Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 104:32 - Buku Lopatulika

32 amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 amene apenyerera pa dziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Iye amati akayang'ana dziko lapansi, limanjenjemera, akakhudza mapiri, mapiriwo amafuka nthunzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera, amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 104:32
16 Mawu Ofanana  

Unjenjemere, dziko lapansi iwe, pamaso pa Ambuye, pamaso pa Mulungu wa Yakobo;


Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike: Khudzani mapiri ndipo adzafuka.


Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Madziwo anakuonani Mulungu; anakuonani madziwo; anachita mantha, zozama zomwe zinanjenjemera.


Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nkumadzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wake ukwera kunthawi za nthawi.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa