Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:8 - Buku Lopatulika

8 Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Dziko lapansi linagwedezeka, inde thambo linakha pamaso pa Mulungu; Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 dziko lidagwedezeka, mlengalenga udagwetsa mvula chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu. Phiri la Sinai lidagwedezeka chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu, Mulungu wa Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula, pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai. Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:8
16 Mawu Ofanana  

Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, pamaso pa Mulungu wa Yakobo;


Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israele, kuchokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha. Amen, ndi Amen.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Liu la bingu lanu linatengezanatengezana; mphezi zinaunikira ponse pali anthu; dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.


Koma Mulungu anawazungulitsa anthuwo, ku njira ya kuchipululu ya Nyanja Yofiira; ndipo ana a Israele anakwera kuchokera m'dziko la Ejipito okonzeka.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


ndipo ndidzakupatsa iwe chuma cha mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israele.


Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;


Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.


Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.


amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa