Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 3:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala m'Ziyoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndidzalipsira magazi a ophedwawo, sindidzalekerera tchimo la olakwawo. Ine Chauta ndimakhala ku Ziyoni.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kukhetsa magazi kwawo kumene Ine sindinakhululuke ndidzakhululuka.” Yehova amakhala mu Ziyoni!

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 3:21
8 Mawu Ofanana  

pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.


Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mzindawo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.


Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa