Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


106 Mau a Mulungu Pa Zokhulupirika ndi Mphatso

106 Mau a Mulungu Pa Zokhulupirika ndi Mphatso

Mulungu waika mphatso yapadera mwa iwe kuti ugwire ntchito inayake. Akufuna kuti uikulitse mphatsoyo molimba mtima, podziwa kuti uli ndi mzimu wake mkati mwako ndipo uli ndi mphamvu zokwaniritsa chilichonse chimene wakuikira. Choyamba, uzikhudzidwa wekha. Ukakhala ndi chikhulupiriro chotere, palibe chokulepheretsa ndipo sungaleke mpaka utakwaniritsa zomwe ukulota.

Chachiwiri, uzimenyane ndi mantha ako, chifukwa mantha, ngati sungawagonjetse, angakulepheretse kuchita chifuniro cha Mulungu. Mdani nthawi zonse amafuna kuti ubise kumbuyo kwa kukayikira kwako, zofooka zako, ndi kusadzidalira kwako. Cholinga chake ndi kukuphimba maso kuti usawone zabwino zonse zimene Mulungu akunena za iwe, ndipo umangoyang'ana pa zoipa zokha, mpaka kufika poletsa maloto ako, mapulojekiti ako, ndi malingaliro ako.

Yesu anaika luso lake mwa iwe ndipo chomwe akufuna kwambiri ndi chakuti usabise mphatso zako. Maluso amene uli nawo unawapatsidwa kuti udzadalitse anthu ambiri, osati kuti udzisungire wekha, koma kuti ukhudze miyoyo yawo. Gwiritsa ntchito maluso ako potumikira Mulungu ndipo ukhale chida chamtengo wapatali m'manja mwake.




1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:29

Pakuti Mulungu sasinthanso ataitana munthu ndi kumpatsa mphatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:4

Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:7

Munthu wotere asamaganiza kuti nkudzalandira kanthu kwa Ambuye ai;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:14

Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-15

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:7

Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:4-7

Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timaŵatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:17

Sikuti ndikuika mtima pa mphatso zanu ai, koma chimene ndikukhumba nchakuti pa zimene muli nazo, pawonjezedwe phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:10

“Anthu onse aluso pakati panupa abwere, ndipo apange zonse zimene Chauta adalamula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:29

Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10-11

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-13

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:4-5

Aliyense aziyesa yekha ntchito zake m'mene ziliri. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, osati chifukwa zapambana ntchito za mnzake. Pakuti aliyense adzayenera kudzisenzera katundu wakewake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:12-14

Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:6

Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:16

Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi, imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:27-31

Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa? Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.” Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira? Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:7

Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:11

Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:7

Komabe aliyense wa ife adalandira mphatso yakeyake yaulere, molingana ndi m'mene Khristu amaperekera mphatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:8

Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:29

Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:24-25

Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:2

Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:2

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:31

Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:21

Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:1

Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:18

Kumene kulibe mithenga yochokera kwa Mulungu, anthu saweruzika, ndi wodala munthu amene amatsata malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:24-26

Kodi mlimi wofuna kubzala amangokhalira kutipula kokhakokha? Kodi amangokhalira kugaula ndi kugalauza? Akasalaza mundawo, suja amafesa maŵere ndi chitoŵe? Suja amafesa tirigu ndi barele m'mizere, nabzala mcheŵere m'mphepete mwa mundawo? Mulungu ndiye amamulangiza ndi kumphunzitsa njira yokhoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28-29

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:24

Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-7

Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:73

Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:15

Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:10

Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-16

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:18

Koma m'mene ziliri Mulungu adaika chiwalo chilichonse pamalo pake m'thupi, monga momwe adafunira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:26

Chiwalo chimodzi chikamamva kuŵaŵa, ziwalo zonse zimamvanso kuŵaŵa. Chiwalo chimodzi chikamalandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwa nao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:13-14

Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe. Amadzetsa mtendere m'malire a dziko lako, amakudyetsa pokupatsa ufa wa tirigu wosalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:5

Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:17

Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:46

Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene adayamba kugwirira ntchito Farao mfumu ya ku Ejipito. Adanyamuka, nayendera dziko lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:2

Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:34-35

Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:5

Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 9:10

Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 90:17

Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:12

Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:4-5

Inu Chauta, mwapereka malamulo anu ndipo mwalamula kuti atsatidwe kwathunthu. Onani ndikulakalaka kutsata malamulo anu. Mundipatse moyo chifukwa ndinu olungama. Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera. Pamenepo ndidzakhala nchoŵayankha anthu ondinyodola, pakuti ndimakhulupirira mau anu. Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu. Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya, ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu. Ndidzalankhula malamulo anu pamaso pa mafumu, ndipo anthu sadzandichititsa manyazi. Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu amene ndimaŵakonda. Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda, ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo. Kumbukirani mau anu aja kwa ine mtumiki wanu, mau amene amandipatsa chikhulupiriro. Ndikadakonda kuti njira zanga zikhale zokhulupirika, pakumvera malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:6-7

Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:24-25

Kwa munthu palibe chabwino china choposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Ngakhale zimenezi ndazindikira kuti nzochokera kwa Mulungu. Nanga popanda Iye ndani angathe kudya, ndani angathe kusangalala?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:16-20

Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu. Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:10

Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:145-146

Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:26-29

Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu. Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:12

Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:9

Pompo anthu onse adzachita mantha, adzasimba zimene Mulungu wachita, adzalingalira zomwe Mulungu wachitazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:5-6

Inu osadziŵa kanthunu, phunzirani nzeru, inu opusanu, khalani tcheru. Mverani, ndikuuzani zazikulu kwambiri, pakamwa panga palankhula zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12-13

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:1-3

Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera. koma changwiro chikadzaoneka, chopereŵeracho chidzatha. Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo. Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu. Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi. Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse. Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:15

Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:66

Patseni luntha ndi nzeru, chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4-5

Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu. Mwana womakolola nthaŵi yachilimwe ndiye wanzeru, koma womangogona nthaŵi yokolola amachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:7

Onsewo amadziŵika ndi dzina langa, ndidaŵalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndidaŵapanga ndi kuŵapatsa moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu wanga, Woyera ndi Woopsa ndinu, palibe chofanana ndi Uyerero wanu, pamaso panu ndimabwera m'dzina la Yesu kukuthokozani chifukwa cha zonse zomwe mudalenga ndi zomwe mwandipatsa ine mwana wanu. Zikomo Ambuye wanga chifukwa cha maluso omwe ndili nawo ndikudziwa kuti ochokera kwa inu ndipo inu ndinu mwini wake, zikomo chifukwa cha chikondi chomwe mumayika mumtima mwanga kuti ndikutumikireni ndikulemekeza dzina lanu kudzera mu zomwe mwandipatsa. Atate modzichepetsa ndikuulula kuti sindimadziona ngati wokhoza, kapena wokonzeka kugwiritsa ntchito maluso awa, koma ndimakhulupirira zomwe mawu anu amanena: "Ndikhulupirira kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzaitsogolera mpaka tsiku la Yesu Khristu." Zikomo chifukwa cha nthawi zomwe mwandigwiritsa ntchito ngati chida chothandizira ena ndikudalitsa miyoyo yambiri ndi chida ichi chomwe mwandipatsa. Nditsogolereni Mzimu Woyera kuti ndizindikire kuti zonse zomwe Mulungu waika m'manja mwanga ndi kuti ulemerero, ulemu ndi chiyamiko zikhale za Iye yekha, sungani mtima wanga ku kudzikuza, ndilanditseni ku kunyada ndikundithandiza kuwachulukitsa pakuti kwalembedwa: "Usanyoze mphatso imene uli nayo, imene inapatsidwa kwa iwe mwa ulosi ndi kuika manja a akulu." Yeretsani Atate wokondedwa mtima wanga kuti ndikukondweretseni monga momwe Davide anakukondweretsani pamene ankaimba masalmo kwa inu. Ndipatseni nzeru kuti ndizigwiritse ntchito ndikuziyang'anira monga momwe mukufunira, mogwirizana ndi chifuniro chanu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa