Mateyu 27:51 - Buku Lopatulika51 Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201451 Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa51 Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero51 Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika. Onani mutuwo |