Masalimo 136 - Buku LopatulikaMulungu alemekezedwe pa chifundo chake 1 Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. 2 Yamikani Mulungu wa milungu; pakuti chifundo chake nchosatha. 3 Yamikani Mbuye wa ambuye; pakuti chifundo chake nchosatha. 4 Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. 5 Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha. 6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pamadzi; pakuti chifundo chake nchosatha. 7 Amene analenga miuni yaikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. 8 Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. 9 Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha. 10 Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. 11 Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha. 12 Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha. 13 Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira; pakuti chifundo chake nchosatha. 14 Napititsa Israele pakati pake; pakuti chifundo chake nchosatha. 15 Nakhuthula Farao ndi khamu lake mu Nyanja Yofiira: pakuti chifundo chake nchosatha. 16 Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu; pakuti chifundo chake nchosatha. 17 Amene anapanda mafumu aakulu; pakuti chifundo chake nchosatha. 18 Ndipo anawapha mafumu omveka; pakuti chifundo chake nchosatha. 19 Sihoni mfumu ya Aamori; pakuti chifundo chake nchosatha. 20 Ndi Ogi mfumu ya Basani; pakuti chifundo chake nchosatha. 21 Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa; pakuti chifundo chake nchosatha. 22 Cholowa cha kwa Israele mtumiki wake; pakuti chifundo chake nchosatha. 23 Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha. 24 Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha. 25 Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha. 26 Yamikani Mulungu wa Kumwamba, pakuti chifundo chake nchosatha. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi