Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoweli 3:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yehova adzabangula kuchokera mu Ziyoni ndipo mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera mu Yerusalemu; dziko lapansi ndi thambo zidzagwedezeka. Koma Yehova adzakhala pothawira pa anthu ake, linga la anthu a ku Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Yoweli 3:16
31 Mawu Ofanana  

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu, Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.


Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine.


Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.


iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.


Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.


Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.


Ndipo ndaika mau anga m'kamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la choipa.


Pakuti ndanena mu nsanje yanga, ndi m'moto wa kuzaza kwanga, Zoonadi tsiku ilo kudzakhala kugwedezeka kwakukulu m'dziko la Israele;


Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kuchokera kumadzulo.


Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.


Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?


Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe;


ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.


Ndipo ndidzawalimbitsa mwa Yehova; ndipo adzayendayenda m'dzina lake; ati Yehova.


Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.


Bwererani kudza kulinga, andende a chiyembekezo inu; ngakhale lero lino ndilalikira kuti ndidzakubwezera chowirikiza.


amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


Ndipo anatsegulidwa Kachisi wa Mulungu amene ali mu Mwamba; ndipo linaoneka likasa la chipangano chake, mu Kachisi mwake, ndipo panali mphezi, ndi mau, ndi mabingu, ndi chivomezi, ndi matalala aakulu.


ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali chivomezi chachikulu chotero sichinaoneke chiyambire anthu padziko, chivomezi cholimba chotero, chachikulu chotero.


Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa