M'Baibulo, Mulungu adzidziwitsa yekha ngati mdani wa osowa pothawirapo komanso Atate wa ana amasiye. M'buku la Deuteronomo 10:18, tikukumbutsidwa kuti: "Amachitira chiweruzo ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo akumupatsa chakudya ndi zovala."
Mu vesili, titha kuwona kuti Mulungu amasamala kwambiri za iwo omwe ali pamavuto ndipo asasiyidwa. Chikondi chake pa anthu n'chachikulu kwambiri moti ndi Iye amene amachitapo kanthu pothandiza ana amasiye, kuwabwezera ufulu wawo, ndikuwalangiza.
M'dziko lino lomwe lili ndi zosowa zambiri, pomwe ambiri amatsutsa ululu, komwe ena sasamala za mavuto a anzawo, ine ndi iwe ndife oitanidwa kuwonetsa Mulungu ndikukhala yankho lake ku zosowa zambiri.
Ndikukupempha kuti usakane kuchita zabwino. Ukhale wachifundo kwa mwana, wachinyamata, ndi wachinyamata omwe alibe pokhala chifukwa chosowa makolo awo. Ukhale wokoma mtima kwa iwo ndi kuwapatsa chithandizo chako.
Usakane kuwapatsa chakudya kuti akhute chifukwa ndikukutsimikizira kuti Mulungu sadzaiwalitsa zabwino zomwe wachitazi.
Pomaliza, usaiwale kuwapempherera ndikuwalankhula za chikondi cha Mulungu. Uwawonetse kuti pali cholinga chosatha chomwe chimadziwa mayina awo ndipo pali chiyembekezo mwa Khristu cha tsogolo lawo.
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.
Zidatero chifukwa choti ndinkapulumutsa amphaŵi olira, ndinkalanditsa ana amasiye opanda woŵathandiza.
Inu Chauta, kumbukirani zimene zatigwera. Muyang'ane, muwone m'mene anthu akutinyozera. Khungu lathu likutentha ngati lili m'ng'anjo chifukwa cha ululu wa njala. Ku Ziyoni akazi akuŵachita zadama mwakhakhamizo. M'mizinda ina ya ku Yuda anamwali akuŵachita chimodzimodzi. Akalonga akuŵapachika pomangirira manja ao, akuluakulu sakuŵalemekeza konse. Achinyamata akuŵakakamiza kupera tirigu, anyamata akudzandira nayo mitolo ya nkhuni. Akuluakulu adachokapo pa bwalo la mzinda, achinyamata nyimbo zao zija zati zi! Chimwemwe chachoka m'mitima mwathu. Kuvina kwathu kwasanduka kulira. Chisoti chathu chaufumu chachoka kumutu, kugwa pansi. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa. Nchifukwa chake mitima yathu yalefuka, chifukwa cha zimenezi m'masomu mwachita chidima. Phiri la Ziyoni lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo. Koma Inu Chauta, ndinu mfumu mpaka muyaya, mpando wanu waufumu udzakhalapo pa mibadwo yonse. Choloŵa chathu chaperekedwa kwa alendo, nyumba zathu zili m'manja mwa anthu akudza. Chifukwa chiyani mwakhala mukutiiŵala nthaŵi yonse? Chifukwa chiyani mwatisiya nthaŵi yaitali chotere? Inu Chauta mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere mwakale. Mutipatsenso masiku onga amakedzana aja. Kaya, monga nkuti mwatitayiratu? Monga nkuti mwatikwiyira kopitirira? Ife tili ngati ana amasiye, opanda bambo wao. Amai athu ali ngati akazi amasiye.
Amateteza ana amasiye ndi akazi amasiye. Amakonda anthu achilendo amene amakhala pakati panu, ndipo amaŵapatsa chakudya ndi zovala zomwe.
Inutu mumaonadi, mumazindikira zovuta ndi zosautsa, kuti muchitepo kanthu. Wopanda mwai amadzipereka kwa Inu. Nayenso wamasiye mumamthandiza.
Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.
Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Ndipo aliyense wolandira bwino mwana wonga ngati uyu chifukwa cha Ine, ndiye kuti akulandira bwino Ine amene.”
Musamazunze akazi amasiye ndi ana amasiye, alendo ndiponso amphaŵi. Musamaganizirane zachiwembu m'mitima mwanu.
Alendo kapena ana amasiye musaŵalande zao zoŵayenera, poŵapotozera mlandu wao. Ndipo mkazi wamasiye musamlande chovala kuti chikhale pinyolo ya ngongole.
Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano.
Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Phunzirani kuchita zabwino. Funafunani chilungamo, opsinjidwa muŵathandize. Tetezani ana amasiye, muŵaimirire pa milandu yao akazi amasiye.”
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?
Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi.
Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa. Amapha akazi amasiye ndi alendo okhala nawo m'dziko mwao, amaphanso ana amasiye.
Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu. Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
Atsogoleri ako apanduka, ndipo amagwirizana ndi mbala. Aliyense amakonda chiphuphu, ndipo amathamangira mphatso. Satchinjiriza ana amasiye, ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye.
Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi.
Anthu ako akhala akunyoza atate ao ndi amai ao. Akhala akuzunza alendo okhala nawe, akhalanso akusautsa ana amasiye ndi akazi amasiye.
Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga.
“Atembereredwe aliyense woweruza mopotoza milandu ya alendo, ya ana amasiye, ndi ya akazi amasiye.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
“Usaope, chifukwa sadzakunyozanso, usataye mtima poti sadzakupeputsanso. Udzaiŵala zimene zidakuchititsa manyazi pa unyamata wako, manyazi a pa umasiye wako sudzaŵakumbukanso.
Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye. Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo.
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Munthu wosalankhula umlankhulire ndiwe. Anthu osiyidwa uŵalankhulire pa zoŵayenerera. Uzilankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uziteteza amphaŵi ndi osauka.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende. Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo. Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.
Pakutero amapotoza malamulo poweruza amphaŵi mosalungama. Amaŵalanda zoŵayenerera anthu anga osauka, amafunkha za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye!
Chakudya chimenechi ncha Alevi, poti alibe zaozao. Ndiponso ncha alendo ndi cha ana amasiye ndi akazi amasiye amene amakhala nanu pamodzi m'midzi mwanu. Anthu otere azibwera kudzatenga zimene akusoŵa. Muzichita zimenezi kuti Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitseni pa ntchito zanu zonse.
Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu. Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Ochepa okha adzatsalako, monga pogwedeza mtengo wa olivi, zimatsalako ndithu zipatso ziŵiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni, kapenanso zinai kapena zisanu pa nthambi zam'munsi,” akutero Chauta, Mulungu wa Israele.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Ndidaonanso kuzunza kulikonse kochitika pansi pano. Ndipo ndidaona ozunzidwa akulira misozi, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti aŵatonthoze. Panalibe oŵatonthoza chifukwa ozunzawo anali ndi mphamvu.
Ndidzati, “Inu omvera Chauta, mtamandeni Iye. Inu nonse ana a Yakobe mlemekezeni Iye, inu nonse ana a Israele, mchitireni Iye ulemu.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake. Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse. Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse. Anthu anjala muziŵagaŵirako chakudya chanu, osoŵa pokhala muziŵapatsako malo. Mukaona wausiŵa, mpatseni chovala, musalephere kuthandiza amene ali abale anu.
Amalankhula modzikuza ndipo amanyadira zoipa zao. Amatswanya anthu anu, Inu Chauta, amazunza anthu anu osankhidwa. Amapha akazi amasiye ndi alendo okhala nawo m'dziko mwao, amaphanso ana amasiye.
Adzakhala wodala munthu amene adzatenga makanda ako ndi kuŵakankhanthitsa ku thanthwe.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali. Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani.
Koma ine m'kulungama kwanga ndidzaona nkhope yanu. Tsono ine nditadzuka, ndidzakondwa kotheratu poonana ndi Inu.
Iye adakakhala pansi poteropo, pa mtunda wa mamita 100, chifukwa ankati, “Ine sindingathe kumaonerera mwana wanga alikufa chotere.” Ali pansi pomwepo, mwanayo adayamba kulira. Mulungu adamumva mwanayo akulira, ndipo mngelo wa Mulungu adalankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba, adati, “Kodi iwe Hagara, chikukuvuta nchiyani? Usachite mantha. Mulungu wamva kulira kwa mwanayu.
sazunza munthu wina aliyense, satenga chigwiriro ndipo saaba. Koma amadyetsa anjala ndi kuveka ausiŵa.
Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake.
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito. Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani.
Alendo kapena ana amasiye musaŵalande zao zoŵayenera, poŵapotozera mlandu wao. Ndipo mkazi wamasiye musamlande chovala kuti chikhale pinyolo ya ngongole. Kumbukirani kuti paja mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo kuti Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani kumeneko. Nchifukwa chake ndakupatsani lamulo limeneli.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Uziŵachitira ulemu azimai amasiye, amenetu ali amasiye enieni. Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika, chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale. Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala. Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
“Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina.
Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku ulamuliro wa manda, sindidzaopa, pakuti Iye adzandilandira.
Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira.
Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu. Inde unali ufulu kuchita zimenezi, komanso unali udindo wao kuthandiza osaukawo. Ayuda adagaŵana madalitso ao achikhristu ndi anthu a mitundu ina, choncho iwowo ayeneranso kuthandiza Ayudawo pa zosoŵa zao za moyo wathupi.
Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
“Chenjerani, musachite ntchito zanu zabwino pamaso pa anthu ndi cholinga choti akuwoneni. Mukatero, simudzalandira mphotho kwa Atate anu amene ali Kumwamba.
Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu. Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti,
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake.
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
kuti ndiwone zokoma za osankhidwa anu, kuti ndigaŵane nawo chisangalalo cha mtundu wanu, kuti ndipeze ulemerero pamodzi ndi anthu anu.
Mlengi wako ali ngati mwamuna wako. Chauta Wamphamvuzonse ndiye dzina lake. Woyera Uja wa Israele ndiye Momboli wako, dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Mmphaŵi usamubere, chifukwa choti iyeyo ndi wosauka. Anthu ozunzika usaŵapondereze pa bwalo la milandu. Pakuti Chauta adzaŵateteza pa mlandu wao, ndipo adzaŵalanda moyo amene amalanda zinthu zao.
Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu. Ndimafunsa kuti, “Kodi mudzandithandiza liti?”
Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo. Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa. Pamene ndidagwa m'zoopsa, Iye adandipulumutsa.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.