Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 8:8 - Buku Lopatulika

8 Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chifukwa cha zonsezi dziko lapansi lidzagwedezeka, ndipo onse okhala m'menemo adzamva chisoni! Dziko lonse lapansi lidzagwedezeka ngati Nailo, lidzafufuma ndi kuteranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi, ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni? Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo; lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata ngati mtsinje wa ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 8:8
22 Mawu Ofanana  

Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.


Chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ake, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lake, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Ndani uyu amene auka ngati mtsinje, madzi ake ogavira monga mitsinje?


Ejipito auka ngati mtsinje, madzi ake agavira ngati mitsinje; ndipo ati, Ndidzauka, ndidzamiza dziko lapansi; ndidzaononga mizinda ndi okhalamo ake.


Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babiloni zilipobe, zoti ayese dziko la Babiloni bwinja lopanda wokhalamo.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.


Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; nilidzatsikanso ngati mtsinje wa mu Ejipito;


Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.


ndipo pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha Mwana wa Munthu; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa Munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa