Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 10:3 - Buku Lopatulika

3 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 10:3
23 Mawu Ofanana  

Ayendayenda ndi kufuna chakudya, nati, Chilikuti? Adziwa kuti lamkonzekeratu pafupi tsiku lamdima.


Phindu la m'nyumba mwake lidzachoka, akatundu ake adzamthawa tsiku la mkwiyo wake.


Adzakuombola kuimfa m'njala, ndi kumphamvu ya lupanga m'nkhondo.


Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.


Kupulumutsa moyo wao kwa imfa, ndi kuwasunga ndi moyo m'nyengo ya njala.


Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta.


Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenye wolungama atasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.


Khulupirira Yehova, ndipo chita chokoma; khala m'dziko, ndipo tsata choonadi.


Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasowa.


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Wodukidwa mtima aputa makangano; koma wokhulupirira Yehova adzakula.


Wopewetsa khutu lake kuti asamve chilamulo, ngakhale pemphero lake linyansa.


iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa