Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo ozonda a Saulo ku Gibea wa ku Benjamini anayang'ana; ndipo, onani, khamu la anthu linamwazikana, kulowa kwina ndi kwina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Alonda a Saulo a ku Gibea ku dziko la Benjamini poti ayang'ane, adangoona chigulu cha adani chikumwazikira uku ndi uku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Alonda a Sauli a ku Gibeya dziko la Benjamini atangomwaza maso anangoona chigulu cha asilikali chikumwazikana uku ndi uku.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:16
8 Mawu Ofanana  

Apitetu ngati madzi oyenda; popiringidza mivi yake ikhale yodukaduka.


Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.


Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mzinda kumenyana ndi mzinda, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.


Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Pamenepo Saulo ananena ndi anthu amene anali naye, Awerenge tsopano, kuti tizindikire anatichokera ndani. Ndipo pamene anawerenga, onani Yonatani ndi wonyamula zida zake panalibe.


Ndipo Saulo ndi anthu onse amene anali naye anaunjikana pamodzi, natulukira kunkhondoko; ndipo taonani, munthu yense anakantha mnzake ndi lupanga, ndipo panali kusokonezeka kwakukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa