Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mateyu 27:50 - Buku Lopatulika

50 Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau aakulu, anapereka mzimu wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

50 Ndipo Yesu, pamene anafuula ndi mau akulu, anapereka mzimu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

50 Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

50 Ndipo pamene Yesu analiranso mofuwula, anapereka mzimu wake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:50
14 Mawu Ofanana  

Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Koma ena anati, Taleka, tione ngati Eliya adzafika kudzampulumutsa.


Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake.


Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.


Ine ndine Mbusa Wabwino; mbusa wabwino ataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.


monga Atate andidziwa Ine, ndi Ine ndimdziwa Atate; ndipo nditaya moyo wanga chifukwa cha nkhosa.


Kunaikidwako chotengera chodzala ndi vinyo wosasayo pa phesi la hisope, nachifikitsa kukamwa kwake.


Pamene Yesu tsono adalandira vinyo wosasayo anati, Kwatha; ndipo anawerama mutu, napereka mzimu.


Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa