wanu.
Ine ndine yani kuti inu, mai wa Ambuye anga, mudzandiyendere?
Chifukwatu pamene ndinamva malonje anu, mwana anayamba kutakataka ndi chimwemwe m'mimba mwanga.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Sara yemwe adalandira mphamvu zakutenga pathupi, ngakhale zaka zake zakubala mwana zinali zitapita kale. Zimenezi zidatheka chifukwa adaavomera kuti amene adazilonjezayo ngwokhulupirika.
Adatenganso pena pathupi, nabala mwana winanso wamwamuna, ndipo adati, “Tsopano ndidzatamanda Chauta.” Motero mwanayo adamutcha Yuda. Apo adayamba walekeza kubala.
Pambuyo pake Mulungu adauza mkaziyo kuti, “Ndidzaonjeza zovuta zako pamene udzakhala ndi pathupi, udzamva zoŵaŵa pa nthaŵi yako ya kubala mwana. Udzakhumba mwamuna wako, ndipo mwamuna wakoyo adzakulamulira iwe.”
Zidafika poipa kwambiri, ndipo mzamba adamuuza kuti, “Musaope, ameneyu ndi mwana wina wamwamuna.”
Motero Hana adaima, ndipo adabala mwana wamwamuna namutcha dzina loti Samuele, kunena kuti, “Ndidachita kumpempha kwa Chauta.”
“Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi.
Adaŵadalitsa poŵauza kuti, “Mubereke ndi kuchulukana, mudzaze dziko lonse lapansi ndi kumalilamulira. Ndakupatsani ulamuliro pa nsomba, mbalame ndi nyama zonse zimene zikukhala pa dziko lapansi.”
Mwana uyu ndidachita kupempha, ndipo Chauta wandipatsa chopempha changacho.
Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako.
Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
Mverani inu anthu a ku maiko a m'mphepete mwa nyanja, tcherani khutu, inu anthu akutali. Chauta adandiitana ndisanabadwe, adanditchula dzina ndidakali m'mimba mwa amai anga.
Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu.
“Mukamathandiza azimai achihebri pochira, akabadwa mwana wamwamuna, mupheni, akakhala wamkazi, mlekeni.”
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
ndipo adabala mwana wake wachisamba wamwamuna. Adamkulunga m'nsalu namgoneka m'chodyera cha zoŵeta, chifukwa adaasoŵa malo m'nyumba ya alendo.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.”
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Chauta adakumbukira Sara namchitira zimene adaamulonjeza.
Sara ataona, adauza Abrahamu kuti, “Mchotseni mdzakaziyu pamodzi ndi mwana wake yemweyu. Mwana wa mdzakazi asadzalandireko chuma chanu chimene adzalandire mwana wanga Isaki.”
Zimenezi zidamuvuta kwambiri Abrahamu, chifukwa chakuti Ismaele nayenso anali mwana wake.
Koma Mulungu adauza Abrahamu kuti, “Mtima wako usavutike chifukwa cha mwanayo ndi mzikazi wako Hagara. Zonse zimene akukuuza Sara uchite, chifukwa Isakiyu ndi amene adzakhala kholo la zidzukulu zako monga momwe ndidakulonjezera.
Mwana wa mdzakaziyunso ndidzampatsa ana ambiri, ndipo adzasanduka mtundu ndithu, popeza kuti iyeyunso ndi mwana wako.”
M'maŵa mwake, m'mamaŵa, Abrahamu adapatsa Hagara chakudya ndi thumba lachikopa la madzi. Kenaka adatenga mwanayo nabereketsa Hagara, ndipo atatero adamuuza kuti azipita. Hagara adachokadi, nkumangoyendayenda m'chipululu cha Beereseba.
Tsono madzi aja atamthera, adangosiya mwanayo pa chitsamba.
Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira.
Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu.
Dzuka, pita, ukamnyamule ndi kumgwiritsa ndi dzanja lako. Zidzukulu zako zidzakhala mtundu waukulu.”
Apo Mulungu adatsekula maso a Hagara, ndipo adaona chitsime. Iye adapita pachitsimepo, nakadzaza thumba lachikopa lija ndi madzi, nkumwetsako mwanayo.
Choncho Sarayo adatenga pathupi, nabalira Abrahamu mwana wamwamuna pamene Abrahamuyo anali nkhalamba. Mwana ameneyu adabadwa pa nthaŵi yeniyeni imene Mulungu adaanena.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo.
Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Kodi ine ndidzafikitsa anthu anga mpaka nthaŵi yobala, koma osalola kuti abaledi?” Akuterotu Chauta. “Kodi Ine, amene ndili wobalitsa, ndingatseke mimba nthaŵi imeneyo?” Akuterotu Mulungu wako.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna.
Anzake ndi abale ake atamva kuti Ambuye amchitira chifundo chachikulu chotere, adakondwera naye pamodzi.
Rakele ataona kuti sakumubalira ana Yakobe, adayamba kuchita nsanje ndi mkulu wake uja, ndipo adauza Yakobe kuti, “Mundipatse ana, apo ai, ndingofa basi.”
Ndipo Zilipa adabala mwana wamwamuna.
Tsono Leya adati, “Ndachita mwai.” Motero mwanayo adamutcha Gadi.
Zilipa mdzakazi wa Leyayo adamubaliranso Yakobe mwana wamwamuna wachiŵiri.
Apo Leya adati, “Ndakondwa! Ndipo akazi adzanditchula wamwai.” Motero mwanayo adamutcha Asere.
Pa nthaŵi yodula tirigu, Rubeni adapita ku minda, nakapezako zipatso za mankhwala a chisulo, ndipo adadzapatsa Leya mai wake. Rakele adauza Leya kuti, “Chonde patseko mankhwala amene mwana wako wakufuniraŵa.”
Leya adayankha kuti, “Kodi sunakhutitsidwebe ndi mwamuna wanga udandilandayu? Tsopano ufuna kutenganso mankhwala a chisulo amene mwana wanga wandifunira?” Rakele adati, “Ukandipatsa mankhwala a chisulo ochokera kwa mwana wakoŵa, ŵamunaŵa akhala ndi iwe usiku uno.”
Pamenepo Yakobe ankabwera madzulo kuchokera ku munda, Leya adatuluka kukamlonjera, nati “Lero mugone kunyumba kwanga kuno, chifukwa cha mankhwala a chisulo ondifunira mwana wanga.” Motero Yakobe adakhala ndi Leya usiku umenewo.
Mulungu adamva pemphero la Leya, choncho adatenga pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu.
Tsono adati, “Mulungu wandipatsa mphotho chifukwa ndidapereka mdzakazi wanga kwa mwamuna wanga.” Motero mwanayo adamutcha Isakara.
Leya adatenganso pena pathupi, namubalira Yakobe mwana wamwamuna wachisanu ndi chimodzi.
Yakobe adapsera mtima Rakele, namuuza kuti, “Sindingathe kuloŵa m'malo mwa Mulungu. Iyeyo ndiye akukuletsa kubala ana.”
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Zoonadi, ndidabadwa mu uchimo, ndinali mu uchimo kuyambira pamene mai wanga adatenga pathupi pa ine.
Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira.
Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere.
Ndiyetu mudamlenga mochepera pang'ono kwa Mulungu amene, mudampatsa ulemerero ndi ulemu wachifumu.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Chauta ataona kuti Yakobe sankakonda kwambiri Leya, adalola kuti Leyayo abale ana, koma Rakele ai.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
“Fuula ndi chimwemwe iwe Yerusalemu amene wakhala ngati chumba chopanda ana, fuula mosangalala, iwe amene sudamvepo zoŵaŵa za kubala. Pakuti tsopano udzakhala ndi ana ochuluka kuposa mkazi amene sadasiyidweko ndi mwamuna wake,” akuterotu Chauta.
Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao, adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima.
Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu.
Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.
Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.
Adzalalika za chipulumutso chake kwa anthu amene mpaka tsopano sanabadwe, ponena kuti Chauta ndiye adapulumutsa anthu ake.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Tsono Sara adati, “Mulungu wandikondweretsa ndi kundiseketsa. Aliyense amene adzamve zimenezi, adzakondwera nane.”
Ndipo adati, “Akadadziŵa ndani kuti Sara nkuyamwitsa mwana? Komabe ndamubalira mwana wamwamuna Abrahamu pamene ali nkhalamba.”
Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Chauta adati, “Ndikukulonjeza kuti pakapita miyezi isanu ndi inai ndidzabweranso, ndipo mkazi wako adzakhala ali ndi mwana wamwamuna.” Sara ankangomvetsera ali kuseri kwa chitseko cha hema.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Chauta adadalitsadi Hana, ndipo adabala ana aamuna atatu ndi ana aakazi aŵiri. Ndipo mnyamata uja Samuele ankakula akutumikira Chauta.
Leya adatenga pathupi, ndipo adabala mwana wamwamuna. Tsono adati, “Chauta waona zovuta zanga. Ndithu tsopano mwamuna wanga adzayamba kundikonda.” Motero mwanayo adamutcha Rubeni.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.