Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, mwina mukudziwa nkhani ya Adamu ndi Eva, momwe anachimwira Mulungu. Chifukwa cha zimenezi, dziko lathu lino linaledzera. Baibulo limatiuza mu Genesis 3:17 kuti Mulungu anauza Adamu kuti, "Popeza wamvera mkazi wako, nudya zipatso za mtengo umene ndinakuletsa, dziko lapansi lidzatembereredwa chifukwa cha iwe; udzadya zipatso zake ndi zowawa masiku onse a moyo wako."
Kumbukirani kuti Mulungu analenga dziko lino labwino kwambiri. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi la chilengedwe, zonse zinali zabwino kwambiri. Koma uchimo unabweretsa temberero ndi matenda. Zinthu ngati zivomerezi zimatipatsa chenjezo. Zimatiwonetsa kuti ufumu wa Khristu ukubwera, ndipo tiyenera kulapa machimo athu ndi mtima wonse.
Ngati sitilapa, tidzatayika miyoyo yathu ndi kukhala pamalo okhetsa mano ndi kulira kwamuyaya. Mulungu akufuna kuti tisinthe miyoyo yathu, tisiye zoyipa ndi machimo, ndi kukhala oyera mtima. Tiyeni timvere mawu a Mulungu ndikukhala moyo woyenera.
ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.
Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.
Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho. Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.
Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.
Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.
Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.
Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.
Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja. Chinkana madzi ake akokoma, nachita thovu, nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwake.
Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;
Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana. Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye. Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.
Dziko lapansi lidzachita dzandidzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati chilindo; ndi kulakwa kwake kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.
Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.
ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele;
Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m'malo ake, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.
Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.
Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.
Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele; Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako kwa Gogi, wa kudziko la Magogi, ndiye mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala; nunenere motsutsana naye, motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama zakuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.
motero kuti nsomba za m'nyanja, ndi mbalame za m'mlengalenga, ndi nyama zakuthengo, ndi zokwawa zonse zakukwawa pansi, ndi anthu onse akukhala padziko, zidzanjenjemera pamaso panga; ndi mapiri adzagwetsedwa, ndi potsetsereka padzagumuka, ndi makoma onse adzagwa pansi.
Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.
Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.
Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.
Ndi mapazi ake adzaponda tsiku lomwelo paphiri la Azitona, lili pandunji pa Yerusalemu kum'mawa, ndi phiri la Azitona lidzang'ambika pakati kuloza kum'mawa ndi kumadzulo, ndipo padzakhala chigwa chachikulu; ndi gawo lina la phirilo lidzamuka kumpoto, ndi gawo lina kumwera.
Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.
Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; ndi manda anatseguka, ndi mitembo yambiri ya anthu oyera mtima, akugona kale, inauka; ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri. Ndipo anali naye akudikira Yesu, anaona chivomezi, ndi zinthu zimene zinachitidwa, anaopa kwambiri, nanena, Indedi Uyu ndiye Mwana wa Mulungu.
Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;
amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.
Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.
amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba. Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.
Ndipo mngeloyo anatenga mbale ya zofukiza, naidzaza ndi moto wopala paguwa la nsembe, nauponya padziko lapansi; ndipo panakhala mabingu, ndi mau, ndi mphezi, ndi chivomezi.
Pamenepo mzimu unandinyamula, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau a mkokomo waukulu, ndi kuti, Wodala ulemerero wa Yehova m'malo mwake.
Pakuti, taonani, Yehova alikutuluka m'malo mwake, nadzatsika, nadzaponda pa misanje ya dziko lapansi.
Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.
Ndipo monga kunakhala masiku a Nowa, momwemo kudzakhalanso masiku a Mwana wa Munthu. Anadya, anamwa, anakwatira, anakwatiwa, kufikira tsiku lija Nowa analowa m'chingalawa, ndipo chinadza chigumula, nkuwaononga onsewo. Monga momwenso kunakhala masiku a Loti; anadya, anamwa, anagula, anagulitsa, anabzala, anamanga nyumba; koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu udavumba moto ndi sulufure zochokera kumwamba, ndipo zinawaononga onsewo; Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire. momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu.
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.
Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.
Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:
Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo. Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika. Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu.