Palibe zaka zokhazikika zoti munthu akwatire kapena kukwatiwa, ngakhale anthu ambiri amatiuza kuti tikwatire kapena kukwatiwa pa zaka zina. Koma taganizirani izi: n’kwabwino kukwatira kapena kukwatiwa potsatira malangizo a Mulungu osati chifukwa chokakamizidwa ndi anthu.
Mzimu Woyera akakutsogolerani, mudzakhala ndi moyo wopambana ndipo mudzakhala otsimikiza kuti chifuniro cha Mulungu pa moyo wanu chidzakuthandizani pa chilichonse. Musamachite manyazi kuti simunaloŵe m’banja. Uwu ndi nthawi yabwino yoti mudzidziŵe bwino, muyandikire Mulungu, kenako mudzagaŵane moyo wanu ndi wina.
Osathamangira. Khalani ndi moyo wotsatira dongosolo la Mulungu, ndipo mverani mawu ake nthawi zonse kuti musakumane ndi mavuto. Gwiritsani ntchito nthawi imeneyi yomwe muli nokha kuti mukule mwauzimu, mudzikonde, mutumikire Mulungu, ndipo mudzaona mmene adzakudalitsireni ndi munthu woyenera kuti mukwaniritse maloto ake padziko lapansi.
Kwa amene sali pa banja, ndiponso kwa azimai amasiye, mau anga ndi aŵa: Nkwabwino kuti iwo akhalebe paokha choncho ngati ineyo.
Tsopano ndiyankhe zimene mudandifunsa m'kalata yanu. Nkwabwino kuti munthu asakwatire,
Kodi ndiwe wapabanja? Usayese kuthetsa banja lako. Kodi ndiwe wopanda banja? Usayese kupeza banja.
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye.
Kwenikweni ndikadakonda kuti anthu onse akhale ngati ine, koma Mulungu adapatsa munthu aliyense mphatso yakeyake, wina mphatso yakuti, winanso yakuti.
Koma ngati sangathe kudziletsa, aloŵe m'banja, pakuti nkwabwino kuloŵa m'banja kupambana kupsa ndi moto wa zilakolako.
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake. Motero amagwira njakata. Mkazi wosakwatiwa, kapenanso namwali, amangotekeseka ndi za Ambuye, kuti adzipereke kwa Ambuye m'thupi ndi mumzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mwamuna wake.
Pambuyo pake Chauta adati, “Sibwino kuti munthuyu akhale yekha. Ndipanga mnzake woti azimthandiza.”
koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.
Kaya simudziŵa kuti munthu amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja Malembo akuti, “Aŵiriwo adzasanduka thupi limodzi.”
Paja pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa adabadwa motero. Pali ena amene sangathe kukwatira, chifukwa anthu adaŵafula. Pali enanso amene adachita kusankha okha kusakwatira, kuti azitumikira bwino Mulungu. Yemwe angathe kumvetsa, amvetse.”
Ndi ameneŵa amene ankadzisunga angwiro osadziipitsa ndi akazi. Ndi ameneŵa amene amatsata Mwanawankhosa uja kulikonse kumene akupita. Ndiwo amene adaomboledwa pakati pa anthu ena onse, kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa uja.
Ndidakakonda kuti pasakhale zokudetsani nkhaŵa. Munthu wosakwatira amangotekeseka ndi za Ambuye, kuganiza za m'mene angakondweretsere Ambuye. Koma munthu wokwatira amatekeseka ndi zapansipano, kuganiza za m'mene angakondweretsere mkazi wake.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Sindikunena zimenezi modandaula kuti ndikusoŵa kanthu, pakuti ine ndaphunzira kukhutira ndi zimene ndili nazo. Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.
Mai amene ali wamasiye kwenikweni, wopanda wina aliyense womsamala, ameneyo waika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimthandiza.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu: Ndaziwona ntchito zimene Mulungu adapatsa anthu kuti azizigwira. Adapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthaŵi yake. M'mitima mwa anthu Mulungu adaikanso nzeru zotanthauzira zochitika za pa mibadwo ndi mibadwo. Komabe anthuwo sangathe kuzitulukira ntchito zonse za Mulungu kuyambira pa chiyambi mpaka pomalizira. Ndikudziŵa kuti kwa anthu palibe chabwino china choposa kukhala osangalala ndi kumadzikondweretsa nthaŵi yonse ya moyo wao. Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa. Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera. Zimene zilipo tsopano zidaaliponso kale. Zimene zidzakhalepo kutsogolo, zidaaliponso kale. Mulungu amabwezanso zakale zimene zidapita kuti zichitikenso. China chimene ndidachiwona pansi pano ndi ichi: Koyenera kukhala chiweruzo chabwino, komwekonso kumapezeka kuipa mtima. Koyenera kukhala chilungamo, komwekonso kumapezeka zoipa. Ndiye ine ndidayamba kulingalira kuti, “Mulungu adzaŵaweruza onse, abwino ndi oipa omwe, pakuti adaika nthaŵi yochitikira chinthu chilichonse ndiponso ntchito iliyonse.” Kunena za anthu, ndinkalingaliranso kuti, “Mulungu amaŵayesa ndi cholinga choti aŵaonetse kuti iwowo sasiyana konse ndi nyama. Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko. Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka? Choncho ndidaona kuti palibe chinthu chabwino kuposa kuti munthu azikondwerera ntchito yake, pakuti chake chenicheni nchimenechi. Ndani angathe kudziŵa chimene chidzamchitikire iye atafa?” Pali nthaŵi yakupha ndi nthaŵi yochiritsa, nthaŵi yogwetsa ndi nthaŵi yomanga. Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina. Pali nthaŵi yokhala malo amodzi ndi nthaŵi yotalikirana, nthaŵi yokumbatirana ndi nthaŵi yoleka zokumbatiranazo. Pali nthaŵi yofunafuna ndi nthaŵi yotaya, nthaŵi yosunga ndi nthaŵi yomwaza. Pali nthaŵi yong'amba ndi nthaŵi yosoka, nthaŵi yokhala chete ndi nthaŵi yolankhula. Pali nthaŵi yokondana ndi nthaŵi yodana, nthaŵi ya nkhondo ndi nthaŵi ya mtendere.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Chifukwa cha masautso a nthaŵi ino, ndiyesa nkwabwino kuti munthu akhale monga momwe aliri.
Choncho tsopano salinso aŵiri koma thupi limodzi. Tsono zimene Mulungu wazilumukiza pamodzi, munthu asazilekanitse.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Koma anthu ofatsa adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala pa mtendere wosaneneka.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
Nzoonadi, kupembedza Mulungu kumapindulitsa kwambiri, malinga munthu akakhutira ndi zimene ali nazo. Sitidatenge kanthu poloŵa m'dziko lino lapansi, ndipo sitingathenso kutenga kanthu potulukamo.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a Malamulo a Mulungu, chonsecho samvetsa zimene iwo omwe akunena kapena zimene akufuna kutsimikiza.
Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye. Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.