Munthu wamkulu koposa onse amene anakhalapo padziko lino lapansi anakumana ndi chinyengo chachikulu. Iye amene anali ndi mtima woyera ndi wowona mtima, wopanda choipa chilichonse, anationetsa chikondi chake ngakhale ambiri anam’tembenukira. Yesu wa ku Nazarete anachitiridwa chinyengo ndi ambiri, kuphatikizapo ineyo ndi iweyo.
Komabe, chitsanzo chake chimatiphunzitsa kuti kukhululukira ndiye mankhwala a ululu wobwera chifukwa cha chinyengo. Kumasula moyo wako ku mkwiyo ndikutsata mapazi abwino a Yesu kudzakubweretsera mphotho ya Atate.
Bisala m’chikondi cha Yesu ndi nsembe yake pa mtanda, ndipo posachedwapa udzachira ndikumwetulira chifukwa cha m’bandakucha wako watsopano. Lolani Mulungu agwire ntchito mwa inu.
Koma Yesu adamufunsa kuti, “Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?”
“Mbale azidzapereka mbale wake kuti aphedwe, bambo azidzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo ao, mpaka kuŵaphetsa.
Koma zonsezi zachitika kuti ziwonekedi zimene aneneri adalemba.” Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumusiya yekha.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
Akadakhala mdani wanga wondinyozayo, ndikadatha kupirira. Akadakhala mdani wanga wondichita chipongweyo, ndikadangobisala basi.
Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye, bwenzi langa wozoloŵerana naye, ndi amene ukuchita zimenezi.
Tinkakambirana nkhani zokoma tili aŵiri, tinkapembedza limodzi m'Nyumba ya Mulungu.
Amene amanka nachita ugogodi, amaulula zinsinsi. Nchifukwa chake usamagwirizane naye wolankhula zopusayo.
Ngakhalenso bwenzi langa lapamtima amene ndinkamkhulupirira, amene ankadya nane pamodzi, wandiwukira.
Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe.
Adakaŵafunsa kuti, “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikadzampereka Yesuyu kwa inu?” Iwo adamupatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
Tsono kuyambira pomwepo iye adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
Ngakhale abale ako ndi anansi ako nawonso amakuchita chiwembu, onsewo amvana pa zokuimba mlandu, usaŵakhulupirire, ngakhale alankhule nawe mau okoma.
Kukhulupirira munthu wosakhulupirika pa nthaŵi yamavuto kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa, kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka.
Ungovomera kulakwa kwako. Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako, kuti udapembedza nao milungu yachilendo patsinde pa mitengo yogudira, ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ” akuterotu Chauta.
Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja.
Amenewo akamchita chipongwe, akamthira malovu, akamkwapula nkumupha. Koma patapita masiku atatu, Iye adzauka.”
Paja Dema adandisiya chifukwa chokonda zapansipano, adapita ku Tesalonika. Kresike adapita ku Galatiya, ndipo Tito adapita ku Dalamatiya.
Anthu anga achita machimo aŵiri: andisiya Ine kasupe wa madzi opatsa moyo, adzikumbira okha zitsime, zitsime zake zong'aluka, zosatha kusunga madzi.
“Rubeni mwana wanga wachisamba, ndiwe nkhongono zanga, ndiwe mphatso yoyamba ya mphamvu zanga. Mwa ana anga onse, wopambana ndiwe pa ulemerero ndi mphamvu.
Lili kuvuma kwa Mamure m'dziko la Kanani. Abrahamu adaagula phangalo pamodzi ndi munda womwe kwa Efuroni Muhiti, kuti pakhale manda.
Kumeneko ndiko kumene adaika Abrahamu pamodzi ndi Sara mkazi wake. Isaki pamodzi ndi mkazi wake Rebeka, adaŵaikanso komweko, ndipo Leya ndidamuika komwekonso.
Mundawo pamodzi ndi phangalo adagula kwa Ahiti.”
Tsono Yakobe atamaliza kulangiza ana ake, adabwezeranso mapazi ake m'bedi ndipo adamwalira.
Uli ngati chigumula cha madzi oopsa, koma sudzakhalanso wopambana, chifukwa chakuti sudaope kugona pa bedi la ine bambo wako. Udaloŵa m'bedi langa, nuliipitsa!
Tsono Abisalomu adalamula antchito ake kuti, “Muwonetsetse nthaŵi imene Aminoni akhale ataledzera ndi vinyo. Ndikakuuzani kuti, ‘Kanthani Aminoni!’ Pomwepo mumuphe. Musaope, nanga sindine ndakulamulani? Mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna.”
Choncho atumiki a Abisalomu adamchita Aminoni monga momwe adaaŵalamulira Abisalomu. Zitatero, ana onse aamuna a mfumu adadzambatuka, aliyense adakwera pa bulu wake, nathaŵa.
Mnzanga adatambasula dzanja lake kuti amenye abwenzi ake, adaphwanya chipangano chake.
Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola.
Simoni, wa m'chipani chandale cha Azelote; ndiponso Yudasi Iskariote, amene pambuyo pake adapereka Yesu kwa adani ake.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Motero amandibwezera zoipa m'malo mwa zabwino, amandiwonetsa chidani m'malo mwa chikondi changa.
Sankhulani munthu woipa kuti aweruze mlandu wa wondiwukirayo, iye aimbidwe mlandu ndi munthu woneneza anzake.
Pomuweruza apezeke kuti ali ndi mlandu, mapemphero ake akhale ngati kupalamula.
Masiku ake akhale oŵerengeka, wina alandire udindo wake.
Tsoka kwa iwe woonongawe, iwe amene sadakuwononge. Tsoka iwe wonyengawe, amene wina aliyense sadakunyenge. Iwe ukadzaleka kuwononga, adzakuwononga, ukadzaleka kunyenga, adzakunyenga.
Adani anga onse amandinyodola, anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa. Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa. Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta.
Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga,
mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi.
Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,
m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe.
Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa.
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino,
opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu.
Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Thandizeni, Inu Chauta, palibenso munthu wosamala za Inu, okhulupirika sapezekanso pakati pa anthu.
Aliyense amangonamiza mnzake, amathyasika ndi pakamwa pake, amalankhula ndi mitima iŵiri.
Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.
Dzambatukani, Inu Chauta, mukumane nawo ndi kuŵagonjetsa. Mundipulumutse ndi lupanga lanu kwa anthu oipawo.
Inu Chauta, ndi dzanja lanu mundilanditse kwa adani, kwa anthu amene moyo wao umangosamala zapansipano. Muŵalange ndi zoŵaŵa zimene mudaŵasungira. Nawonso ana awo akhale nazo zambiri, ndipo iwowo asiyireko ana aonso.
“Aliyense achenjere ndi mnzake, asakhulupirire ngakhale mbale wake. Zoona, aliyense amafuna kulanda malo a mbale wake. Aliyense amachitira mnzake ugogodi.
“Koma anthuwo adaphwanya chipangano changa monga adachitira Adamu. Potero, adandichitira zosakhulupirika.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’
Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.”
Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu.
Bambo adzakangana ndi mwana wake wamwamuna, mwana wamwamuna adzakangana ndi bambo wake. Mai adzakangana ndi mwana wake wamkazi, mwana wamkazi adzakangana ndi mai wake. Apongozi adzakangana ndi mkazi wa mwana wao, ndipo mkaziyo adzakangana ndi apongozi akewo.”
Koma pamene Petro adafika ku Antiokeya, ndidamtsutsa poyera, chifukwa adaapezeka wolakwadi.
Pakuti asanafike anthu ena amene Yakobe adaaŵatuma, iye ankadya pamodzi ndi abale osakhala Ayuda. Koma atafika iwowo, iye adayamba kudzipatula, osafuna kudya nawonso, chifukwa choopa anthu amene ankafuna kuti omwe sali Ayuda aumbalidwe.
Abale ena onse ochokera ku Chiyuda nawonso adayamba kuchita chiphamaso, kotero kuti ngakhale Barnabasi yemwe adaatengeka nacho chiphamaso chaocho.
Ndipo ndimati, “Ndikadakhala ndi mapiko onga a njiŵa, bwenzi nditauluka kupita kutali kukapuma.
Inde, ndikadathaŵira kutali ndi kukakhala ku chipululu.
“Ndikadafulumira kupeza pobisalira mphepo yaukali yamkunthoyi.”
Paja mwa anthu anga muli ena achifwamba, amene amalalira anzao monga m'mene amachitira otchera mbalame. Amatcha misampha nakola anthu.
Nyumba zao nzodzaza ndi chuma chochipeza mwachinyengo, ngati chitatanga chodzaza ndi mbalame. Nchifukwa chake adasanduka otchuka ndi olemera.
Adanenepa nkukhala a matupi osalala. Ntchito zao zoipa nzopanda malire, saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye, kuti iyende bwino, ndipo sateteza amphaŵi.
Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse.
Sindikhala pamodzi ndi anthu onyenga, sindiyenda ndi anthu achiphamaso.
Ndimadana ndi anthu ochita zoipa, sindikhala pamodzi ndi anthu oipa.
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.
Taonanitu! Mzinda umene kale udaali wokhulupirika ndi wachilungamo, tsopano ukuchita zadama. Mzinda umene kale udaali ndi anthu aungwiro, tsopano wadzaza ndi anthu opha anzao.
Ntchentche zakufa zimaika fungo loipa m'mafuta onunkhira bwino. Choncho kupusa kwapang'ono kumatha kuwononga nzeru ndi ulemu.
Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao, koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika kwenikweni?
Anthu anga amadzasonkhana kwa iwe nakhala pansi kuti amve zimene iweyo unene. Koma akazimva, sazitsata zimenezo. Zokamba zao zimaonetsa chikondi, m'menemo mitima yao imangokonda phindu chabe.
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Kuweruza kolungama kwalekeka, ndipo kuchita zaungwiro kwaiŵalika. Zoona sizikupezekanso m'mabwalo a milandu, ndipo chilungamo sichikutha kupezeka kumeneko.
Zoona zikusoŵa kumeneko, ndipo wina aliyense akapanda kuchita nawo zoipa, amapeza mavuto.” Chauta adaziwona zimenezi ndipo zidamunyansa kuti palibe chilungamo.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
“Pakuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe, ali ndi khwinthi la phindu lopeza mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe ao, onsewo ndi onyenga.
Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha. Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’ chonsecho kulibe konse mtendere.
Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana.
Kudzaoneka aneneri onama ambiri, amene azidzasokeza anthu ambiri.
Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.
Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
Cholinga chao nchongofuna kumtsitsa pa malo ake aulemu. Amakonda kulankhula zonama. Amadalitsa ndi pakamwa pao, koma mumtima mwao amatemberera.
Yesu akulankhula choncho, padabwera khamu la anthu. Amene ankaŵatsogolera anali Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Iyeyu adadza pafupi ndi Yesu kuti amumpsompsone.
Koma Yesu adamufunsa kuti, “Yudasi, mongadi ukupereka Mwana wa Munthu kwa adani pakumumpsompsona?”
amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.
Pansi pano chinthu chilichonse chili ndi nyengo yake ndi nthaŵi yake yomwe adaika Mulungu:
Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidaŵabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
Munthu wachidani pakamwa pake pamalankhula zabwino, pamene mumtima mwake muli zonyenga.
Woteroyo akamalankhula mokometsa mau, usamkhulupirire, pakuti mumtima mwake mwadzaza zoipa.
Ngakhale amabisa chidani mochenjera, kuipa kwakeko kudzaoneka poyera pakati pa anthu.
Munthu wosinjirira mnzake kuseri ndidzamcheteketsa. Wooneka wonyada ndi wodzikuza sindidzamulekerera.
Yudasi, amene pambuyo pake adapereka Yesu, adafunsa kuti, “Monga nkukhala ine, Aphunzitsi?” Yesu adamuyankha kuti, “Wanena wekha.”
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.
Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele?
Sindikondwera nayo imfa ya munthu wina aliyense. Nchifukwa chake lapani, kuti mukhale ndi moyo. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera.
Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika.
Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira munthu.
Kuthaŵira kwa Chauta nkwabwino kupambana kukhulupirira mafumu.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.
ngakhale kuti anthu ena adaafuna kuti iyeyu aumbalidwe ndithu. Anthu ameneŵa adaabwera modzizimbayitsa ngati abale athu. Iwowo adangodzaloŵa ngati azondi kuti adzaone ufulu wathu umene tili nawo mwa Khristu Yesu. Ankafuna kutisandutsa akapolo.
Koma adani anga ondifunira zoipa, amati, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti, kuti aiŵalike?”
Amene amabwera kudzandiwona, ndi wosakhulupirika, mumtima mwake amaganiza zoipa za ine, ndipo akatuluka, amakaziwanditsa.
“Ndikukuuzani inu, abwenzi anga, kuti musamaopa anthu. Iwo angathe kupha thupi lokha, koma pambuyo pake alibenso china choti angachitepo.
Choncho inunso khalani okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene simukuyembekeza.”
Pamenepo Petro adati, “Ambuye, kodi fanizoli mukuphera ife tokha, kapena mukuuza onse?”
Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?
Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse.
“Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, amuna ndi akazi, ndiponso kumadya, kumamwa ndi kuledzera.
Tsono mbuye wake adzangoti mbwe mwadzidzidzi, pa tsiku limene iye sakumuyembekeza. Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu osakhulupirika.
“Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri.
Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”
“Ndidabwera kudzaponya moto pa dziko lapansi, ndipo ndikadakonda utayaka kale.
Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa.
Chuma chomachipeza monyenga chimangoti wuzi ngati nthunzi, ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza, pamene ndidaona anthu oipa akulemera.
Iwowo samva kupweteka konse. Matupi ao ndi onenepa ndi athanzi.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Nchifukwa chake timagwira ntchito kolimba, ndipo timayesetsa kupambana, pakuti chiyembekezo chathu chili pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka okhulupirira Khristu.
Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa.
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.
Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.
Zophunzitsa zimenezi nzochokera ku chinyengo cha anthu onama, amene mumtima mwao adalembedwa chizindikiro ndi chitsulo chamoto.
Ndithudi, pa dziko lapansi palibe munthu amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa konse.
Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.
Amagwirizana kuti aononge anthu osalakwa, nagamula kuti opanda mlandu aphedwe.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Adzaŵalanga chifukwa cha machimo ao, adzaŵaononga chifukwa cha kuipa kwao, zoonadi, Chauta, Mulungu wathu, ndiye amene adzaŵafafanize.
Mpang'ono pomwe. Koma anthu adziŵe kuti zimene Mulungu amalankhula nzoonadi, ngakhale kuti anthu onse ndi onama. Ndi monga Malembo akunenera kuti, “Inu Mulungu, anthu adziŵe kuti mumanena zoona mukamalankhula, adziŵe kuti mumapambana mukamazenga mlandu.”
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko,
dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
Adzaŵabwezera adani anga zoipa. Aonongeni, Inu Ambuye, chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa:
maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa,
mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa,
mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.