Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono Afilisti onse m'dzikomo adasokonezeka ndi mantha aakulu. Ankhondo a ku kaboma kankhondo kaja ndi anzao enanso ankanjenjemera kwambiri. Kudachita chivomezi ndipo kugwedezeka kwa dziko kudakulitsa mantha a Afilisti aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:15
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.


Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo, nadzampirikitsa kumbuyo kwake.


Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Pamenepo padasandulika pa nkhope pake pa mfumu, ndi maganizo ake anamsautsa, ndi mfundo za m'chuuno mwake zinaguluka, ndi maondo ake anaombana.


Koma inu mudzayamba kumva za nkhondo, ndi mbiri za nkhondo; onani, musadere nkhawa; pakuti kuyenera kuti izi zioneke; koma chitsiriziro sichinafike.


nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.


Ndipo anaima yense m'mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m'misasa onse, nafuula, nathawa.


Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala;


gulu lina linalowa njira yonka ku Betehoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku chigwa cha Zeboimu kuchipululuko.


Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anatuluka kunja ku mpata wa ku Mikimasi.


Kuwapha koyambako, Yonatani ndi wonyamula zida zake, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi.


Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.


Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa