Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 12:26 - Buku Lopatulika

26 amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 amene mau ake anagwedeza dziko pamenepo; koma tsopano adalonjeza, ndi kuti, Kamodzinso ndidzagwedeza, si dziko lokha, komanso m'mwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Pa nthawiyo mawu ake anagwedeza dziko lapansi, koma tsopano Iye walonjeza kuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza osati dziko lapansi lokha komanso thambo.”

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:26
12 Mawu Ofanana  

Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Chifukwa chake ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kuchokera m'malo ake, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wake waukali.


Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.


Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.


Ndipo Yehova adzadzuma ali ku Ziyoni, ndi kumveketsa mau ake ali ku Yerusalemu; ndi thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka; koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu adzakhala chopulumukirako anthu ake, ndi linga la ana a Israele.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi;


ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.


Ndipo ichi, chakuti kamodzinso, chilozera kusuntha kwake kwa zinthu zogwedezeka, monga kwa zinthu zolengedwa, kuti zinthu zosagwedezeka zikhale.


Yehova, muja mudatuluka mu Seiri, muja mudayenda kuchokera ku thengo la Edomu, dziko linanjenjemera, thambo lomwe linakha, inde mitambo inakha madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa