Kale, anthu ankapereka nsembe za nyama kwa Mulungu m’Chipangano Chakale. Koma, pali mavesi ambiri omwe amasonyeza kuti Mulungu safuna nsembe zimenezo ndipo amafuna kuti tisamalire zinyama.
Mwachitsanzo, lemba la Miyambo 12:10a limati, “Wolungama asamalira moyo wa nyama yake; Koma mtima wa oipa ndi wankhanza.” Mawu a Mulungu amalankhulapo zoteteza zinyama; ngati titayang’anitsitsa mau a aneneri, tipeza mavesi ambiri amene amatilimbikitsa kusamalira zinyama.
M’buku la Hoseya 8:13b timawerenga kuti, “Nsembe zawo za nyama ndi kudya nyama kwandibweretsera chonyansa, ndipo Ambuye sakondwera nazo, koma adzakumbukira mphulupulu zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
Mulungu ndipo adalenga zinsomba zazikulu ndi zoyendayenda zamoyo zakuchuluka m'madzi mwa mitundu yao, ndi mbalame zamapiko, yonse monga mwa mtundu wake: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
ndiponso ndapatsa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi zokwawa zonse za dziko lapansi m'mene muli moyo, therere laliwisi lonse likhale chakudya: ndipo kunatero.
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi.
Ndipo adati Mulungu, Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng'ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao: ndipo kunatero.
Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.
Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m'chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pang'ombe, ndi padziko lonse lapansi, ndi pazokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi. Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi. Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba za m'nyanja, ndi pambalame za m'mlengalenga, ndi pazamoyo zonse zokwawa padziko lapansi.
Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga, ndi pa zonse zokwawa pansi, ndi pansomba zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu. Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wampesa: namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake. Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja. Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao. Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziwa chimene anamchitira iye mwana wake wamng'ono. Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani; adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo. Ndipo anati, Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake. Mulungu akuze Yafeti, akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake. Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu. Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira. Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
Ndipo Yehova Mulungu anatenga munthuyo, namuika iye m'munda wa Edeni kuti aulime nauyang'anire.
Ukakomana ndi ng'ombe kapena bulu wa mdani wako zilinkusokera, uzimbwezera izo ndithu. Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.
Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;
Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako; pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo. Amatuta udzu, msipu uoneka, atchera masamba a kumapiri. Anaankhosa akuveka, atonde aombolera munda; mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya; ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.
Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.
Ndipo zonse zokhala ndi moyo, ziwiriziwiri za mtundu wao ulowetse m'chingalawamo, kuti zikhale ndi moyo pamodzi ndi iwe; zikhale zamphongo ndi zazikazi.
Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke.
Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zilikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu. Musamalima ndi bulu ndi ng'ombe zikoke pamodzi. Musamavala nsalu yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje. Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho. Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda, namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana naye sindinapeze zizindikiro zakuti ndiye namwali ndithu; pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wake azitenga ndi kutuluka nazo zizindikiro za unamwali wake wa namwaliyo, kunka nazo kwa akulu a mzinda kuchipata; ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akulu, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wake, koma amuda; ndipo, taonani, wamneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kuti, Sindinapeze zizindikiro za unamwali wake m'mwana wako wamkazi; koma si izi zizindikiro za unamwali wa mwana wanga wamkazi. Ndipo azifunyulula chovalacho pamaso pa akulu a mzindawo. Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula; ndi kumlipitsa masekeli makumi okhaokha khumi a siliva, ndi kuipereka kwa atate wa namwaliyo, popeza anamveketsa dzina loipa namwali wa Israele, ndipo azikhala mkazi wake, sangathe kumchotsa masiku ake onse. Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu kunyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo. Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mzinda wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa mu Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu. Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele. Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mzinda mwamuna, nagona naye; muziwatulutsa onse awiri kunka nao ku chipata cha mzinda uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanafuule angakhale anali m'mzinda; ndi mwamuna popeza anachepetsa mkazi wa mnansi wake; chotero muzichotsa choipacho pakati panu. Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye; koma namwaliyo musamamchitira kanthu; namwaliyo alibe tchimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzake namupha; pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anafuula, koma panalibe wompulumutsa. Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anamchepetsa; sangathe kumchotsa masiku ake onse. Mutero nayenso bulu wake; mutero nachonso chovala chake, mutero nachonso chotayika chilichonse cha mbale wanu, chakumtayikira mukachipeza ndi inu; musamazilekerera. Munthu asatenge mkazi wa atate wake, kapena kuvula atate wake. Mukapenya bulu kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.
Pakuti chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera nchimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi chabe. mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; Onse apita kumalo amodzi; onse achokera m'fumbi ndi onse abweranso kufumbi.
Mukachipeza chisa cha mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi make alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga make pamodzi ndi ana; muloletu make amuke, koma mudzitengere ana; kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke.
Ukaona bulu wa munthu wakudana nawe alikugona pansi ndi katundu wake, ndipo ukadaleka kuthandiza, koma uzimthandiza ndithu.
Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao aang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m'funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.
Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.
Pakuti zamoyo zonse zakuthengo ndi zanga, ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri, ndipo nyama zakuthengo zili ndi Ine.
Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu:
Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu bulu wake kapena ng'ombe yake itagwa m'chitsime, ndipo sadzaitulutsa pomwepo tsiku la Sabata kodi?
Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.
Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.
ndipo sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Ninive mzinda waukulu uwu; m'mene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati padzanja lao lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando, m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka; zamoyo zazing'ono ndi zazikulu.
Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga; koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.
Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.
Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;
kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.
Kodi udziwa nyengo yakuswana zinkhoma? Kodi wapenyerera pakuswa mbawala? Kodi ukhoza kumanga njati ndi lamba lake ilime m'mchera? Kapena idzakutsata kodi kufafaniza nthumbira m'zigwa? Udzaikhulupirira kodi, popeza mphamvu yake njaikulu? Udzaisiyira ntchito yako kodi? Kodi udzaitama kuti itute mbeu zako, ndi kuzisonkhanitsira kudwale? Phiko la nthiwatiwa likondwera, koma mapiko ndi nthenga zake nzofatsa kodi? Pakuti isiya mazira ake panthaka, nimafunditsa m'fumbi, nkuiwala kuti phazi lingawaphwanye, kapena chilombo chingawapondereze. Iumira mtima ana ake monga ngati sali ake; idzilemetsa ndi ntchito chabe, popeza ilibe mantha; pakuti Mulungu anaimana nzeru, ndipo sanaigawire luntha. Ikafika nthawi yake, iweramuka, iseka kavalo ndi wa pamsana pake. Wampatsa kavalo mphamvu yake kodi? Wamveka pakhosi pake chenjerere chogwedezeka? Ukhoza kodi kuwerenga miyezi yakuzipitira, kapena udziwa nyengo yoti ziswane? Wamlumphitsa kodi ngati dzombe? Ulemerero wa kumina kwake ngwoopsa. Apalasa kuchigwa, nakondwera nayo mphamvu yake; atuluka kukomana nao eni zida. Aseka mantha osaopsedwa, osabwerera kuthawa lupanga. Phodo likuti kochokocho panthiti pake, mkondo wonyezimira ndi nthungo yomwe. Ndi kunjenjemera kwaukali aimeza nthaka, osaimitsika pomveka lipenga. Pomveka lipenga akuti, Hee! Anunkhiza nkhondo ilikudza kutali, kugunda kwa akazembe ndi kuhahaza. Kodi kabawi auluka mwa nzeru zako, natambasula mapiko ake kunka kumwera? Kodi chiombankhanga chikwera m'mwamba pochilamulira iwe, nkumanga chisanja chake m'mwamba? Kwao nkuthanthwe, chigona komweko, pansonga pa thanthwe pokhazikikapo. Pokhala kumeneko chiyang'ana chakudya; maso ake achipenyetsetsa chili kutali. Zithuntha, ziswa, zitaya zowawa zao. Ana ake akumwa mwazi, ndipo pomwe pali ophedwa, apo pali icho. Ana ao akhala ojincha, akulira kuthengo, achoka osabwerera kwa amao.
Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake; nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo, ndi nyama zakuthengo zomwe; mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja. Zopita m'njira za m'nyanja.