Ndisanabadwe, Mulungu anali kale kuganiza za ine. Ndili m'mimba mwa amayi anga, Iye anali kupanga thupi langa ndi kundiona ndi chikondi chachikulu. Kuyambira pachiyambi, maganizo Ake anali abwino, akuona mwa ine mphamvu yokwaniritsa chilichonse chimene anakonza.
Sanalakwitse pondipatsa moyo ndi kundilola kufika pano chifukwa cholinga Chake ndi chachikulu. Wandipulutsa ku imfa, ku ngozi zoopsa, ku nkhanza, ku matenda ndi ku zizolowezi zoipa. Wandiitana ku kuunika Kwake kodabwitsa.
Gawo lililonse la moyo wanga ndi malo aliwonse ndikuwonetsa cholinga chimene anandipatsa. Palibe chimene chingandiletse kukwaniritsa cholinga changa koma ine ndekha. Zonse zimene zimandigwera, ngakhale zitavuta bwanji, zimagwirira ntchito zabwino. Zonse zimene ndakhala nazo zikukonzekera njira yamtsogolo mwanga.
Pukuta misozi yako, osadziimba mlandu, yang'ana kutsogolo. Pali anthu ambiri amene akukufuna. Kumbukira kuti zonse zimene zinachitika mpaka pano si chifukwa chakuti Mulungu ndi woipa, koma zidzakuthandiza kuchira msanga.
Tsiku lililonse, ukadzuka, dzuka ndi chikhulupiriro kuti uli ndi cholinga chachikulu chokwaniritsa padziko lapansi. Kuyitanidwa kwako kukufunika kupangidwa ndi kukonzedwa mpaka kufika pa msinkhu wa Khristu. Khalani olimba mtima ndi kutumikira Mulungu amene anakusunga moyo wako n’disanabadwe.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Mulungu adachita zimenezi kuti zichitikedi zimene Iye adakonzeratu mwa Khristu Yesu Ambuye athu chikhalire, nthaŵi isanayambe.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha.
Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana. Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Onsewo amadziŵika ndi dzina langa, ndidaŵalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndidaŵapanga ndi kuŵapatsa moyo.”
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho.
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, mphamvu zakezo nkuzibwezeranso nchiyani? Ulibenso ntchito mpang'ono pomwe, koma kungoutaya kunja basi, anthu nkumauponda. “Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina. Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani. Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu. Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe.
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite. Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala. Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera. Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse. Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Koma ndimadalira Inu Chauta, ndimati, “Inu ndinu Mulungu wanga.” Masiku anga ali m'manja mwanu. Pulumutseni kwa adani anga ndi kwa ondizunza.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Munthu woyesa kusunga moyo wake, adzautaya, ndipo wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzausunga.
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.
Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.