Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 68:9 - Buku Lopatulika

9 Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula, munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Inu, Mulungu, munavumbitsa chimvula, munatsitsimutsa cholowa chanu pamene chidathodwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Inu Mulungu, mudagwetsa mvula yokwanira pa dziko. Mudalimbitsanso dziko, choloŵa cha anthu anu, pamene lidaali lofooka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu; munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 68:9
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Pakuti ndidzaika izi ndi midzi yozungulira chitunda changa, zikhale mdalitso; ndipo ndidzavumbitsa mivumbi m'nyengo yake, padzakhala mivumbi ya madalitso.


ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m'nyengo yake, ya chizimalupsa ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.


Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.


Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Sinai lili pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa