Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 1:1 - Buku Lopatulika

1 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mau a Amosi, amene anali mwa oweta ng'ombe a ku Tekowa, ndiwo amene anawaona za Israele masiku a Uziya mfumu ya Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele, zitatsala zaka ziwiri chisanafike chivomezi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 1:1
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu anatumiza ku Tekowa, natenga kumeneko mkazi wanzeru, nanena naye, Ukokomezeke monga mfedwa, nuvale zovala za pamaliro, osadzola mafuta, koma ukhale ngati munthu wamkazi wakulira akufa nthawi yaikulu.


Tsono anachokako, napeza Elisa mwana wa Safati alikukoketsa chikhasu ng'ombe ziwiriziwiri magoli khumi ndi awiri, iye yekha anakhala pa goli lakhumi ndi chiwiri; ndipo Eliya ananka kunali iyeyo, naponya chofunda chake pa iye.


Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.


Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake mu Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.


Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekowa,


Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala mu Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.


Koma Mose analikuweta gulu la Yetero mpongozi wake, wansembe wa ku Midiyani; natsogolera gululo m'tsogolo mwa chipululu, nafika kuphiri la Mulungu, ku Horebu.


Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.


Mau a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;


Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi mafumu aakulu, za nkhondo, ndi za choipa, ndi za mliri.


Ananu a Benjamini, pulumukani pothawa pakati pa Yerusalemu, ombani lipenga mu Tekowa, kwezani chizindikiro mu Betehakeremu; pakuti chaoneka choipa chotuluka m'mpoto ndi kuononga kwakukulu.


Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakutchera nkhuyu;


Mau a Yehova amene anadza kwa Mika wa ku Moreseti masiku a Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, amene adaona za Samariya ndi Yerusalemu.


Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.


Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba.


koma Mulungu anasankhula zopusa za dziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru; ndipo zofooka za dziko lapansi Mulungu anazisankhula, kuti akachititse manyazi zamphamvu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa