Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 24:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m'malo akutiakuti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mtundu ndi mtundu udzawukirana, ndipo ufumu ndi ufumu udzawukirana. Kudzakhala njala ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 24:7
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anapasulidwa, mtundu wa anthu kupasula unzake, ndi mzinda kupasula mzinda; pakuti Mulungu anawavuta ndi masautso ali onse.


Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.


Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi chivomezi, ndi mkokomo waukulu, kamvulumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.


Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?


Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.


Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti chisokonezo chachikulu chochokera kwa Yehova chidzakhala pakati pao; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukira dzanja la mnzake.


ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.


Ndipo ananyamuka mmodzi wa iwo, dzina lake Agabu, nalosa mwa Mzimu, kuti padzakhala njala yaikulu padziko lonse lokhalamo anthu; ndiyo idadza masiku a Klaudio.


Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m'thambo la kumwamba, ndi zizindikiro padziko lapansi; mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;


Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.


Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;


Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu chikunena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lake.


Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa