Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:25 - Buku Lopatulika

25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:25
22 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.


Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.


Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse? Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?


Ana ake akhale amchirakuyenda ndi opemphapempha; afunefune zosowa zao kuchokera m'mabwinja mwao.


Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.


Moyo wake udzakhala mokoma; ndi mbumba zake zidzalandira dziko lapansi.


Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.


Ayendeyende ndi kufuna chakudya, nachezere osakhuta.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake, ndipo sadzataya cholowa chake.


Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.


Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.


Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.


olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;


Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.


Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa