Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

103 Mau a Mulungu Okhudza Maganizo

Ndikukuuzani, mu Mateyu 12:30 tikuphunzira kuti tiyenera kukonda Ambuye ndi mtima wathu wonse, chifukwa m'maganizo mwathu ndi momwe chikondi ndi chidani zimachokera. M'maganizo mwathu tingalenge, tingalote, tingadalitse kapena tingatemberere, tingasunge zinthu zomwe zimatipweteka kapena tingazitaye zomwe sizitiyendera. Ndife ife amene timasankha zomwe tisunge m'maganizo mwathu, kaya zabwino kapena zoipa.

Koma Mulungu sakufuna kuti tizitsatira maganizo athu okha, koma akufuna kutiyendetsera ndi kutiphunzitsa zomwe zili zabwino kwa miyoyo yathu. Tiyenera kumukonda ndi maganizo athu onse, moona mtima, opanda chinyengo, kulola chikondi chake kulamulira malingaliro ndi mtima wathu. Ndikutero tikhoza kukhala moyo womukondweretsa.


Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 22:37

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:5

ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 2:16

Ndi monga Malembo anenera kuti, “Ndani adadziŵa maganizo a Ambuye, kuti athe kuŵalangiza?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 3:5

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:1-2

Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.

ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.

Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”

ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.

Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.

Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.

Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.

Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.

Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 7:25

Tiyamike Mulungu! Adzandipulumutsa ndiye kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu. Motero ineyo, ndi mtima wanga ndimatumikira Malamulo a Mulungu, chonsecho ndi khalidwe langa lokonda zoipa, ndimatumikira lamulo la uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 23:7

Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu. Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!” Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 1:13

Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 94:19

Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:8

pakuti iyeyo ndi wa mitima iŵiri, ndi wosakhazikika pa zochita zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:6

Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 4:23

Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:5

Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu:

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:17-18

Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.

Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:14

Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:16

Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 4:12

Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:8-9

Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi.

Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 77:6

Ndimasinkhasinkha mumtima mwanga usiku. Ndimadzifunsa ndi kufufuzafufuza mumtima mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 1:28

Tsono popeza kuti iwo sadalabadireko za kumvera Mulungu, Mulunguyo adaŵasiya m'maganizo ao opusa, kotero kuti amachita zosayenera.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:21

Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:8

Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 6:10-11

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 5:21

koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 18:15

Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 12:2

Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 26:2

Mundiyang'anitsitse, Inu Chauta, ndi kundiyesa. Muwone mtima wanga pamodzi ndi maganizo anga.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 10:10

Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.

Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:19

Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:10

ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:59

Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:21

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:3

Ngati munthu adziyesa kanthu, pamene chikhalirecho sali kanthu konse, amangodzinyenga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Petro 5:8

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:5-6

Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna.

Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:148

Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 15:33

Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.”

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 14:12

Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kopherezera kwake nku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 26:12

Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 4:16

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo
Aefeso 5:18

Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:73

Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 2:8

Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 55:22

Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 8:7

Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 2:15-16

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.

Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 16:9

Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:25

Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 3:18

Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:11

Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Timoteyo 2:22

Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 62:1-2

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,

chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 48:18

Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 19:7

Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:5

Ena amaganiza kuti tsiku lakutilakuti ndi loposa masiku ena, koma pamene ena akuganiza kuti masiku onse nchimodzimodzi. Aliyense achite monga momwe watsimikizira kwenikweni mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 7:24-25

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.

Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 6:7-8

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 1:21-22

Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa.

Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Atesalonika 4:5

Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 130:5

Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 3:13-14

Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo.

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 4:7-8

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Uziilemekeza nzeruyo, ndipo idzakukweza. Uifungate ndipo idzakupatsa ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Akorinto 10:3-4

Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe.

Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 12:10

Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 28:18

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:80

Mtima wanga ukhale wopanda choudzudzulira pa malamulo anu, kuti ndisachite manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 32:17

Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 2:6

Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 25:4-5

Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu.

Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 8:10

“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Yohane 3:20

nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo
Akolose 3:12

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Agalatiya 5:22

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 86:15

Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 2:14

Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo,

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 2:29

Myuda weniwenitu ndi amene ali Myuda mumtima mwake, ndipo kuumbala kwenikweni ndi kwa mtima, kochitika ndi Mzimu Woyera, osati ndi Malamulo olembedwa ai. Woyamikira munthu wotere ndi Mulungu, osati anthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 2:12

Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 16:26

Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 139:14

Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga Wamuyaya, Wamkulu komanso Wamphamvu, Inu nokha ndinu Woyenera ulemerero ndi ulemu wonse! M'dzina la Yesu, ndikukupemphani kuti ndikuthokozani ndi mtima wanga wonse chifukwa cha chikondi ndi mphamvu zanu, ndikukuthokozani chifukwa cha madalitso onse omwe mwandipatsa, kuyambira pa moyo mpaka kwa okondedwa anga. Atate, ndikudziwa kuti kuti ndisinthe machitidwe anga ndiyenera kusintha maganizo anga, choncho ndikupemphani kuti nthawi ino mulandire maganizo anga ku zisonkhezero zonse zomwe zimandivetsa, kundisokoneza ndikubera mtendere mtima mwanga, zomwe zimakhudzanso banja langa. Mzimu Woyera mundimasule ku mantha, ku chidani, ku kuvutika maganizo ndi kudzipha. Mulungu wanga, yeretsani ndi mawu anu neuron iliyonse mu ubongo wanga, khudzani maganizo anga ndi kukhalapo kwanu, kuti pasakhale malo m'maganizo mwanga a mdani ndi mawu ake oipa. Ndikutsutsa kudzimvera chisoni, kukana, zilakolako zopanda pake, uhule, zolaula ndi kugonana kosalamulirika. Ndikulengeza kuti ndine mfulu ndi cholengedwa chatsopano mwa Khristu Yesu, chifukwa mawu anu amati: "Tikugwetsa mfundo ndi chinthu chilichonse chokwezeka chimene chimatsutsana ndi kudziwa Mulungu, ndipo tikugonjetsa maganizo onse ku kumvera Khristu." Ndikukana m'dzina la Yesu ntchito zonse za mdima m'maganizo mwanga, ndikudula mgwirizano uliwonse wa maganizo anga ndi kuthyola unyolo uliwonse wa ukapolo, chifukwa Mulungu ananditulutsa mu mdima ndi machimo kulowa mu kuunika kwake kodabwitsa. M'dzina la Yesu, Ameni.