Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 16:26 - Buku Lopatulika

26 ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 16:26
15 Mawu Ofanana  

Namuka iye, napeza mtembo wake wogwera m'njira, ndi bulu ndi mkango zili chiimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula bulu.


kuti amve kubuula kwa wandende; namasule ana a imfa.


ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.


Mulungu amangitsira banja anthu a pa okha; atulutsa am'ndende alemerere; koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.


Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.


kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake.


Ndipo m'mene adapitirira podikira poyamba ndi pachiwiri, anadza kuchitseko chachitsulo chakuyang'ana kumzinda; chimene chidawatsegukira chokha; ndipo anatuluka, napitirira khwalala limodzi; ndipo pomwepo mngelo anamchokera.


Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga. Ndipo maunyolo anagwa kuchoka m'manja mwake.


Ndipo m'mene adapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mau a Mulungu molimbika mtima.


Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa