Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

49 Mau a Mulungu Okhudza Chakudya

Chakudya ndi nkhani yofunika kwambiri imene imapezeka kangapo m’Baibulo. Uku mu Genesis, mukupezeka nkhani ya zipatso ndi zomera monga chakudya cha munthu.

Mu Chipangano Chakale, mulinso malamulo okhudza zakudya, omwe amatiuza zamitundu ya nyama zomwe tingadye. Ndipo mu Chipangano Chatsopano, pali nkhani zambiri zomwe Yesu anadya limodzi ndi otsatira ake, kusonyeza kufunika kwa ubale wathu ndi Mulungu ndi anzathu pamene tidya limodzi.

Komanso, Baibulo limatiphunzitsa kuti thupi lathu ndi kachisi wa Mzimu Woyera, choncho tiyenera kulisamalira bwino. Ndipo kusamalira thupi lathu kumaphatikizapo kudya bwino.

Zonsezi zimatiphunzitsa kuti chakudya si chongotipatsa mphamvu zokha, koma ndi njira yoti tilimbikitse ubale wathu ndi Mulungu komanso ndi anzathu. Monga mwambi umati, “M’mimba mulibe m’bale”. Koma ife, monga Akhristu, tiyenera kuona chakudya ngati njira yoti tigwirizanitse anthu, monga momwe Yesu anachitira.


Luka 12:22-23

Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.

Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 107:9

Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka, nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 136:25

Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:3

Wakudyayo asapeputse wosadyayo; ndipo wosadyayo asaweruze wakudyayo; pakuti Mulungu wamlandira.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 27:7

Mtima wokhuta upondereza chisa cha uchi; koma wakumva njala ayesa zowawa zonse zotsekemera.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 16:4

Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndidzavumbitsira inu mkate wodzera kumwamba; ndipo anthu azituluka ndi kuola muyeso wa tsiku pa tsiku lake, kuti ndiwayese, ngati ayenda m'chilamulo changa kapena iai.

Mutu    |  Mabaibulo
Eksodo 16:12-15

Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Ndipo kunali madzulo zinakwera zinziri, ndipo zinakuta tsasa, ndi m'mawa padagwa mame pozungulira tsasa.

Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka.

Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Levitiko 26:4-5

ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.

Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.

Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.

Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.

Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.

Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 8:3

Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 11:14-15

ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.

Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 4:4

Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:22-24

Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.

Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.

Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Mutu    |  Mabaibulo
Deuteronomo 28:12

Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 145:15-16

Maso a onse ayembekeza Inu; ndipo muwapatsa chakudya chao m'nyengo zao.

Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 34:10

Misona ya mkango isowa nimva njala, koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 23:1-2

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 10:13-14

Ndipo anamdzera mau, Tauka, Petro; ipha, mudye.

Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadye ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 37:25

Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 9:3-4

Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:1-2

Inu nonse, inu akumva ludzu, idzani kumadzi; ndi osowa ndalama idzani inu mugule mudye; inde idzani, mugule vinyo ndi mkaka opanda ndalama ndi opanda mtengo wake.

Pakuti monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbeu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya;

momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.

Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.

M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.

Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 78:24-25

Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba.

Yense anadya mkate wa angelo, anawatumizira chakudya chofikira.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 104:14-15

Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;

ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 9:3

Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 111:5

Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 132:15

Ndidzadalitsatu chakudya chake; aumphawi ake ndidzawakhutitsa ndi mkate.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 8:8

Koma chakudya sichitivomerezetsa kwa Mulungu; kapena ngati sitidya sitisowa; kapena ngati tidya tilibe kupindulako.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 1:29

Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Akorinto 6:13

Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 10:3

Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo
Genesis 1:29-30

Ndipo anati Mulungu, Taonani, ndakupatsani inu therere lonse lakubala mbeu lili padziko lapansi, ndi mitengo yonse m'mene muli chipatso cha mtengo wakubala mbeu; chidzakhala chakudya cha inu:

Ndipo anati Mulungu, Kuyere; ndipo kunayera.

ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.

Mutu    |  Mabaibulo
Miyambo 30:8-9

Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera;

ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 55:2

Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:11

Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:36

natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 6:25-26

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?

Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 14:19-20

Ndipo Iye analamulira makamu a anthu akhale pansi paudzu; ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo, ndipo m'mene anayang'ana kumwamba, anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo.

nanena kwa anyamata ake, Uyo ndiye Yohane Mbatizi; anauka kwa akufa; ndipo chifukwa cha ichi zamphamvuzi zilimbalimba mwa iye.

Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 15:35-37

Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse;

natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu.

Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 12:24

Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

Mutu    |  Mabaibulo
Yohane 6:35

Yesu anati kwa iwo, Ine ndine mkate wamoyo; iye amene adza kwa Ine sadzamva njala, ndi iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo
Machitidwe a Atumwi 14:17

Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.

Mutu    |  Mabaibulo
Aroma 14:6

Iye wakusamalira tsiku, alisamalira kwa Ambuye: ndipo iye wakudya, adya mwa Ambuye, pakuti ayamika Mulungu; ndipo iye wosadya, mwa Ambuye sakudya, nayamikanso Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Timoteyo 4:4-5

Pakuti cholengedwa chonse cha Mulungu nchabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi chiyamiko;

pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.

Mutu    |  Mabaibulo
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga Wamuyaya, Ambuye Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, ndi woyenera kutamandidwa konse ndi kupembedzedwa. Atate, zikomo chifukwa chakuti zonse munazipanga bwino kwambiri ndipo munalenga zabwino kwambiri kwa anthu, munatipatsa zipatso za dziko lapansi ndi chakudya choti tidye. Ndikukupemphani kuti mundithandize kusamalira thupi langa chifukwa ndi kachisi ndi nyumba ya Mzimu wanu Woyera. Mundiphunzitse kukhala wanzeru pa kudya, kusamalira thupi langa, kugwiritsa ntchito bwino chakudya, ndi kudya zakudya zabwino. Mundithandize kuti ndisadye dala zakudya zoipa zomwe zingandichititse kudwala. M'dzina la Yesu. Ameni!